1 | GEN 1:1 | Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
2 | GEN 1:2 | Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. |
3 | GEN 1:3 | Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
4 | GEN 1:4 | Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima. |
5 | GEN 1:5 | Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba. |
6 | GEN 1:6 | Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” |
7 | GEN 1:7 | Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi. |
8 | GEN 1:8 | Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri. |
9 | GEN 1:9 | Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. |
10 | GEN 1:10 | Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
11 | GEN 1:11 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. |
12 | GEN 1:12 | Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
13 | GEN 1:13 | Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu. |
14 | GEN 1:14 | Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; |
15 | GEN 1:15 | zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.” |
16 | GEN 1:16 | Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. |
18 | GEN 1:18 | kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
19 | GEN 1:19 | Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi. |
20 | GEN 1:20 | Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.” |
21 | GEN 1:21 | Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
22 | GEN 1:22 | Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.” |
23 | GEN 1:23 | Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachisanu. |
24 | GEN 1:24 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
25 | GEN 1:25 | Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
26 | GEN 1:26 | Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” |
27 | GEN 1:27 | Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi. |
28 | GEN 1:28 | Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.” |
29 | GEN 1:29 | Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu. |
30 | GEN 1:30 | Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi. |
31 | GEN 1:31 | Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi. |
32 | GEN 2:1 | Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo. |
33 | GEN 2:2 | Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. |
34 | GEN 2:3 | Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira. |
36 | GEN 2:5 | zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka, |
37 | GEN 2:6 | koma kasupe ankatuluka mʼnthaka ndi kuthirira pa dziko lonse. |
38 | GEN 2:7 | Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. |
39 | GEN 2:8 | Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. |
40 | GEN 2:9 | Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa. |
41 | GEN 2:10 | Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi. |
42 | GEN 2:11 | Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
43 | GEN 2:12 | (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
46 | GEN 2:15 | Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira. |
48 | GEN 2:17 | koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.” |
49 | GEN 2:18 | Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.” |
50 | GEN 2:19 | Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. |
51 | GEN 2:20 | Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. |
52 | GEN 2:21 | Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
53 | GEN 2:22 | Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye. |
54 | GEN 2:23 | Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.” |
55 | GEN 2:24 | Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi. |
56 | GEN 2:25 | Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi. |
57 | GEN 3:1 | Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ” |
59 | GEN 3:3 | koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ” |
60 | GEN 3:4 | “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. |
61 | GEN 3:5 | “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.” |
62 | GEN 3:6 | Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. |
63 | GEN 3:7 | Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala. |
64 | GEN 3:8 | Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. |
66 | GEN 3:10 | Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.” |
68 | GEN 3:12 | Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.” |
69 | GEN 3:13 | Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.” |
70 | GEN 3:14 | Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. |
71 | GEN 3:15 | Ndipo ndidzayika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; Iye adzaphwanya mutu wako ndipo iwe udzaluma chidendene chake.” |
72 | GEN 3:16 | Kwa mkaziyo Iye anati, “Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.” |
73 | GEN 3:17 | Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako. |
74 | GEN 3:18 | Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula ndipo udzadya zomera zakuthengo. |
75 | GEN 3:19 | Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.” |
76 | GEN 3:20 | Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo. |
77 | GEN 3:21 | Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. |
78 | GEN 3:22 | Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” |
79 | GEN 3:23 | Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. |
80 | GEN 3:24 | Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo. |
81 | GEN 4:1 | Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” |
82 | GEN 4:2 | Kenaka anabereka mʼbale wake Abele. Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. |
83 | GEN 4:3 | Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. |
84 | GEN 4:4 | Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. |
85 | GEN 4:5 | Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. |
87 | GEN 4:7 | Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” |
88 | GEN 4:8 | Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha. |
89 | GEN 4:9 | Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” |
90 | GEN 4:10 | Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. |
91 | GEN 4:11 | Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. |
92 | GEN 4:12 | Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.” |
93 | GEN 4:13 | Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. |
94 | GEN 4:14 | Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.” |
95 | GEN 4:15 | Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. |
96 | GEN 4:16 | Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni. |
97 | GEN 4:17 | Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. |
98 | GEN 4:18 | Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki. |
99 | GEN 4:19 | Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. |
100 | GEN 4:20 | Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto. |
101 | GEN 4:21 | Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. |
102 | GEN 4:22 | Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
103 | GEN 4:23 | Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. |
104 | GEN 4:24 | Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.” |
105 | GEN 4:25 | Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” |
106 | GEN 4:26 | Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova. |
107 | GEN 5:1 | Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. |