Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   A    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

27  GEN 1:27  Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.
45  GEN 2:14  Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate.
50  GEN 2:19  Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.
51  GEN 2:20  Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza.
73  GEN 3:17  Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.
77  GEN 3:21  Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka.
79  GEN 3:23  Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera.
80  GEN 3:24  Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
81  GEN 4:1  Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.”
82  GEN 4:2  Kenaka anabereka mʼbale wake Abele. Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi.
84  GEN 4:4  Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake.
88  GEN 4:8  Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.
89  GEN 4:9  Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti,Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”
99  GEN 4:19  Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila.
100  GEN 4:20  Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto.
103  GEN 4:23  Lameki anawuza akazi akewo kuti,Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
105  GEN 4:25  Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”
107  GEN 5:1  Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.
108  GEN 5:2  Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
109  GEN 5:3  Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
110  GEN 5:4  Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
111  GEN 5:5  Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
113  GEN 5:7  Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
116  GEN 5:10  Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
119  GEN 5:13  Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
122  GEN 5:16  Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
125  GEN 5:19  Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
128  GEN 5:22  Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
136  GEN 5:30  Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
139  GEN 6:1  Anthu atayamba kuchuluka pa dziko lapansi ndi kubereka ana aakazi,
142  GEN 6:4  Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu.
188  GEN 8:4  ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.
211  GEN 9:5  Aliyense wopha munthu adzaphedwa, nyama iliyonse yopha munthu idzaphedwa, munthu aliyense wopha munthu mnzake, adzaphedwa.
212  GEN 9:6  Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.
224  GEN 9:18  Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani.
225  GEN 9:19  Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi.
229  GEN 9:23  Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.
231  GEN 9:25  anati, Atembereredwe Kanaani! Adzakhala kapolo wa pansi kwenikweni kwa abale ake.”
232  GEN 9:26  Anatinso, Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu.
235  GEN 9:29  Anamwalira ali ndi zaka 950.
236  GEN 10:1  Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
237  GEN 10:2  Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
238  GEN 10:3  Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.
239  GEN 10:4  Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
240  GEN 10:5  (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
241  GEN 10:6  Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.
242  GEN 10:7  Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
245  GEN 10:10  Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
246  GEN 10:11  Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
248  GEN 10:13  Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
249  GEN 10:14  Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
250  GEN 10:15  Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
251  GEN 10:16  Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
252  GEN 10:17  Ahivi, Aariki, Asini,
253  GEN 10:18  Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
254  GEN 10:19  mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
255  GEN 10:20  Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
257  GEN 10:22  Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
258  GEN 10:23  Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
259  GEN 10:24  Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
260  GEN 10:25  A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
261  GEN 10:26  Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
263  GEN 10:28  Obali, Abimaeli, Seba,
266  GEN 10:31  Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
267  GEN 10:32  Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
273  GEN 11:6  Yehova anati, Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
277  GEN 11:10  Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi.
278  GEN 11:11  Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
279  GEN 11:12  Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela.
280  GEN 11:13  Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
282  GEN 11:15  Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.