Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   7    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

104  GEN 4:24  Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.”
113  GEN 5:7  Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
118  GEN 5:12  Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.
131  GEN 5:25  Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.
132  GEN 5:26  Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
137  GEN 5:31  Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
171  GEN 7:11  Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka.
188  GEN 8:4  ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.
198  GEN 8:14  Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.
288  GEN 11:21  Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
293  GEN 11:26  Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
303  GEN 12:4  Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75.
573  GEN 23:1  Sara anakhala ndi moyo zaka 127.
666  GEN 25:7  Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175.
676  GEN 25:17  Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
1086  GEN 37:2  Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.
1414  GEN 46:27  Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.
1449  GEN 47:28  Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147.
1538  EXO 1:5  Anthu onse obadwa mwa Yakobo analipo 70. Yosefe nʼkuti ali kale ku Igupto.
1672  EXO 6:16  Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.
1676  EXO 6:20  Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.
2274  EXO 27:1  “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229.
2635  EXO 38:1  Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229.
3632  NUM 1:27  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
3636  NUM 1:31  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
3644  NUM 1:39  Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.
3663  NUM 2:4  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.
3667  NUM 2:8  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400.
3685  NUM 2:26  Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700.
3690  NUM 2:31  Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo.
3715  NUM 3:22  Chiwerengero cha amuna onse amene anawawerenga a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 7,500.
3736  NUM 3:43  Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273.
3739  NUM 3:46  Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi,
3780  NUM 4:36  atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750.
3936  NUM 7:85  Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika.
4041  NUM 11:16  Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe.
4244  NUM 17:14  Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora.
4498  NUM 26:7  Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.
4513  NUM 26:22  Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.
4525  NUM 26:34  Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.
4542  NUM 26:51  Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.
4698  NUM 31:32  Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000,
4699  NUM 31:33  Ngʼombe 72,000,
4702  NUM 31:36  Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali: nkhosa 337,500,
4703  NUM 31:37  mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675;
4704  NUM 31:38  ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72;
4709  NUM 31:43  Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500,
4771  NUM 33:9  Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.
6518  JDG 1:7  Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko.
6735  JDG 8:14  Kumeneko iye anagwira mnyamata wa ku Sukoti ndipo atamufunsa, mnyamatayo anamulembera mayina a akuluakulu ndi atsogoleri 77 a ku Sukoti.
6751  JDG 8:30  Ana a Gideoni anali 70 popeza anali ndi akazi ambiri.
6760  JDG 9:4  Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira.
6774  JDG 9:18  Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu.
6780  JDG 9:24  Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo.
6812  JDG 9:56  Mmenemu ndi mmene Mulungu analipsirira tchimo la Abimeleki limene anachitira abambo ake pakupha abale ake 70 aja.
6885  JDG 12:14  Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu.
7071  JDG 20:15  Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa.
7072  JDG 20:16  Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya.
7103  JDG 20:47  Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi.
7352  1SA 6:19  Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri.
7625  1SA 17:5  Iye ankavala chipewa chamkuwa ndi malaya achitsulo olemera makilogalamu 57.
7882  1SA 25:18  Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu.
8216  2SA 8:4  Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
8261  2SA 10:18  Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo.
8695  2SA 23:39  ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37.
8710  2SA 24:15  Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba.
8896  1KI 5:29  Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri,
8901  1KI 6:2  Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka.
9114  1KI 11:3  Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa.
9242  1KI 14:21  Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.
9296  1KI 16:10  Zimuri anadzalowa, namukantha ndi kumupha mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Ndipo Zimuriyo anakhala mfumu mʼmalo mwake.
9301  1KI 16:15  Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimuri analamulira ku Tiriza masiku asanu ndi awiri. Gulu la ankhondo linali litamanga misasa pafupi ndi Gibetoni, mzinda wa Afilisti.
9408  1KI 19:18  Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”
9426  1KI 20:15  Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000.
9441  1KI 20:30  Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.
9535  1KI 22:52  Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
9606  2KI 3:26  Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera.
9798  2KI 10:1  Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati,
9803  2KI 10:6  Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.” Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera.
9804  2KI 10:7  Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu.
9876  2KI 13:1  Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17.
9885  2KI 13:10  Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16.
9930  2KI 15:1  Mʼchaka cha 27 cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
9968  2KI 16:1  Mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
10222  2KI 24:16  Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000.
10253  2KI 25:27  Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27.
10450  1CH 5:18  Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo.
10544  1CH 7:5  Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
10550  1CH 7:11  Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.
10632  1CH 9:13  Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.
10750  1CH 12:26  Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100;
10752  1CH 12:28  mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700,
10759  1CH 12:35  Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo;
10899  1CH 18:4  Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
10930  1CH 19:18  Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo.
10944  1CH 21:5  Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.
10953  1CH 21:14  Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000.
11035  1CH 24:15  a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi,