24 | GEN 1:24 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
35 | GEN 2:4 | Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba, |
107 | GEN 5:1 | Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. |
147 | GEN 6:9 | Mbiri ya Nowa inali yotere: Nowa anali munthu wolungama ndi wopanda tchimo pakati pa anthu a mʼbado wake. Ndipo anayenda ndi Mulungu. |
148 | GEN 6:10 | Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
181 | GEN 7:21 | Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu. |
205 | GEN 8:21 | Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. |
217 | GEN 9:11 | Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.” |
237 | GEN 10:2 | Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi. |
238 | GEN 10:3 | Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima. |
239 | GEN 10:4 | Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. |
241 | GEN 10:6 | Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani. |
242 | GEN 10:7 | Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani. |
257 | GEN 10:22 | Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. |
258 | GEN 10:23 | Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki. |
260 | GEN 10:25 | A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. |
362 | GEN 15:1 | Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: “Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.” |
365 | GEN 15:4 | Yehova anayankhula naye nati: “Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.” |
395 | GEN 16:13 | Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.” |
402 | GEN 17:4 | “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. |
572 | GEN 22:24 | Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka. |
672 | GEN 25:13 | Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, |
736 | GEN 27:8 | Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: |
764 | GEN 27:36 | Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?” |
771 | GEN 27:43 | Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. |
862 | GEN 30:31 | Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira: |
914 | GEN 31:40 | Moyo wanga unali wotere: Dzuwa limanditentha masana ndipo usiku ndimazunzika ndi kuzizira. Tulo sindimalipeza konse. |
933 | GEN 32:5 | Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. |
942 | GEN 32:14 | Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake: |
1034 | GEN 35:22 | Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri: |
1035 | GEN 35:23 | Ana a Leya ndi awa: Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni. |
1036 | GEN 35:24 | Ana a Rakele ndi awa: Yosefe ndi Benjamini. |
1037 | GEN 35:25 | Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa: Dani ndi Nafutali. |
1038 | GEN 35:26 | Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa: Gadi ndi Aseri. Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu. |
1042 | GEN 36:1 | Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu: |
1051 | GEN 36:10 | Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau. |
1052 | GEN 36:11 | Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. |
1054 | GEN 36:13 | Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau. |
1055 | GEN 36:14 | Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora. |
1056 | GEN 36:15 | Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, |
1058 | GEN 36:17 | Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau. |
1059 | GEN 36:18 | Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana. |
1061 | GEN 36:20 | Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
1063 | GEN 36:22 | Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani. |
1064 | GEN 36:23 | Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. |
1065 | GEN 36:24 | Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni. |
1066 | GEN 36:25 | Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi. |
1067 | GEN 36:26 | Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. |
1068 | GEN 36:27 | Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. |
1069 | GEN 36:28 | Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani. |
1070 | GEN 36:29 | Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
1072 | GEN 36:31 | Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: |
1081 | GEN 36:40 | Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa: Timna, Aliva, Yeteti, |
1086 | GEN 37:2 | Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake. |
1090 | GEN 37:6 | Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota: |
1167 | GEN 39:17 | Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. |
1185 | GEN 40:12 | Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. |
1191 | GEN 40:18 | Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. |
1201 | GEN 41:5 | Posakhalitsa anagonanso ndipo analota kachiwiri: Analota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi labwino zitabala pa phata limodzi. |
1267 | GEN 42:14 | Yosefe anawawuza kuti, “Ndi momwe ndaneneramo: Inu ndinu akazitape. |
1268 | GEN 42:15 | Ndiye ndikuyesani motere: Ine ndikulumbira pali Farao ndithu, inuyo simudzachoka malo ano mpaka wotsirizayo atabwera kuno. |
1271 | GEN 42:18 | Pa tsiku lachitatu Yosefe anawawuza kuti, “Popeza ine ndimaopa Mulungu, ndipo inuyo ngati mukufuna kukhala ndi moyo muchite izi: |
1286 | GEN 42:33 | Ndipo nduna ija inati kwa ife, “Kuti ndidziwedi kuti ndinu anthu owona mtima muchite izi: Mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, ndipo enanu mutenge chakudya ndi kubwerera kwanu kumene kuli njalako. |
1302 | GEN 43:11 | Tsono abambo awo Israeli anawawuza kuti, “Ngati pafunika kutero, ndiye muchite izi: Ikanimo zipatso zabwino kwambiri za dziko lino mʼmatumba mwanu ndi kumutengera munthuyo ngati mphatso. Mumutengere mafuta wopaka pangʼono, uchi pangʼono, mafuta wonunkhiritsa chakudya, mule, mtedza ndi alimoni. |
1382 | GEN 45:23 | Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake. |
1395 | GEN 46:8 | Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto: Rubeni mwana woyamba wa Yakobo. |
1396 | GEN 46:9 | Ana aamuna a Rubeni ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. |
1397 | GEN 46:10 | Ana aamuna a Simeoni ndi awa: Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani. |
1398 | GEN 46:11 | Ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. |
1399 | GEN 46:12 | Ana aamuna a Yuda ndi awa: Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani. Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli. |
1400 | GEN 46:13 | Ana aamuna a Isakara ndi awa: Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi. |
1401 | GEN 46:14 | Ana aamuna a Zebuloni ndi awa: Seredi, Eloni ndi Yahaleeli. |
1403 | GEN 46:16 | Ana aamuna a Gadi ndi awa: Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli. |
1404 | GEN 46:17 | Ana aamuna a Aseri ndi awa: Imuna, Isiva, Isivi, Beriya ndi Sera mlongo wawo. Ana aamuna a Beriya ndi awa: Heberi ndi Malikieli. |
1406 | GEN 46:19 | Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali: Yosefe ndi Benjamini. |
1407 | GEN 46:20 | Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu. |
1408 | GEN 46:21 | Ana aamuna a Benjamini ndi awa: Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi. |
1410 | GEN 46:23 | Mwana wa mwamuna wa Dani anali: Husimu. |
1411 | GEN 46:24 | Ana aamuna a Nafutali ndi awa: Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu. |
1472 | GEN 48:20 | Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati, “Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati: Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.” Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase. |
1475 | GEN 49:1 | Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo. |
1503 | GEN 49:29 | Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. |
1519 | GEN 50:12 | Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: |
1523 | GEN 50:16 | Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: |
1524 | GEN 50:17 | ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira. |
1534 | EXO 1:1 | Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake: |
1594 | EXO 3:14 | Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” |
1657 | EXO 6:1 | Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.” |
1670 | EXO 6:14 | Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni. |
1672 | EXO 6:16 | Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1702 | EXO 7:16 | Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. |
1703 | EXO 7:17 | Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: |
1735 | EXO 8:20 | Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto. |
1742 | EXO 8:27 | Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala. |
1781 | EXO 10:3 | Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze. |
1828 | EXO 12:11 | Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova. |
1860 | EXO 12:43 | Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa: “Mlendo asadye Paska. |
1922 | EXO 15:1 | Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja. |
1942 | EXO 15:21 | Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.” |