Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   ?    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

57  GEN 3:1  Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ 
65  GEN 3:9  Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?
67  GEN 3:11  Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?
69  GEN 3:13  Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
86  GEN 4:6  Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa?
87  GEN 4:7  Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”
89  GEN 4:9  Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?
90  GEN 4:10  Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka.
317  GEN 12:18  Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako?
318  GEN 12:19  Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!”
328  GEN 13:9  Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.”
363  GEN 15:2  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko?
369  GEN 15:8  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?
390  GEN 16:8  Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
415  GEN 17:17  Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?
434  GEN 18:9  Anthuwo anafunsa Abrahamu kuti, “Mkazi wako Sara ali kuti?Iye anati, “Ali mu tentimu.”
437  GEN 18:12  Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, “Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba.”
438  GEN 18:13  Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?
439  GEN 18:14  Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.”
442  GEN 18:17  Tsono Yehova anati mu mtima mwake, “Kodi ndingamubisire Abrahamu chimene ndikuti ndichite posachedwa?
448  GEN 18:23  Kenaka Abrahamu anasendera kufupi ndi Iye nati, “Kodi mudzawonongera kumodzi wolungama ndi woyipa?
449  GEN 18:24  Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo?
450  GEN 18:25  Ndithu simungachite zimenezi, kupha anthu olungama pamodzi ndi oyipa. Nʼzosatheka kuti inu nʼkufananitsa olungama ndi oyipa. Kodi woweruza wa dziko lapansi nʼkulephera kuchita chilungamo?
453  GEN 18:28  bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.”
454  GEN 18:29  Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.”
455  GEN 18:30  Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.”
456  GEN 18:31  Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.”
457  GEN 18:32  Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.”
463  GEN 19:5  Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.”
470  GEN 19:12  Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno,
478  GEN 19:20  Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.”
500  GEN 20:4  Nthawi imeneyi nʼkuti Abimeleki asanamukhudze mkaziyo, kotero kuti anati, “Ambuye, kodi mudzawonongadi mtundu wolungama?
501  GEN 20:5  Kodi Abrahamu sanandiwuze kuti iyeyu ndi mlongo wake? Ndiponso mkaziyu ankanena kuti Abrahamu ndi mlongo wake. Choncho ine pochita izi, ndinkachita moona mtima ndiponso mopanda chinyengo.”
505  GEN 20:9  Kenaka Abimeleki anayitana Abrahamu ndipo anati, “Kodi wachita chiyani? Ndakulakwira chiyani kuti undibweretsere ine pamodzi ndi anthu anga chilango chachikulu chotere? Wandichitira zinthu zimene sizinayenera kuchitika.”
506  GEN 20:10  Ndipo Abrahamu anafunsa Abimeleki kuti, “Chifukwa chiyani wachita zimenezi?
521  GEN 21:7  Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”
531  GEN 21:17  Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo.
543  GEN 21:29  ndipo Abimeleki anafunsa Abrahamu, “Kodi tanthauzo lake la ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wawapatula pawokhawa nʼchiyani?
555  GEN 22:7  Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.” Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
587  GEN 23:15  “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.”
597  GEN 24:5  Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?
615  GEN 24:23  Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?
623  GEN 24:31  Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.”
631  GEN 24:39  “Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, ‘Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?
639  GEN 24:47  “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?“Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake,
650  GEN 24:58  Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?Iye anayankha kuti, “Ndipita.”
657  GEN 24:65  nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.
681  GEN 25:22  Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.
691  GEN 25:32  Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?
702  GEN 26:9  Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”
703  GEN 26:10  Tsono Abimeleki anati, “Nʼchiyani chimene watichitira? Mmodzi mwa anthuwa anatsala pangʼono kugona ndi mkazi wako ndipo ukanatisandutsa ife kukhala olakwa.”
720  GEN 26:27  Tsopano Isake anawafunsa kuti, “Bwanji mwabwera kwa ine, popeza munandichitira nkhanza ndi kundithamangitsa?
746  GEN 27:18  Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.” Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?
748  GEN 27:20  Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”
752  GEN 27:24  Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
760  GEN 27:32  Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
761  GEN 27:33  Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
764  GEN 27:36  Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?
765  GEN 27:37  Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?
766  GEN 27:38  Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
773  GEN 27:45  Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?
800  GEN 29:4  Yakobo anafunsa abusawo kuti, “Abale anga, mwachokera kuti?Iwo anayankha, “Tachokera ku Harani.”
801  GEN 29:5  Iye anawafunsanso kuti, “Kodi Labani, mdzukulu wa Nahori mukumudziwa?Iwo anayankha, “Inde tikumudziwa?
802  GEN 29:6  Ndipo Yakobo anawafunsanso, “Kodi ali bwino?Iwo anati, “Inde ali bwino. Nayu Rakele mwana wake akubwera apoyu ndi nkhosa.”
