1 | GEN 1:1 | Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
3 | GEN 1:3 | Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
6 | GEN 1:6 | Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” |
14 | GEN 1:14 | Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; |
33 | GEN 2:2 | Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. |
36 | GEN 2:5 | zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka, |
40 | GEN 2:9 | Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa. |
42 | GEN 2:11 | Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
61 | GEN 3:5 | “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.” |
62 | GEN 3:6 | Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. |
70 | GEN 3:14 | Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. |
83 | GEN 4:3 | Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. |
95 | GEN 4:15 | Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. |
106 | GEN 4:26 | Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova. |
107 | GEN 5:1 | Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. |
109 | GEN 5:3 | Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
112 | GEN 5:6 | Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. |
115 | GEN 5:9 | Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. |
118 | GEN 5:12 | Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. |
121 | GEN 5:15 | Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. |
124 | GEN 5:18 | Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. |
127 | GEN 5:21 | Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. |
131 | GEN 5:25 | Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. |
134 | GEN 5:28 | Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. |
138 | GEN 5:32 | Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. |
143 | GEN 6:5 | Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha, |
162 | GEN 7:2 | Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso. |
164 | GEN 7:4 | Pakapita masiku asanu ndi awiri ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku ndipo ndidzawononga cha moyo chilichonse chimene ndinachipanga pa dziko lapansi.” |
166 | GEN 7:6 | Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600. |
170 | GEN 7:10 | Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi. |
171 | GEN 7:11 | Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. |
187 | GEN 8:3 | Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, |
190 | GEN 8:6 | Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo |
195 | GEN 8:11 | Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. |
197 | GEN 8:13 | Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
198 | GEN 8:14 | Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu. |
204 | GEN 8:20 | Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza. |
217 | GEN 9:11 | Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.” |
241 | GEN 10:6 | Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani. |
253 | GEN 10:18 | Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, |
260 | GEN 10:25 | A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. |
269 | GEN 11:2 | Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako. |
276 | GEN 11:9 | Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi. |
277 | GEN 11:10 | Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. |
279 | GEN 11:12 | Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. |
281 | GEN 11:14 | Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. |
283 | GEN 11:16 | Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. |
284 | GEN 11:17 | Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
285 | GEN 11:18 | Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. |
286 | GEN 11:19 | Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
287 | GEN 11:20 | Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. |
289 | GEN 11:22 | Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. |
291 | GEN 11:24 | Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. |
293 | GEN 11:26 | Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. |
298 | GEN 11:31 | Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. |
303 | GEN 12:4 | Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. |
313 | GEN 12:14 | Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. |
314 | GEN 12:15 | Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao. |
327 | GEN 13:8 | Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. |
338 | GEN 14:1 | Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu |
343 | GEN 14:6 | amene ankakhala ku Ahori, ku dziko la mapiri la Seiri mpaka ku Eli Parani kufupi ndi chipululu. |
352 | GEN 14:15 | Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko. |
372 | GEN 15:11 | Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa. |
373 | GEN 15:12 | Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba. |
377 | GEN 15:16 | Patapita mibado inayi, adzukulu ako adzabwereranso kuno popeza tchimo la Aamori silinafike pachimake kuti alangidwe.” |
379 | GEN 15:18 | Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. |
386 | GEN 16:4 | Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba. Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai. |
387 | GEN 16:5 | Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.” |
398 | GEN 16:16 | Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86. |
399 | GEN 17:1 | Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. |
401 | GEN 17:3 | Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, |
402 | GEN 17:4 | “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. |
405 | GEN 17:7 | Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. |
439 | GEN 18:14 | Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.” |
444 | GEN 18:19 | Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye.” |
455 | GEN 18:30 | Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?” Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.” |
457 | GEN 18:32 | Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.” |
481 | GEN 19:23 | Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka. |
514 | GEN 20:18 | Paja Yehova nʼkuti atatseka akazi onse a mʼbanja la Abimeleki kuti asabereke ana chifukwa cha Sara, mkazi wa Abrahamu. |
535 | GEN 21:21 | Akukhala ku chipululu cha Parani, mayi ake anamupezera mkazi wochokera ku Igupto. |
536 | GEN 21:22 | Pa nthawiyo, Abimeleki ndi Fikolo wamkulu wankhondo wake anati kwa Abrahamu, “Mulungu ali nawe pa chilichonse umachita. |
552 | GEN 22:4 | Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. |
554 | GEN 22:6 | Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, |
562 | GEN 22:14 | Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.” |
568 | GEN 22:20 | Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. |
570 | GEN 22:22 | Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” |
578 | GEN 23:6 | “Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.” |
582 | GEN 23:10 | Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu |
654 | GEN 24:62 | Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. |
679 | GEN 25:20 | ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu. |
683 | GEN 25:24 | Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. |
696 | GEN 26:3 | Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako. |
718 | GEN 26:25 | Isake anamanga guwa lansembe pamenepo ndipo anapembedza Yehova. Pomwepo anamanga tenti yake, ndipo antchito ake anakumba chitsime. |
726 | GEN 26:33 | Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero. |
727 | GEN 26:34 | Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti. |
737 | GEN 27:9 | Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera. |
749 | GEN 27:21 | Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.” |
766 | GEN 27:38 | Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa. |