43 | GEN 2:12 | (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
237 | GEN 10:2 | Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi. |
238 | GEN 10:3 | Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima. |
254 | GEN 10:19 | mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. |
258 | GEN 10:23 | Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki. |
329 | GEN 13:10 | Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). |
338 | GEN 14:1 | Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu |
339 | GEN 14:2 | anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). |
345 | GEN 14:8 | Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo |
346 | GEN 14:9 | Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. |
347 | GEN 14:10 | Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri. |
348 | GEN 14:11 | Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo. |
445 | GEN 18:20 | Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Kulirira Gomora kwakula ndipo tchimo lawo lafika poyipa kwambiri |
482 | GEN 19:24 | Ndiye Yehova anathira sulufule wamoto wochokera kumwamba kwa Yehova pa Sodomu ndi Gomora. |
486 | GEN 19:28 | Anayangʼana kumunsi ku Sodomu, Gomora ndi ku dziko lonse la ku chigwa, ndipo anaona chiwutsi chikufuka mʼdzikolo ngati chikuchokera mʼngʼanjo. |
497 | GEN 20:1 | Abrahamu anachokako kumeneko napita ku Negevi ndipo anakakhala ku dziko la Gerari, limene lili pakati pa mzinda wa Kadesi ndi mzinda wa Suri. Anakhala ku Gerari kwa kanthawi, |
498 | GEN 20:2 | ndipo Abrahamu ankawawuza za Sara kuti, “Iyeyu ndi mlongo wanga.” Choncho Abimeleki, mfumu wa ku Gerari anamutenga Sara uja. |
572 | GEN 22:24 | Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka. |
694 | GEN 26:1 | Tsono kunagwa njala ina mʼdzikomo kuwonjezera pa ija ya poyamba ya nthawi ya Abrahamu ndipo Isake anapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. |
699 | GEN 26:6 | Choncho Isake anakhala ku Gerari. |
710 | GEN 26:17 | Choncho Isake anachokako kumeneko nakakhala ku chigwa cha Gerari kumene anakhazikikako. |
713 | GEN 26:20 | Koma abusa a ku Gerari anakangana ndi abusa a Isake nati, “Madziwa ndi athu.” Motero iye anachitcha chitsimecho Mkangano chifukwa anakangana naye. |
719 | GEN 26:26 | Abimeleki pamodzi ndi Ahuzati mlangizi wake ndi Fikolo mkulu wa ankhondo ake anabwera kwa Isake kuchokera ku Gerari. |
842 | GEN 30:11 | Pamenepo Leya anati, “Mwayi wangawo!” Choncho anamutcha Gadi. |
895 | GEN 31:21 | Choncho anathawa ndi zonse anali nazo. Ananyamuka nawoloka mtsinje wa Yufurate kupita cha ku Giliyadi, dziko la mapiri. |
897 | GEN 31:23 | Pomwepo anatengana ndi abale ake namulondola Yakobo kwa masiku asanu ndi awiri ndipo anakamupezera ku Giliyadi, dziko la mapiri. |
899 | GEN 31:25 | Pamene Labani amamupeza Yakobo, nʼkuti Yakobo atamanga matenti ake ku mapiri a dziko la Giliyadi. Nayenso Labani ndi abale ake anamanga matenti awo komweko. |
921 | GEN 31:47 | Labani anawutcha muluwo Yegara-sahaduta, ndipo Yakobo anawutcha Galeeda. |
922 | GEN 31:48 | Labani anati, “Mulu uwu ndi mboni pakati pa inu ndi ine lero.” Ndi chifukwa chake unatchedwa Galeeda. |
1038 | GEN 35:26 | Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa: Gadi ndi Aseri. Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu. |
1052 | GEN 36:11 | Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. |
1057 | GEN 36:16 | Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada. |
1109 | GEN 37:25 | Atakhala pansi kuti adye chakudya, anatukula maso naona gulu la Aismaeli akubwera kuchokera ku Giliyadi. Ngamira zawo zinanyamula zonunkhiritsa bwino zakudya zamitundumitundu, ndipo zimenezi ankapita nazo ku Igupto. |
1369 | GEN 45:10 | Ndipo inu, ana anu, zidzukulu zanu, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zanu ndi antchito anu amene muli nawo muzidzakhala mʼdziko la Goseni pafupi ndi ine. |
1398 | GEN 46:11 | Ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. |
1403 | GEN 46:16 | Ana aamuna a Gadi ndi awa: Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli. |
1408 | GEN 46:21 | Ana aamuna a Benjamini ndi awa: Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi. |
1411 | GEN 46:24 | Ana aamuna a Nafutali ndi awa: Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu. |
1415 | GEN 46:28 | Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni, |
1416 | GEN 46:29 | Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali. |
1421 | GEN 46:34 | Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.” |
1422 | GEN 47:1 | Yosefe anapita kukamuwuza Farao kuti, “Abambo anga, abale anga pamodzi ndi nkhosa, ngʼombe zawo, ndi antchito awo abwera kuchokera ku dziko la Kanaani ndipo tsopano ali ku Goseni.” |
