121 | GEN 5:15 | Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. |
124 | GEN 5:18 | Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. |
126 | GEN 5:20 | Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira. |
127 | GEN 5:21 | Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. |
129 | GEN 5:23 | Zaka zonse za Enoki zinali 365. |
133 | GEN 5:27 | Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira. |
166 | GEN 7:6 | Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600. |
171 | GEN 7:11 | Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. |
197 | GEN 8:13 | Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
398 | GEN 16:16 | Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86. |
685 | GEN 25:26 | Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa. |
1405 | GEN 46:18 | Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16. |
1413 | GEN 46:26 | Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66. |
1854 | EXO 12:37 | Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana. |
1897 | EXO 14:7 | Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. |
2206 | EXO 25:10 | “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. |
2213 | EXO 25:17 | “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. |
2219 | EXO 25:23 | “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. |
2249 | EXO 26:13 | Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. |
2252 | EXO 26:16 | Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69. |
2261 | EXO 26:25 | Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse. |
2282 | EXO 27:9 | “Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. |
2284 | EXO 27:11 | Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. |
2291 | EXO 27:18 | Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. |
2385 | EXO 30:2 | Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. |
2588 | EXO 36:21 | Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69. |
2597 | EXO 36:30 | Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse. |
2606 | EXO 37:1 | Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. |
2611 | EXO 37:6 | Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. |
2615 | EXO 37:10 | Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. |
2630 | EXO 37:25 | Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo. |
2643 | EXO 38:9 | Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. |
2645 | EXO 38:11 | Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. |
2660 | EXO 38:26 | Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. |
2747 | LEV 1:1 | 26 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati, |
3050 | LEV 12:5 | Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo. |
3574 | LEV 27:3 | mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. |
3626 | NUM 1:21 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500. |
3630 | NUM 1:25 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650. |
3632 | NUM 1:27 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600. |
3644 | NUM 1:39 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700. |
3651 | NUM 1:46 | Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550. |
3663 | NUM 2:4 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600. |
3668 | NUM 2:9 | Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka. |
3670 | NUM 2:11 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500. |
3674 | NUM 2:15 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650. |
3685 | NUM 2:26 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700. |
3690 | NUM 2:31 | Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. |
3691 | NUM 2:32 | Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. |
3721 | NUM 3:28 | Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika. |
3727 | NUM 3:34 | Chiwerengero cha amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 6,200. |
3743 | NUM 3:50 | Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. |
3784 | NUM 4:40 | atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630. |
3939 | NUM 7:88 | Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa. |
4046 | NUM 11:21 | Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ |
4513 | NUM 26:22 | Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500. |
4516 | NUM 26:25 | Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300. |
4518 | NUM 26:27 | Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500. |
4532 | NUM 26:41 | Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600. |
4534 | NUM 26:43 | Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400. |
4542 | NUM 26:51 | Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. |
4698 | NUM 31:32 | Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000, |
4700 | NUM 31:34 | abulu 61,000, |
4703 | NUM 31:37 | mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675; |
4704 | NUM 31:38 | ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72; |
4705 | NUM 31:39 | abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61; |
4706 | NUM 31:40 | anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32. |
4710 | NUM 31:44 | ngʼombe 36,000, |
4712 | NUM 31:46 | anthu 16,000. |
4981 | DEU 3:4 | Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu. |
5983 | JOS 7:5 | Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu. |
6186 | JOS 13:30 | Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko. |
6245 | JOS 15:41 | Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. |
6345 | JOS 19:22 | Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake. |
6601 | JDG 3:31 | Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli. |
7006 | JDG 18:11 | Kenaka anthu 600 a fuko la Dani ananyamuka ku Zora ndi Esitaoli atanyamula zida za nkhondo. |
7011 | JDG 18:16 | Nthawi imeneyi nʼkuti anthu 600 a fuko la Dani aja atayima pa chipata atanyamula zida za nkhondo. |
7012 | JDG 18:17 | Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata. |
7071 | JDG 20:15 | Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa. |
7502 | 1SA 13:15 | Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600. |
7512 | 1SA 14:2 | Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. |
7826 | 1SA 23:13 | Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja. |
7935 | 1SA 27:2 | Choncho Davide ndi anthu 600 amene anali nawo anachoka napita kwa Akisi mwana wa Maoki mfumu ya ku Gati. |
7990 | 1SA 30:9 | Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena. |
8083 | 2SA 2:31 | Koma ankhondo a Davide anapha ankhondo a fuko la Benjamini 360 amene anali ndi Abineri. |
8410 | 2SA 15:18 | Ankhondo ake onse anayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti, pamodzinso ndi Agiti okwanira 600 amene anamutsata kuchokera ku Gati, nawonso anayenda pamaso pake. |
8969 | 1KI 7:32 | Pansi pa matabwawo panali mikombero inayi, ndipo mitanda ya mikomberoyo inalumikizidwa ku phakalo. Msinkhu wa mkombero uliwonse unali masentimita 66. |
9111 | 1KI 10:29 | Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya. |
9294 | 1KI 16:8 | Mʼchaka cha 26 cha ufumu wa Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira ku Tiriza zaka ziwiri. |
9310 | 1KI 16:24 | Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 za siliva ndipo pa phiripo anamangapo mzinda, nawutcha Samariya, potsata dzina la Semeri, dzina la mwini wakale wa phirilo. |
9656 | 2KI 5:5 | Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero. |
9674 | 2KI 5:23 | Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi. |
9885 | 2KI 13:10 | Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16. |
9921 | 2KI 14:21 | Ndipo anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya, amene anali ndi zaka 16 namulonga ufumu mʼmalo mwa abambo ake Amaziya. |
9931 | 2KI 15:2 | Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 16 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. |
9962 | 2KI 15:33 | Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Amayi ake anali Yerusa mwana wa Zadoki. |
9969 | 2KI 16:2 | Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira. |