Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   S    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

49  GEN 2:18  Ndipo Yehova Mulungu anati,Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.”
89  GEN 4:9  Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti,Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”
95  GEN 4:15  Koma Yehova anamuwuza kuti,Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe.
105  GEN 4:25  Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”
106  GEN 4:26  Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.
109  GEN 5:3  Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
110  GEN 5:4  Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
112  GEN 5:6  Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
113  GEN 5:7  Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
114  GEN 5:8  Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
138  GEN 5:32  Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
141  GEN 6:3  Tsono Yehova anati,Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”
148  GEN 6:10  Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.
173  GEN 7:13  Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo.
205  GEN 8:21  Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake:Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.
224  GEN 9:18  Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani.
229  GEN 9:23  Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.
232  GEN 9:26  Anatinso, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu.
233  GEN 9:27  Mulungu akulitse dziko la Yafeti; Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu, ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.”
236  GEN 10:1  Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
242  GEN 10:7  Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
245  GEN 10:10  Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
250  GEN 10:15  Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
254  GEN 10:19  mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
256  GEN 10:21  Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
257  GEN 10:22  Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
259  GEN 10:24  Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
261  GEN 10:26  Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
263  GEN 10:28  Obali, Abimaeli, Seba,
265  GEN 10:30  Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
266  GEN 10:31  Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
269  GEN 11:2  Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
277  GEN 11:10  Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi.
278  GEN 11:11  Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
279  GEN 11:12  Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela.
280  GEN 11:13  Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
281  GEN 11:14  Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi.
282  GEN 11:15  Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
287  GEN 11:20  Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi.
288  GEN 11:21  Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
289  GEN 11:22  Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori.
290  GEN 11:23  Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
296  GEN 11:29  Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani.
297  GEN 11:30  Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
298  GEN 11:31  Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
300  GEN 12:1  Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
304  GEN 12:5  Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.
305  GEN 12:6  Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo.
310  GEN 12:11  Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri.
313  GEN 12:14  Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi.
315  GEN 12:16  Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.
316  GEN 12:17  Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu.
329  GEN 13:10  Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora).
331  GEN 13:12  Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu.
332  GEN 13:13  Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri.
338  GEN 14:1  Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu
339  GEN 14:2  anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari).
340  GEN 14:3  Mafumu onse anathiridwa nkhondowa anagwirizana pamodzi kupita ku Chigwa cha Sidimu (Nyanja ya Mchere).
342  GEN 14:5  Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu
343  GEN 14:6  amene ankakhala ku Ahori, ku dziko la mapiri la Seiri mpaka ku Eli Parani kufupi ndi chipululu.
345  GEN 14:8  Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo
346  GEN 14:9  Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu.
347  GEN 14:10  Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.
348  GEN 14:11  Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo.
349  GEN 14:12  Anatenganso Loti, mwana wa mʼbale wake wa Abramu pamodzi ndi katundu wake popeza ankakhala mu Sodomu.
354  GEN 14:17  Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).
355  GEN 14:18  Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba,
358  GEN 14:21  Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”
359  GEN 14:22  Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira
361  GEN 14:24  Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
383  GEN 16:1  Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara;
384  GEN 16:2  ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.” Abramu anamvera Sarai.
385  GEN 16:3  Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi.
386  GEN 16:4  Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba. Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai.
387  GEN 16:5  Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
388  GEN 16:6  Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
389  GEN 16:7  Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri.
390  GEN 16:8  Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
403  GEN 17:5  Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
413  GEN 17:15  Mulungu anatinso kwa Abrahamu,Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara.
415  GEN 17:17  Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?”
417  GEN 17:19  Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.
419  GEN 17:21  Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.”
431  GEN 18:6  Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.”
434  GEN 18:9  Anthuwo anafunsa Abrahamu kuti, “Mkazi wako Sara ali kuti?” Iye anati, “Ali mu tentimu.”
435  GEN 18:10  Tsono mmodzi mwa iwo anati, “Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi.
436  GEN 18:11  Abrahamu ndi Sara anali okalamba kale ndipo anali ndi zaka zambiri. Sara nʼkuti atapyola kale pa msinkhu oti nʼkubereka.
438  GEN 18:13  Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’
439  GEN 18:14  Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.”
440  GEN 18:15  Koma Sara ndi mantha ananama nati,Sindinaseke.” Koma Iye anati, “Inde iwe unaseka.”