1425 | GEN 47:4 | Ife tabwera kudzakhala kuno kwa kanthawi chifukwa njala yafika poopsa ku Kanaani motero kuti kulibe msipu wodyetsera ziweto. Ndiye bwana tiloleni kuti tikhale ku Goseni.” |
1427 | GEN 47:6 | Dziko lonse la Igupto lili mʼdzanja lako. Uwakhazike abambo ako ndi abale ako mʼmalo achonde kwambiri. Akhale ku Goseni. Ndipo ngati ukudziwapo ena mwa iwo amene ali akatswiri pa kuweta ziweto, uwapatse udindo woyangʼanira ziweto zanga.” |
1448 | GEN 47:27 | Tsono Aisraeli anakhazikika mʼdziko la Igupto ku chigawo cha Goseni. Kumeneko anapeza chuma ndipo anaberekana nachuluka kwambiri. |
1493 | GEN 49:19 | “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo, koma iye adzawathamangitsa. |
1515 | GEN 50:8 | Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni |
1517 | GEN 50:10 | Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. |
1518 | GEN 50:11 | Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu. |
1537 | EXO 1:4 | Dani, Nafutali; Gadi ndi Aseri. |
1577 | EXO 2:22 | Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.” |
1672 | EXO 6:16 | Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1673 | EXO 6:17 | Ana a Geresoni, mwa mafuko awo, anali Libini ndi Simei. |
1733 | EXO 8:18 | “Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino. |
1769 | EXO 9:26 | Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli. |
1864 | EXO 12:47 | Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi. |
1985 | EXO 17:1 | Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. |
2003 | EXO 18:3 | mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” |
2199 | EXO 25:3 | Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. |
2281 | EXO 27:8 | Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja. |
2537 | EXO 35:5 | Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; |
2641 | EXO 38:7 | Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. |
2658 | EXO 38:24 | Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika. |
2959 | LEV 9:5 | Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova. |
3463 | LEV 24:16 | Aliyense wonyoza dzina la Yehova, mlendo ngakhale mbadwa, aphedwe. Gulu lonse la anthu limuponye miyala. |
3615 | NUM 1:10 | Mwa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri; |
3616 | NUM 1:11 | Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini, |
3619 | NUM 1:14 | Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi, |
3629 | NUM 1:24 | Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
3630 | NUM 1:25 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650. |
3673 | NUM 2:14 | Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli. |
3679 | NUM 2:20 | Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri. |
3681 | NUM 2:22 | Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni. |
3710 | NUM 3:17 | Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. |
3711 | NUM 3:18 | Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simei. |
3714 | NUM 3:21 | Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. |
3861 | NUM 7:10 | Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo. |
3893 | NUM 7:42 | Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake. |
3905 | NUM 7:54 | Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Gamalieli mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa fuko Manase, anabweretsa chopereka chake. |
3910 | NUM 7:59 | ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Gamalieli mwana wa Pedazuri. |
3911 | NUM 7:60 | Pa tsiku lachisanu ndi chinayi Abidani mwana wa Gideoni mtsogoleri wa fuko la Benjamini, anabweretsa chopereka chake. |
3916 | NUM 7:65 | ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni. |
4009 | NUM 10:20 | ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. |
4012 | NUM 10:23 | Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase. |
4013 | NUM 10:24 | Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini. |
4086 | NUM 13:10 | kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi; |
4087 | NUM 13:11 | kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi; |
4088 | NUM 13:12 | kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali; |
4091 | NUM 13:15 | kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki. |
4111 | NUM 14:2 | Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno! |
4169 | NUM 15:15 | Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. |
4180 | NUM 15:26 | Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa. |
4189 | NUM 15:35 | Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” |
4334 | NUM 20:22 | Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. |
4380 | NUM 22:4 | Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo, |
4506 | NUM 26:15 | Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni; |