3 | GEN 1:3 | Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
6 | GEN 1:6 | Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” |
11 | GEN 1:11 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. |
24 | GEN 1:24 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
29 | GEN 1:29 | Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu. |
39 | GEN 2:8 | Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. |
43 | GEN 2:12 | (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
50 | GEN 2:19 | Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. |
51 | GEN 2:20 | Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. |
57 | GEN 3:1 | Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ” |
63 | GEN 3:7 | Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala. |
64 | GEN 3:8 | Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. |
67 | GEN 3:11 | Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?” |
68 | GEN 3:12 | Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.” |
72 | GEN 3:16 | Kwa mkaziyo Iye anati, “Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.” |
75 | GEN 3:19 | Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.” |
79 | GEN 3:23 | Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. |
81 | GEN 4:1 | Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” |
82 | GEN 4:2 | Kenaka anabereka mʼbale wake Abele. Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. |
83 | GEN 4:3 | Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. |
85 | GEN 4:5 | Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. |
86 | GEN 4:6 | Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? |
87 | GEN 4:7 | Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” |
88 | GEN 4:8 | Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha. |
89 | GEN 4:9 | Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” |
90 | GEN 4:10 | Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. |
93 | GEN 4:13 | Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. |
95 | GEN 4:15 | Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. |
96 | GEN 4:16 | Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni. |
97 | GEN 4:17 | Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. |
102 | GEN 4:22 | Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
104 | GEN 4:24 | Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.” |
105 | GEN 4:25 | Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” |
115 | GEN 5:9 | Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. |
116 | GEN 5:10 | Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
118 | GEN 5:12 | Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. |
119 | GEN 5:13 | Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
120 | GEN 5:14 | Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira. |
146 | GEN 6:8 | Koma Yehova anamukomera mtima Nowa. |
156 | GEN 6:18 | Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho. |
162 | GEN 7:2 | Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso. |
176 | GEN 7:16 | Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo. |
192 | GEN 8:8 | Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. |
193 | GEN 8:9 | Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. |
210 | GEN 9:4 | “Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda. |
224 | GEN 9:18 | Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. |
228 | GEN 9:22 | Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja. |
229 | GEN 9:23 | Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo. |
231 | GEN 9:25 | anati, “Atembereredwe Kanaani! Adzakhala kapolo wa pansi kwenikweni kwa abale ake.” |
232 | GEN 9:26 | Anatinso, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu. |
233 | GEN 9:27 | Mulungu akulitse dziko la Yafeti; Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu, ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.” |
239 | GEN 10:4 | Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. |
241 | GEN 10:6 | Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani. |
242 | GEN 10:7 | Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani. |
243 | GEN 10:8 | Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. |
245 | GEN 10:10 | Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. |
246 | GEN 10:11 | Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, |
247 | GEN 10:12 | ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala. |
250 | GEN 10:15 | Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; |
254 | GEN 10:19 | mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. |
271 | GEN 11:4 | Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.” |
272 | GEN 11:5 | Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. |
298 | GEN 11:31 | Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. |
304 | GEN 12:5 | Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. |
306 | GEN 12:7 | Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe. |
307 | GEN 12:8 | Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. |
308 | GEN 12:9 | Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi. |
309 | GEN 12:10 | Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri. |
316 | GEN 12:17 | Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. |
328 | GEN 13:9 | Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.” |
331 | GEN 13:12 | Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. |
333 | GEN 13:14 | Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. |
338 | GEN 14:1 | Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu |
341 | GEN 14:4 | Kwa zaka khumi ndi ziwiri anali pansi pa ulamuliro wa Kedorilaomere, koma mʼchaka cha khumi ndi chitatu anamuwukira. |
342 | GEN 14:5 | Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu |
344 | GEN 14:7 | Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara. |
346 | GEN 14:9 | Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. |
347 | GEN 14:10 | Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri. |
350 | GEN 14:13 | Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu. |
354 | GEN 14:17 | Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu). |
359 | GEN 14:22 | Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira |
363 | GEN 15:2 | Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko? |
369 | GEN 15:8 | Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?” |
370 | GEN 15:9 | Kotero Yehova anati kwa iye, “Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.” |
375 | GEN 15:14 | Koma ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo ndipo pambuyo pake iwo adzatulukamo ndi chuma chambiri. |
376 | GEN 15:15 | Komabe iweyo udzamwalira mu mtendere ndi kuyikidwa mʼmanda utakalamba bwino. |
383 | GEN 16:1 | Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; |
385 | GEN 16:3 | Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi. |
396 | GEN 16:14 | Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi. |