109 | GEN 5:3 | Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
111 | GEN 5:5 | Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira. |
122 | GEN 5:16 | Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
128 | GEN 5:22 | Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
129 | GEN 5:23 | Zaka zonse za Enoki zinali 365. |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
234 | GEN 9:28 | Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. |
279 | GEN 11:12 | Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. |
280 | GEN 11:13 | Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
282 | GEN 11:15 | Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
283 | GEN 11:16 | Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. |
284 | GEN 11:17 | Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
287 | GEN 11:20 | Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. |
351 | GEN 14:14 | Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. |
676 | GEN 25:17 | Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. |
944 | GEN 32:16 | ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi. |
1242 | GEN 41:46 | Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto. |
1402 | GEN 46:15 | Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33. |
1430 | GEN 47:9 | Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.” |
1672 | EXO 6:16 | Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1674 | EXO 6:18 | Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. |
1676 | EXO 6:20 | Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1693 | EXO 7:7 | Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao. |
1857 | EXO 12:40 | Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430. |
1858 | EXO 12:41 | Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto. |
2235 | EXO 25:39 | Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. |
2274 | EXO 27:1 | “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. |
2285 | EXO 27:12 | “Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi. |
2286 | EXO 27:13 | Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, kutalika kwa bwalo kukhale mamita 23. |
2291 | EXO 27:18 | Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. |
2310 | EXO 28:16 | Kutalika kwake kukhale kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, ndipo chikhale chopinda pawiri. |
2467 | EXO 32:28 | Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000. |
2629 | EXO 37:24 | Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. |
2635 | EXO 38:1 | Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. |
2646 | EXO 38:12 | Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. |
2647 | EXO 38:13 | Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, inalinso yotalika mamita 23. |
2659 | EXO 38:25 | Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. |
2660 | EXO 38:26 | Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. |
2661 | EXO 38:27 | Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. |
2674 | EXO 39:9 | Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. |
3049 | LEV 12:4 | Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha. |
3628 | NUM 1:23 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300. |
3640 | NUM 1:35 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200. |
3642 | NUM 1:37 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400. |
3648 | NUM 1:43 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400. |
3651 | NUM 1:46 | Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550. |
3672 | NUM 2:13 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300. |
3680 | NUM 2:21 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200. |
3682 | NUM 2:23 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400. |
3689 | NUM 2:30 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400. |
3691 | NUM 2:32 | Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. |
3736 | NUM 3:43 | Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273. |
3739 | NUM 3:46 | Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi, |
3743 | NUM 3:50 | Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. |
3784 | NUM 4:40 | atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630. |
3788 | NUM 4:44 | atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200. |
4498 | NUM 26:7 | Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730. |
4516 | NUM 26:25 | Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300. |
4528 | NUM 26:37 | Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo. |
4538 | NUM 26:47 | Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400. |
4542 | NUM 26:51 | Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. |
4553 | NUM 26:62 | Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo. |
4701 | NUM 31:35 | ndi atsikana omwe sanagonepo ndi mwamuna 32,000. |
4702 | NUM 31:36 | Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali: nkhosa 337,500, |
4704 | NUM 31:38 | ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72; |
4705 | NUM 31:39 | abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61; |
4706 | NUM 31:40 | anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32. |
4709 | NUM 31:43 | Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500, |
4710 | NUM 31:44 | ngʼombe 36,000, |
4711 | NUM 31:45 | abulu 30,500, |
4801 | NUM 33:39 | Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123. |
4954 | DEU 2:14 | Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira. |
5981 | JOS 7:3 | Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.” |
5982 | JOS 7:4 | Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai. |
5983 | JOS 7:5 | Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu. |
6007 | JOS 8:3 | Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku |
6156 | JOS 12:24 | mfumu ya Tiriza imodzi mafumu onse pamodzi analipo 31. |
6329 | JOS 19:6 | Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo. |
6387 | JOS 21:4 | Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. |
6389 | JOS 21:6 | Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani. |
6402 | JOS 21:19 | Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni. |
6416 | JOS 21:33 | Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto. |
6702 | JDG 7:6 | Ndipo anthu 300 anamwa mokhathira, pamene ena onse anagwada pansi pakumwa. |
6703 | JDG 7:7 | Yehova anati kwa Gideoni, “Ndi anthu 300 amene anamwa madzi mokhathira ndi manja awo ndidzakupulumutsani ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu. Koma anthu ena onse apite ku nyumba kwawo.” |
6704 | JDG 7:8 | Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo. Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa. |
6712 | JDG 7:16 | Anawagawa anthu 300 aja magulu atatu, nawapatsa malipenga mʼmanja mwawo ndi mbiya zimene mʼkati mwake munali nsakali zoyaka. |
6718 | JDG 7:22 | Anthu 300 aja ataliza malipenga, Yehova anawasokoneza ankhondo a Midiyani aja motero kuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo anathawira ku Beti-Sita cha ku Zerera mpaka ku malire a Abeli-Mehola pafupi ndi Tabati. |
6725 | JDG 8:4 | Gideoni anafika ndi kuwoloka mtsinje wa Yorodani pamodzi ndi anthu 300 amene anali naye. Ngakhale kuti anali otopa anapirikitsabe adani awo. |
6815 | JDG 10:2 | Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri. |
6857 | JDG 11:26 | Pamene Aisraeli ankakhala mʼdziko la Hesiboni ndi mʼmidzi yake, mʼdziko la Aroeri ndi midzi yake, komanso mʼmizinda yonse imene ili mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani inu simunalande malowo nthawi imeneyo? |
6935 | JDG 15:4 | Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali. |
6942 | JDG 15:11 | Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?” Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.” |
6978 | JDG 16:27 | Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera. |
7309 | 1SA 4:10 | Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. |
7455 | 1SA 11:8 | Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. |