109 | GEN 5:3 | Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
110 | GEN 5:4 | Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
111 | GEN 5:5 | Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira. |
112 | GEN 5:6 | Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. |
113 | GEN 5:7 | Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
115 | GEN 5:9 | Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. |
117 | GEN 5:11 | Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira. |
118 | GEN 5:12 | Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. |
119 | GEN 5:13 | Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
120 | GEN 5:14 | Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira. |
122 | GEN 5:16 | Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
125 | GEN 5:19 | Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
128 | GEN 5:22 | Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
138 | GEN 5:32 | Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. |
141 | GEN 6:3 | Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
166 | GEN 7:6 | Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600. |
171 | GEN 7:11 | Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. |
184 | GEN 7:24 | Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150. |
187 | GEN 8:3 | Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, |
197 | GEN 8:13 | Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
234 | GEN 9:28 | Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. |
235 | GEN 9:29 | Anamwalira ali ndi zaka 950. |
277 | GEN 11:10 | Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. |
278 | GEN 11:11 | Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
280 | GEN 11:13 | Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
282 | GEN 11:15 | Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
284 | GEN 11:17 | Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
286 | GEN 11:19 | Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
288 | GEN 11:21 | Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
290 | GEN 11:23 | Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
293 | GEN 11:26 | Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. |
299 | GEN 11:32 | Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205. |
374 | GEN 15:13 | Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. |
415 | GEN 17:17 | Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” |
454 | GEN 18:29 | Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.” |
519 | GEN 21:5 | Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa. |
587 | GEN 23:15 | “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.” |
588 | GEN 23:16 | Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito. |
614 | GEN 24:22 | Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100. |
685 | GEN 25:26 | Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa. |
727 | GEN 26:34 | Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti. |
935 | GEN 32:7 | Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.” |
943 | GEN 32:15 | Anasankhula mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi 200 ndi nkhosa zazimuna makumi awiri, |
944 | GEN 32:16 | ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi. |
962 | GEN 33:1 | Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja. |
980 | GEN 33:19 | Malo amenewo anagula kwa zidzukulu za Hamori, abambo a Sekemu ndi ndalama 100 zasiliva. |
1040 | GEN 35:28 | Isake anakhala ndi moyo zaka 180. |
1242 | GEN 41:46 | Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto. |
1414 | GEN 46:27 | Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70. |
1430 | GEN 47:9 | Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.” |
1510 | GEN 50:3 | Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri. |
1529 | GEN 50:22 | Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 |
1533 | GEN 50:26 | Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto. |
1538 | EXO 1:5 | Anthu onse obadwa mwa Yakobo analipo 70. Yosefe nʼkuti ali kale ku Igupto. |
1693 | EXO 7:7 | Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao. |
1854 | EXO 12:37 | Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana. |
1857 | EXO 12:40 | Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430. |
1858 | EXO 12:41 | Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto. |
1897 | EXO 14:7 | Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. |
1983 | EXO 16:35 | Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani. |
2021 | EXO 18:21 | Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. |
2025 | EXO 18:25 | Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. |
2196 | EXO 24:18 | Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku. |
2241 | EXO 26:5 | Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. |
2246 | EXO 26:10 | Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. |
2247 | EXO 26:11 | Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. |
2255 | EXO 26:19 | Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. |
2257 | EXO 26:21 | Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. |
2291 | EXO 27:18 | Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. |
2467 | EXO 32:28 | Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000. |
2525 | EXO 34:28 | Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi. |
2580 | EXO 36:13 | Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi. |
2585 | EXO 36:18 | Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. |
2591 | EXO 36:24 | ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. |
2658 | EXO 38:24 | Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika. |
2659 | EXO 38:25 | Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. |
2660 | EXO 38:26 | Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. |
2661 | EXO 38:27 | Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. |
3533 | LEV 26:8 | Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga. |
3574 | LEV 27:3 | mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. |
3626 | NUM 1:21 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500. |
3628 | NUM 1:23 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300. |
3630 | NUM 1:25 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650. |
3632 | NUM 1:27 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600. |
3634 | NUM 1:29 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400. |
3636 | NUM 1:31 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400. |
3638 | NUM 1:33 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500. |