1585 | EXO 3:5 | Mulungu anati, “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.” |
2441 | EXO 32:2 | Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” |
4090 | NUM 13:14 | kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi; |
5045 | DEU 4:39 | Vomerezani lero ndipo dziwani mu mtima mwanu kuti Yehova ndiye Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Palibenso wina. |
5793 | DEU 32:33 | Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka, ululu woopsa wa mphiri. |
5951 | JOS 5:15 | Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo. |
12293 | EZR 10:36 | Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, |
12715 | EST 1:9 | Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero. |
12717 | EST 1:11 | kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. |
12718 | EST 1:12 | Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima. |
12721 | EST 1:15 | Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?” |
12722 | EST 1:16 | Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. |
12723 | EST 1:17 | Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ |
12725 | EST 1:19 | “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. |
12729 | EST 2:1 | Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. |
12732 | EST 2:4 | Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo. |
12745 | EST 2:17 | Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. |
12847 | EST 9:9 | Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, |
17025 | PRO 20:1 | Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola; aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru. |
18172 | ISA 24:7 | Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota; onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni. |
18340 | ISA 32:11 | Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu; ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu. Vulani zovala zanu, ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu. |
18752 | ISA 51:9 | Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe, Inu Yehova; dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana, monga nthawi ya mibado yakale. Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe, amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija? |
18767 | ISA 52:1 | Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni, vala zilimbe. Vala zovala zako zokongola, iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika. Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa sadzalowanso pa zipata zako. |
19084 | JER 3:13 | Ungovomera kulakwa kwako kuti unawukira Yehova Mulungu wako. Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndiponso kuti sunandimvere,’ ” akutero Yehova. |
20199 | JER 49:3 | “Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika! Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba! Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu; thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga, chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake. |
21039 | EZK 21:31 | Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. |
26167 | JHN 2:3 | Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.” |
27218 | ACT 7:33 | “Ndipo Ambuye anati kwa Mose, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika. |
27414 | ACT 12:8 | Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” |
29415 | EPH 6:11 | Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. |
29419 | EPH 6:15 | Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. |
29421 | EPH 6:17 | Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. |
30766 | REV 1:1 | Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane, |