Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   ‘    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

54  GEN 2:23  Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”
57  GEN 3:1  Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
59  GEN 3:3  koma Mulungu anati, Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”
73  GEN 3:17  Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.
311  GEN 12:12  Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo.
360  GEN 14:23  kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, Ndamulemeretsa Abramu.’
438  GEN 18:13  Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’
509  GEN 20:13  Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ”
599  GEN 24:7  Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi.
606  GEN 24:14  Ine ndipempha mtsikana wina kuti, Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.
629  GEN 24:37  Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani,
631  GEN 24:39  “Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?’
632  GEN 24:40  “Iye anayankha, Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa.
634  GEN 24:42  “Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu,
636  GEN 24:44  ndipo ngati adzandiyankha kuti, Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.”
637  GEN 24:45  “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, Chonde patseko madzi akumwa.’
638  GEN 24:46  “Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo.
639  GEN 24:47  “Ndinamufunsa kuti, Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake,
702  GEN 26:9  Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”
735  GEN 27:7  Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’
882  GEN 31:8  Pamene abambo anu anati, Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi.
885  GEN 31:11  Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, Yakobo.’ Ine ndinayankha, Ee, Ambuye.’
886  GEN 31:12  Ndipo iye anati, Tayangʼana ndipo taona kuti atonde onse okwerana ndi ziweto ali amichocholozi, amawangamawanga kapena a mathothomathotho, popeza ndaona zonse zimene Labani wakhala akukuchitira.
903  GEN 31:29  Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’
933  GEN 32:5  Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano.
938  GEN 32:10  Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’
946  GEN 32:18  Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’
947  GEN 32:19  Pamenepo ukayankhe kuti, Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ”
949  GEN 32:21  Muzikanena kuti, Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.”
1101  GEN 37:17  Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, Tiyeni tipite ku Dotani.’ ” Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani.
1142  GEN 38:22  Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ”
1284  GEN 42:31  Koma tinamuwuza kuti, Ndife anthu woona mtima osati akazitape.
1294  GEN 43:3  Koma Yuda anati kwa iye, “Munthu uja anatichenjeza monenetsa kuti, Simudzandionanso ine pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanu.’
1296  GEN 43:5  Koma mukapanda kumulola, ife sitipita, chifukwa munthuyo anatiwuza kuti, Simudzandionanso pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanuyo.’ ”
1298  GEN 43:7  Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?”
1329  GEN 44:4  Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino?
1344  GEN 44:19  Mbuye wanga munafunsa akapolo anufe kuti, Kodi muli ndi abambo anu kapena mʼbale wanu?’
1345  GEN 44:20  Ndipo ife tinayankha, Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’
1346  GEN 44:21  “Ndipo inu munatiwuza kuti, Mubwere naye kwa ine kuti ndidzamuone ndekha.’
1347  GEN 44:22  Ife tinati, Mbuye wathu, mnyamatayo sangasiye abambo ake, akawasiya ndiye kuti abambo akewo adzafa.’
1348  GEN 44:23  Koma inu munatichenjeza kuti, Pokhapokha mutabwera naye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri, simudzandionanso.’
1350  GEN 44:25  “Abambo athu anatiwuza kuti, Pitaninso mukagule kachakudya pangʼono.’
1351  GEN 44:26  Koma tinati, Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’
1352  GEN 44:27  “Koma kapolo wanu, abambo athu anatiwuza kuti, Inu mukudziwa kuti mkazi wanga anandiberekera ana aamuna awiri.
1357  GEN 44:32  Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’
1368  GEN 45:9  Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe.
1376  GEN 45:17  Farao anati kwa Yosefe, “Uwawuze abale ako kuti, Senzetsani nyama zanu katundu ndi kubwerera ku dziko la Kanaani.
1378  GEN 45:19  “Uwawuzenso kuti, Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno.
1418  GEN 46:31  Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine.
1420  GEN 46:33  Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, Kodi mumagwira ntchito yanji?’
1421  GEN 46:34  Muyankhe kuti, Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”
1456  GEN 48:4  nati kwa ine, Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’
1512  GEN 50:5  Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”
1524  GEN 50:17  Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
1593  EXO 3:13  Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?”
1594  EXO 3:14  Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: NDINE wandituma kwa inu.’ ”
1595  EXO 3:15  Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli.
1596  EXO 3:16  “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani.
1598  EXO 3:18  “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’
1603  EXO 4:1  Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, Yehova sanakuonekere iwe.’ ”
1624  EXO 4:22  Ndipo iwe ukati kwa Farao, Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’
1625  EXO 4:23  Choncho ndikuti, Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”
1634  EXO 5:1  Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”
1641  EXO 5:8  Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
1643  EXO 5:10  Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “Farao akuti sadzakupatsaninso udzu.
1649  EXO 5:16  Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.”
1650  EXO 5:17  Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’
1662  EXO 6:6  “Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.
1695  EXO 7:9  “Ngati Farao adzati kwa inu, Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.”
1702  EXO 7:16  Ndipo ukamuwuze Farao kuti, Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere.
1705  EXO 7:19  Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”
1716  EXO 8:1  Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ”
1731  EXO 8:16  Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.
1781  EXO 10:3  Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.
1843  EXO 12:26  Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’
1844  EXO 12:27  Inu mukawawuze kuti, Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza.
1876  EXO 13:8  Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’
1882  EXO 13:14  “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu.
1893  EXO 14:3  Farao adzaganiza kuti Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’
1902  EXO 14:12  Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”
1957  EXO 16:9  Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”
1960  EXO 16:12  “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
1964  EXO 16:16  Yehova walamula kuti, Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ”
1971  EXO 16:23  Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ”
1980  EXO 16:32  Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”
2031  EXO 19:4  Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine.
2039  EXO 19:12  Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu.
2074  EXO 20:22  Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba.
2083  EXO 21:5  “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’
2447  EXO 32:8  Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”
2451  EXO 32:12  Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu.
2452  EXO 32:13  Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ”
2462  EXO 32:23  Iwo anati kwa ine, Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’
2463  EXO 32:24  Choncho ine ndinawawuza kuti, Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”
2466  EXO 32:27  Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ”
2475  EXO 33:1  Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’
2479  EXO 33:5  Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.”
2486  EXO 33:12  Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’
2749  LEV 1:3  Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire.
2756  LEV 1:10  Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema.