26 | GEN 1:26 | Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” |
27 | GEN 1:27 | Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi. |
33 | GEN 2:2 | Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. |
34 | GEN 2:3 | Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
48 | GEN 2:17 | koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.” |
52 | GEN 2:21 | Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
54 | GEN 2:23 | Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.” |
55 | GEN 2:24 | Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi. |
59 | GEN 3:3 | koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ” |
60 | GEN 3:4 | “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. |
66 | GEN 3:10 | Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.” |
67 | GEN 3:11 | Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?” |
70 | GEN 3:14 | Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. |
73 | GEN 3:17 | Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako. |
75 | GEN 3:19 | Kuti upeze chakudya udzayenera kukhetsa thukuta, mpaka utabwerera ku nthaka pakuti unachokera kumeneko; pakuti ndiwe fumbi ku fumbi komweko udzabwerera.” |
76 | GEN 3:20 | Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo. |
78 | GEN 3:22 | Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” |
84 | GEN 4:4 | Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. |
86 | GEN 4:6 | Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? |
87 | GEN 4:7 | Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” |
89 | GEN 4:9 | Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” |
103 | GEN 4:23 | Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. |
107 | GEN 5:1 | Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. |
109 | GEN 5:3 | Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
130 | GEN 5:24 | Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga. |
138 | GEN 5:32 | Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. |
142 | GEN 6:4 | Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu. |
145 | GEN 6:7 | Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.” |
148 | GEN 6:10 | Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. |
150 | GEN 6:12 | Mulungu atayangʼana, anaona kuti dziko layipadi chifukwa cha makhalidwe oyipa a anthu onse pa dziko lapansi. |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
155 | GEN 6:17 | Ndidzagwetsa mvula ya chigumula pa dziko lapansi kuti ndiwononge zamoyo zonse za pansi pa thambo ndipo chilichonse cha pa dziko lapansi chidzafa. |
161 | GEN 7:1 | Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu. |
171 | GEN 7:11 | Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. |
173 | GEN 7:13 | Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo. |
178 | GEN 7:18 | Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo. |
180 | GEN 7:20 | Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri. |
181 | GEN 7:21 | Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu. |
182 | GEN 7:22 | Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa. |
193 | GEN 8:9 | Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. |
197 | GEN 8:13 | Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
205 | GEN 8:21 | Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. |
212 | GEN 9:6 | “Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. |
224 | GEN 9:18 | Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. |
229 | GEN 9:23 | Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo. |
233 | GEN 9:27 | Mulungu akulitse dziko la Yafeti; Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu, ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.” |
236 | GEN 10:1 | Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula. |
237 | GEN 10:2 | Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi. |
238 | GEN 10:3 | Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima. |
240 | GEN 10:5 | (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake). |
244 | GEN 10:9 | Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” |
245 | GEN 10:10 | Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. |
248 | GEN 10:13 | Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, |
249 | GEN 10:14 | Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti). |
253 | GEN 10:18 | Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, |
255 | GEN 10:20 | Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo. |
256 | GEN 10:21 | Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi. |
260 | GEN 10:25 | A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. |
261 | GEN 10:26 | Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, |
264 | GEN 10:29 | Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani. |
265 | GEN 10:30 | Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa. |
266 | GEN 10:31 | Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo. |
267 | GEN 10:32 | Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija. |
271 | GEN 11:4 | Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.” |
273 | GEN 11:6 | Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. |
276 | GEN 11:9 | Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi. |
297 | GEN 11:30 | Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka. |
298 | GEN 11:31 | Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. |
302 | GEN 12:3 | Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.” |
304 | GEN 12:5 | Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. |
305 | GEN 12:6 | Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. |
312 | GEN 12:13 | Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.” |
313 | GEN 12:14 | Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. |
315 | GEN 12:16 | Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira. |
316 | GEN 12:17 | Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. |
317 | GEN 12:18 | Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? |
318 | GEN 12:19 | Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” |
322 | GEN 13:3 | Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, |
327 | GEN 13:8 | Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. |
331 | GEN 13:12 | Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. |
335 | GEN 13:16 | Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako. |
336 | GEN 13:17 | Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.” |
337 | GEN 13:18 | Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe. |