811  GEN 29:15  Tsono Labani anawuza Yakobo kuti, “Zoona iwe ndi ife ndi abale. Koma suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro. Ndiwuze kuti malipiro ako azikhala wotani?
821  GEN 29:25  Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?
833  GEN 30:2  Yakobo anapsera mtima Rakele ndipo nati, “Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu amene wakulepheretsa iwe kukhala ndi ana?
846  GEN 30:15  Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.” Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.”
862  GEN 30:31  Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira:
888  GEN 31:14  Pamenepo Rakele ndi Leya anayankha, “Kodi ngati ife tilinso ndi gawo ngati cholowa pa chuma cha abambo athu?
889  GEN 31:15  Kodi abambo athu samationa ife ngati alendo? Iwo anatigulitsa ndi kuwononga ndalama zonse anazipeza pa ifezo.
900  GEN 31:26  Tsono Labani anati kwa Yakobo, “Kodi ndakuchita chiyani kuti iwe undinamize ndi kutenga ana anga ngati anthu ogwidwa ku nkhondo?
901  GEN 31:27  Chifukwa chiyani unandinamiza ndi kuthawa mozemba wosandiwuza? Ukanandiwuza, bwezi titatsanzikana mwa chisangalalo ndi kuyimba nyimbo ndi zisekese ndi azeze.
904  GEN 31:30  Ndikudziwa kuti unachoka chifukwa unapukwa kufuna kubwerera kwanu kwa abambo ako. Koma nʼchifukwa chiyani unaba milungu yanga?
910  GEN 31:36  Yakobo anapsa mtima nafunsa Labani mwaukali kuti, “Kodi ndalakwa chiyani? Ndi tchimo lanji limene ndachita kuti muchite kundisaka chonchi?
911  GEN 31:37  Chifukwa chiyani mwafunyulula katundu wanga? Ndipo mwapeza chiyani cha inu pamenepa? Chimene mwapezapo chiyikeni poyera pamaso pa abale anu ndi anga kuti atiweruze.
917  GEN 31:43  Labani anayankha Yakobo nati, “Ana aakaziwa ndi anga, ana awo ndi anganso. Ziwetozi ndi zanga. Chilichonse ukuona apa ndi changa. Koma tsopano ndingachite chiyani ndi ana anga aakaziwa kapena ndi ana awo?
946  GEN 32:18  Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?
956  GEN 32:28  Munthu uja anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi dzina lako ndiwe yani?Iye anayankha, “Ndine Yakobo.”
958  GEN 32:30  Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.” Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?Kenaka anamudalitsa pomwepo.
966  GEN 33:5  Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”
969  GEN 33:8  Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.”
976  GEN 33:15  Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.” Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”
1012  GEN 34:31  Koma iwo anayankha kuti, “Pepani, nanga achite kumusandutsa mlongo wathu ngati mkazi wachiwerewere?
1092  GEN 37:8  Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo.
1094  GEN 37:10  Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?
1099  GEN 37:15  munthu wina anamupeza akungozungulirazungulira mʼmunda ndipo anamufunsa, “Ukufunafuna chiyani?
1100  GEN 37:16  Iye anayankha, “Ndikufuna abale anga. Mungandiwuze kumene akudyetsa ziweto zawo?
1110  GEN 37:26  Yuda anafunsa abale ake nati, “Kodi tidzapindula chiyani tikapha mʼbale wathuyu ndi kuphimbitsa magazi ake?
1114  GEN 37:30  nabwerera kwa abale ake nati, “Mnyamata uja mulibemo! Nanga ndilowere kuti ine tsopano?
1136  GEN 38:16  Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake. Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?
1137  GEN 38:17  Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.” Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?
1138  GEN 38:18  Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi.
1141  GEN 38:21  Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.”
1145  GEN 38:25  Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?
1159  GEN 39:9  Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?
1180  GEN 40:7  Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?
1234  GEN 41:38  Choncho Farao anafunsa nduna zake nati, “Kodi tingathe kumupeza munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?
1254  GEN 42:1  Yakobo atamva kuti ku Igupto kuli tirigu, anati kwa ana ake, “Nʼchifukwa chiyani mukungoyangʼanana wina ndi mnzake?
1260  GEN 42:7  Yosefe atangowaona abale ake anawazindikira, koma ananamizira kukhala ngati mlendo nawayankhula mwaukali kuwafunsa kuti, “Mwachokera kuti?Iwo anayankha, “Ku dziko la Kanaani, tikudzagula chakudya.”