Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   ,    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

3  GEN 1:3  Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.
6  GEN 1:6  Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
7  GEN 1:7  Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
9  GEN 1:9  Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,ndipo zinachitikadi.
10  GEN 1:10  Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
11  GEN 1:11  Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
14  GEN 1:14  Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;
17  GEN 1:17  Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi,
18  GEN 1:18  kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
20  GEN 1:20  Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.”
22  GEN 1:22  Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”
24  GEN 1:24  Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi.
25  GEN 1:25  Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
26  GEN 1:26  Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
27  GEN 1:27  Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.
28  GEN 1:28  Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
29  GEN 1:29  Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.
30  GEN 1:30  Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi.
31  GEN 1:31  Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
32  GEN 2:1  Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo.
34  GEN 2:3  Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira.
35  GEN 2:4  Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,
36  GEN 2:5  zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka,
42  GEN 2:11  Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide.
47  GEN 2:16  Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu;
48  GEN 2:17  koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.”
49  GEN 2:18  Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.”
50  GEN 2:19  Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.
51  GEN 2:20  Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza.
52  GEN 2:21  Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu.
54  GEN 2:23  Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,popeza wachokera mwa mwamuna.”
55  GEN 2:24  Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.
56  GEN 2:25  Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.
57  GEN 3:1  Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
58  GEN 3:2  Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu,
59  GEN 3:3  koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”
60  GEN 3:4  “Ndithudi simudzafa,inatero njokayo kwa mkaziyo.
61  GEN 3:5  “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”
62  GEN 3:6  Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso.
63  GEN 3:7  Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.
64  GEN 3:8  Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo.
65  GEN 3:9  Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”
66  GEN 3:10  Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”
67  GEN 3:11  Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”
68  GEN 3:12  Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”
69  GEN 3:13  Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
70  GEN 3:14  Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.
71  GEN 3:15  Ndipo ndidzayika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; Iye adzaphwanya mutu wako ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”
72  GEN 3:16  Kwa mkaziyo Iye anati, “Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.”
73  GEN 3:17  Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.
75  GEN 3:19  Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.”
76  GEN 3:20  Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.
78  GEN 3:22  Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.”
80  GEN 3:24  Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
81  GEN 4:1  Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.”
83  GEN 4:3  Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe.
86  GEN 4:6  Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa?
87  GEN 4:7  Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”
88  GEN 4:8  Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.
89  GEN 4:9  Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”
90  GEN 4:10  Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka.
93  GEN 4:13  Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga.
94  GEN 4:14  Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”
95  GEN 4:15  Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe.
96  GEN 4:16  Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.
98  GEN 4:18  Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki.
99  GEN 4:19  Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila.
102  GEN 4:22  Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama.
103  GEN 4:23  Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
104  GEN 4:24  Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.”
105  GEN 4:25  Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”
106  GEN 4:26  Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.
107  GEN 5:1  Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.
109  GEN 5:3  Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
110  GEN 5:4  Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
112  GEN 5:6  Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
113  GEN 5:7  Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
115  GEN 5:9  Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.
116  GEN 5:10  Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
118  GEN 5:12  Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.
119  GEN 5:13  Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
120  GEN 5:14  Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
121  GEN 5:15  Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.
122  GEN 5:16  Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
124  GEN 5:18  Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.
125  GEN 5:19  Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
127  GEN 5:21  Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.
128  GEN 5:22  Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
131  GEN 5:25  Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.
132  GEN 5:26  Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
133  GEN 5:27  Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
134  GEN 5:28  Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.
135  GEN 5:29  Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
136  GEN 5:30  Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
137  GEN 5:31  Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
138  GEN 5:32  Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
139  GEN 6:1  Anthu atayamba kuchuluka pa dziko lapansi ndi kubereka ana aakazi,
141  GEN 6:3  Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”
142  GEN 6:4  Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu.
143  GEN 6:5  Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha,