Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   4    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

119  GEN 5:13  Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
153  GEN 6:15  Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake.
280  GEN 11:13  Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
282  GEN 11:15  Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
283  GEN 11:16  Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi.
284  GEN 11:17  Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
374  GEN 15:13  Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.
453  GEN 18:28  bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?” Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.”
454  GEN 18:29  Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.”
587  GEN 23:15  “Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.”
588  GEN 23:16  Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.
727  GEN 26:34  Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti.
935  GEN 32:7  Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.”
944  GEN 32:16  ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi.
962  GEN 33:1  Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja.
1449  GEN 47:28  Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147.
1510  GEN 50:3  Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
1835  EXO 12:18  Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo.
1857  EXO 12:40  Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430.
1858  EXO 12:41  Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto.
1983  EXO 16:35  Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani.
2196  EXO 24:18  Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.
2206  EXO 25:10  “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.
2213  EXO 25:17  “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69.
2219  EXO 25:23  “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.
2235  EXO 25:39  Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
2249  EXO 26:13  Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo.
2255  EXO 26:19  Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
2257  EXO 26:21  Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse.
2282  EXO 27:9  “Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.
2284  EXO 27:11  Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
2291  EXO 27:18  Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa.
2385  EXO 30:2  Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo.
2525  EXO 34:28  Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.
2591  EXO 36:24  ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
2606  EXO 37:1  Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.
2611  EXO 37:6  Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69.
2615  EXO 37:10  Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.
2629  EXO 37:24  Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
2630  EXO 37:25  Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo.
2643  EXO 38:9  Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.
2645  EXO 38:11  Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
2659  EXO 38:25  Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika.
2661  EXO 38:27  Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi.
2663  EXO 38:29  Mkuwa ochokera ku nsembe yoweyula unali makilogalamu 2,425.
3408  LEV 23:5  Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba.
3478  LEV 25:8  “ ‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49.
3626  NUM 1:21  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.
3630  NUM 1:25  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.
3632  NUM 1:27  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
3634  NUM 1:29  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.
3636  NUM 1:31  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
3638  NUM 1:33  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.
3642  NUM 1:37  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.
3646  NUM 1:41  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.
3648  NUM 1:43  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.
3663  NUM 2:4  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.
3665  NUM 2:6  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400.
3667  NUM 2:8  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400.
3668  NUM 2:9  Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka.
3670  NUM 2:11  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500.
3674  NUM 2:15  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650.
3675  NUM 2:16  Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.
3678  NUM 2:19  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500.
3682  NUM 2:23  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400.
3687  NUM 2:28  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500.
3689  NUM 2:30  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400.
3939  NUM 7:88  Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.
3964  NUM 8:24  “Ntchito za Alevi ndi izi: Amuna a zaka 24 kapena kuposera pamenepa ndiye azibwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano.
3969  NUM 9:3  Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.”
3971  NUM 9:5  ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
3977  NUM 9:11  Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba.
4244  NUM 17:14  Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora.
4481  NUM 25:9  Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa.
4498  NUM 26:7  Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.
4509  NUM 26:18  Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.
4516  NUM 26:25  Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.
4532  NUM 26:41  Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.
4534  NUM 26:43  Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.
4538  NUM 26:47  Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.
4541  NUM 26:50  Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.
4595  NUM 28:16  “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova.
4851  NUM 35:4  “Malo a msipu a mudziwo amene mudzawapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mudzi ndipo adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mudziwo.
4853  NUM 35:6  “Isanu ndi umodzi mwa midzi imene mudzapereke kwa Alevi idzakhala mizinda yopulumukirako, kumene munthu wopha mnzake adzathawireko. Ndipo mudzawapatsenso midzi ina 42.
4854  NUM 35:7  Midzi yonse imene mudzapereke kwa Alevi idzakhale 48, pamodzi ndi malo oweterako ziweto.
5925  JOS 4:13  Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo.
5946  JOS 5:10  Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo.
6199  JOS 14:10  “Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85.
6240  JOS 15:36  Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.
6323  JOS 18:28  Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.
6424  JOS 21:41  Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto.
6633  JDG 5:8  Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
6749  JDG 8:28  Choncho Amidiyani anagonjetsedwa ndi Aisraeli ndipo sanayeserenso kuwawukira. Ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 40 pamene Gideoni anali ndi moyo.
6877  JDG 12:6  Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’ ” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000.
7058  JDG 20:2  Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga.