26 | GEN 1:26 | Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” |
38 | GEN 2:7 | Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
52 | GEN 2:21 | Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
58 | GEN 3:2 | Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, |
69 | GEN 3:13 | Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.” |
78 | GEN 3:22 | Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” |
88 | GEN 4:8 | Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha. |
90 | GEN 4:10 | Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. |
102 | GEN 4:22 | Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
141 | GEN 6:3 | Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” |
152 | GEN 6:14 | Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. |
185 | GEN 8:1 | Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. |
186 | GEN 8:2 | Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. |
199 | GEN 8:15 | Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, |
201 | GEN 8:17 | Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.” |
209 | GEN 9:3 | Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse. |
215 | GEN 9:9 | “Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, |
227 | GEN 9:21 | Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche. |
237 | GEN 10:2 | Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi. |
238 | GEN 10:3 | Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima. |
239 | GEN 10:4 | Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. |
270 | GEN 11:3 | Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. |
271 | GEN 11:4 | Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.” |
274 | GEN 11:7 | Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.” |
291 | GEN 11:24 | Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. |
292 | GEN 11:25 | Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
293 | GEN 11:26 | Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. |
294 | GEN 11:27 | Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. |
295 | GEN 11:28 | Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. |
298 | GEN 11:31 | Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. |
299 | GEN 11:32 | Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205. |
300 | GEN 12:1 | Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza. |
311 | GEN 12:12 | Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. |
312 | GEN 12:13 | Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.” |
327 | GEN 13:8 | Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. |
328 | GEN 13:9 | Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.” |
332 | GEN 13:13 | Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri. |
338 | GEN 14:1 | Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu |
344 | GEN 14:7 | Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara. |
345 | GEN 14:8 | Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo |
346 | GEN 14:9 | Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. |
350 | GEN 14:13 | Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu. |
366 | GEN 15:5 | Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.” |
374 | GEN 15:13 | Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. |
383 | GEN 16:1 | Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; |
385 | GEN 16:3 | Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi. |
388 | GEN 16:6 | Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa. |
397 | GEN 16:15 | Tsono Hagara anamuberekera Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anamutcha mwanayo Ismaeli. |
421 | GEN 17:23 | Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira. |
427 | GEN 18:2 | Tsono Abrahamu atakweza maso ake patali anangoona anthu atatu atayima cha potero. Atawaona, ananyamuka mofulumira kuti awachingamire. Atafika anaweramitsa mutu pansi mwa ulemu nati, |
430 | GEN 18:5 | Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.” Ndipo iwo anamuyankha nati, “Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.” |
431 | GEN 18:6 | Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.” |
433 | GEN 18:8 | Tsono Abrahamu anatenga chambiko, mkaka ndi mwana wangʼombe wokonzedwa uja nazipereka kwa anthu aja. Alendowo akudya, Abrahamu ankawayangʼana atayimirira pansi pa mtengo. |
435 | GEN 18:10 | Tsono mmodzi mwa iwo anati, “Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi. |
442 | GEN 18:17 | Tsono Yehova anati mu mtima mwake, “Kodi ndingamubisire Abrahamu chimene ndikuti ndichite posachedwa? |
452 | GEN 18:27 | Ndipo Abrahamu anayankhulanso nati, “Tsono poti ndalimba mtima kuyankhula ndi Ambuye, ngakhale kuti ndine fumbi ndi phulusa chabe, |
456 | GEN 18:31 | Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?” Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.” |
466 | GEN 19:8 | Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.” |
467 | GEN 19:9 | Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. |
475 | GEN 19:17 | Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!” |
477 | GEN 19:19 | Taonani, Inu mwachitira mtumiki wanu chifundo, ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu pondipulumutsa. Sindingathawire ku mapiri chifukwa chiwonongekochi chikhoza kundipeza ndisanafike ku mapiriko ndipo ndingafe. |
489 | GEN 19:31 | Tsiku lina mwana wake wamkazi wamkulu anawuza mngʼono wake kuti, “Abambo athu ndi wokalamba ndipo palibe mwamuna aliyense pano woti atikwatire ndi kubereka ana monga mwa chikhalidwe cha pa dziko lonse lapansi. |
490 | GEN 19:32 | Tiye tiwamwetse vinyo ndipo tigone nawo. Tikatero mtundu wathu udzakhalapobe.” |
492 | GEN 19:34 | Tsiku linali mwana wamkazi wamkulu uja anati kwa mngʼono wake, “Usiku wathawu ine ndinagona ndi abambo anga. Tiye tiwaledzeretsenso vinyo usiku uno ndipo iwe upite ndi kugona nawo ndipo mtundu wathu udzakhalapobe.” |
502 | GEN 20:6 | Tsono kumaloto komweko Mulungu anati kwa iye, “Inde ndikudziwa kuti wachita izi moona mtima, ndipo Ine sindinafune kuti undichimwire. Nʼchifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze. |
503 | GEN 20:7 | Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.” |
508 | GEN 20:12 | Komabe kunena zoona, iyeyu ndi mlongo wangadi, mwana wamkazi wa abambo anga ngakhale kuti si ife a mayi mmodzi. Tsono akhoza kukhala mkazi wanga. |
510 | GEN 20:14 | Tsono Abimeleki anapereka nkhosa, ngʼombe ndi antchito aamuna ndi aakazi kwa Abrahamu. Ndipo anamubwezeranso Abrahamu Sara, mkazi wake. |
511 | GEN 20:15 | Tsono Abimeleki anati kwa Abrahamu, “Dziko langa ndi limene ukulionali; ukhale paliponse pamene ufuna.” |
513 | GEN 20:17 | Tsono Abrahamu anapemphera kwa Mulungu ndipo Mulunguyo anachiritsa Abimeleki, mkazi wake pamodzi ndi adzakazi ake kuti athenso kubereka ana. |
522 | GEN 21:8 | Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu. |
537 | GEN 21:23 | Tsopano undilumbirire ine pano pamaso pa Mulungu kuti sudzachita mwa chinyengo ndi ine kapena ana anga kapena zidzukulu zanga. Undionetse ine pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo ngati mlendo, kukoma mtima kokhala ngati kumene ndinakuonetsa ine.” |
550 | GEN 22:2 | Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.” |
572 | GEN 22:24 | Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka. |
578 | GEN 23:6 | “Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.” |
579 | GEN 23:7 | Tsono Abrahamu anayimirira naweramira anthu a dziko la Hiti aja |
593 | GEN 24:1 | Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita. |
594 | GEN 24:2 | Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. |
602 | GEN 24:10 | Tsono wantchito uja anatengapo ngamira khumi mwa ngamira za mbuye wake pamodzi ndi zinthu zabwino za mitundumitundu. Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda wa Nahori, mʼdziko la Mesopotamiya. |
605 | GEN 24:13 | Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi. |
606 | GEN 24:14 | Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. |
621 | GEN 24:29 | Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani. |
623 | GEN 24:31 | Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.” |
628 | GEN 24:36 | Sara, mkazi wa mbuye wanga anamubalira iye mwana wamwamuna ngakhale kuti Sarayo anali wokalamba. Tsono mbuye wanga wamupatsa mwanayo chuma chonse. |
629 | GEN 24:37 | Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani, |
634 | GEN 24:42 | “Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu, |
639 | GEN 24:47 | “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake, |
641 | GEN 24:49 | Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.” |
646 | GEN 24:54 | Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko. Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.” |
655 | GEN 24:63 | Tsiku lina chakumadzulo, Isake anatuluka kukayendayenda ku munda, ndipo atakweza maso anaona ngamira zikubwera. |