| 102 | GEN 4:22 | Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
| 246 | GEN 10:11 | Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, |
| 261 | GEN 10:26 | Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, |
| 342 | GEN 14:5 | Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu |
| 344 | GEN 14:7 | Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara. |
| 396 | GEN 16:14 | Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi. |
| 496 | GEN 19:38 | Mwana wamkazi wamngʼono naye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha iye Beni-Ammi. Iyeyu ndiye kholo la Aamoni onse. |
| 562 | GEN 22:14 | Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.” |
| 574 | GEN 23:2 | Anamwalirira ku Kiriyati-Araba, kumeneku ndi ku Hebroni, mʼdziko la Kanaani, ndipo Abrahamu anapita kukakhuza maliro a Sara, namulirira. |
| 654 | GEN 24:62 | Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. |
| 670 | GEN 25:11 | Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya). |
| 921 | GEN 31:47 | Labani anawutcha muluwo Yegara-sahaduta, ndipo Yakobo anawutcha Galeeda. |
| 1020 | GEN 35:8 | Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro). |
| 1030 | GEN 35:18 | Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini. |
| 1039 | GEN 35:27 | Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale. |
| 1079 | GEN 36:38 | Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake. |
| 1080 | GEN 36:39 | Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. |
| 1241 | GEN 41:45 | Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto. |
| 1517 | GEN 50:10 | Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. |
| 1518 | GEN 50:11 | Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu. |
| 1892 | EXO 14:2 | “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. |
| 1899 | EXO 14:9 | Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. |
| 4352 | NUM 21:11 | Kenaka anasamuka ku Oboti nakamanga misasa yawo ku Iye-Abarimu, mʼchipululu chimene chili kummawa kwa Mowabu, kotulukira dzuwa. |
| 4415 | NUM 22:39 | Pamenepo Balaamu anapita pamodzi ndi Balaki ku Kiriati-Huzoti. |
| 4475 | NUM 25:3 | Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri. |
| 4477 | NUM 25:5 | Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.” |
| 4755 | NUM 32:35 | Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha, |
| 4756 | NUM 32:36 | Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo. |
| 4758 | NUM 32:38 | Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo. |
| 4761 | NUM 32:41 | Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi. |
| 4769 | NUM 33:7 | Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli. |
| 4778 | NUM 33:16 | Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava. |
| 4779 | NUM 33:17 | Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti. |
| 4781 | NUM 33:19 | Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi. |
| 4782 | NUM 33:20 | Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina. |
| 4794 | NUM 33:32 | Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi. |
| 4795 | NUM 33:33 | Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata. |
| 4797 | NUM 33:35 | Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi. |
| 4798 | NUM 33:36 | Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi. |
| 4806 | NUM 33:44 | Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu. |
| 4807 | NUM 33:45 | Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi. |
| 4808 | NUM 33:46 | Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu. |
| 4809 | NUM 33:47 | Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo. |
| 4811 | NUM 33:49 | Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu. |
| 4822 | NUM 34:4 | Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, |
| 4827 | NUM 34:9 | ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto. |
| 4828 | NUM 34:10 | “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. |
| 5006 | DEU 3:29 | Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori. |
| 5009 | DEU 4:3 | Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita ku Baala-Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga aliyense amene anatsata Baala wa ku Peori pakati panu. |
| 5052 | DEU 4:46 | Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto. |
| 5847 | DEU 34:6 | Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. |
| 5980 | JOS 7:2 | Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai. |
| 6056 | JOS 9:17 | Tsono Aisraeli ananyamuka ulendo ndipo tsiku lachitatu anafika ku mizinda ya Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriati-Yearimu. |
| 6067 | JOS 10:1 | Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo. |
| 6069 | JOS 10:3 | Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni. |
| 6076 | JOS 10:10 | Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda. |
| 6077 | JOS 10:11 | Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli. |
| 6126 | JOS 11:17 | Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo |
| 6135 | JOS 12:3 | Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga. |
| 6139 | JOS 12:7 | Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. |
| 6161 | JOS 13:5 | Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. |
| 6162 | JOS 13:6 | “Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira. |
| 6173 | JOS 13:17 | Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni, |
| 6175 | JOS 13:19 | Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa, |
| 6176 | JOS 13:20 | Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti. |
| 6182 | JOS 13:26 | ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri. |
| 6183 | JOS 13:27 | Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto. |
| 6210 | JOS 15:6 | napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani. |
| 6229 | JOS 15:25 | Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori) |
| 6231 | JOS 15:27 | Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti |
| 6232 | JOS 15:28 | Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya, |
| 6238 | JOS 15:34 | Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu, |
| 6241 | JOS 15:37 | Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi, |
| 6245 | JOS 15:41 | Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. |
| 6253 | JOS 15:49 | Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri) |
| 6257 | JOS 15:53 | Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki |
| 6258 | JOS 15:54 | Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake. |
| 6263 | JOS 15:59 | Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake |
| 6265 | JOS 15:61 | Mizinda ya ku chipululu inali iyi: Beti-Araba, Midini, Sekaka, |
| 6270 | JOS 16:3 | Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja. |
| 6272 | JOS 16:5 | Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili: Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni. |
| 6284 | JOS 17:7 | Malire a dziko la Manase anayambira ku Aseri, ndipo anakafika ku Mikimetati kummawa kwa Sekemu. Tsono malire anapita kummwera kuloza kwa anthu a ku Eni-Tapuwa. |
| 6288 | JOS 17:11 | Mʼdziko la Isakara ndi Aseri, Manase analinso ndi mizinda ya Beti-Seani ndi Ibuleamu pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. Panalinso Akanaani amene ankakhala ku Dori, Endori, Taanaki ndi Megido pamodzi ndi mizinda yozungulira (wachitatu pa mʼndandandawu ndi Nafati Dori). |
| 6293 | JOS 17:16 | Tsono zidzukulu za Yosefe zinati, “Dziko la ku mapiri ndi losatikwaniradi, komanso Akanaani onse amene akukhala ku chigwa pamodzi ndi amene akukhala ku Beti-Seani ndi madera awo ndiponso amene ali ku chigwa cha Yezireeli ali ndi magaleta azitsulo.” |
| 6307 | JOS 18:12 | Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. |
| 6308 | JOS 18:13 | Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi. |
| 6309 | JOS 18:14 | Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo. |
| 6312 | JOS 18:17 | Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. |
| 6314 | JOS 18:19 | Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera. |
| 6316 | JOS 18:21 | Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi; Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, |
| 6317 | JOS 18:22 | Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli |
| 6319 | JOS 18:24 | Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake |
| 6326 | JOS 19:3 | Hazari-Suwali, Bala, Ezemu, |
| 6328 | JOS 19:5 | Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa, |
| 6329 | JOS 19:6 | Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo. |
| 6331 | JOS 19:8 | Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera. Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo. |
| 6335 | JOS 19:12 | Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya. |
| 6336 | JOS 19:13 | Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni. |
| 6344 | JOS 19:21 | Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi. |
| 6345 | JOS 19:22 | Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake. |