Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   a    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

1  GEN 1:1  Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.
2  GEN 1:2  Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
3  GEN 1:3  Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.
4  GEN 1:4  Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.
5  GEN 1:5  Mulungu anatcha kuwalako “usanandipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
6  GEN 1:6  Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
7  GEN 1:7  Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
8  GEN 1:8  Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
9  GEN 1:9  Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
10  GEN 1:10  Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
11  GEN 1:11  Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
12  GEN 1:12  Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.