Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   j    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

2  GEN 1:2  Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
7  GEN 1:7  Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
8  GEN 1:8  Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
10  GEN 1:10  Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
21  GEN 1:21  Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
22  GEN 1:22  Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”
26  GEN 1:26  Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
28  GEN 1:28  Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
35  GEN 2:4  Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,
39  GEN 2:8  Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja.
40  GEN 2:9  Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa.
41  GEN 2:10  Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi.
42  GEN 2:11  Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide.
44  GEN 2:13  Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi.
45  GEN 2:14  Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate.
46  GEN 2:15  Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira.
47  GEN 2:16  Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu;
50  GEN 2:19  Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.
51  GEN 2:20  Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza.
52  GEN 2:21  Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu.
53  GEN 2:22  Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.
54  GEN 2:23  Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”
56  GEN 2:25  Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.
57  GEN 3:1  Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
58  GEN 3:2  Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu,
60  GEN 3:4  “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo.
64  GEN 3:8  Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo.
65  GEN 3:9  Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”
68  GEN 3:12  Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”
69  GEN 3:13  Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
70  GEN 3:14  Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.
76  GEN 3:20  Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.
78  GEN 3:22  Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.”
80  GEN 3:24  Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
86  GEN 4:6  Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa?
87  GEN 4:7  Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”
142  GEN 6:4  Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu.
152  GEN 6:14  Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja.
154  GEN 6:16  Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba.
161  GEN 7:1  Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.
167  GEN 7:7  Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula.
173  GEN 7:13  Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo.
175  GEN 7:15  Nowa analowa mu chombo muja pamodzi ndi zamoyo zonse.
177  GEN 7:17  Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko.
188  GEN 8:4  ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.
193  GEN 8:9  Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali.
194  GEN 8:10  Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja.
196  GEN 8:12  Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.
197  GEN 8:13  Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma.
206  GEN 8:22  “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.”
208  GEN 9:2  Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire.
213  GEN 9:7  Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.”
217  GEN 9:11  Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”
224  GEN 9:18  Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani.
228  GEN 9:22  Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja.
230  GEN 9:24  Nowa atadzuka, kuledzera kutatha, ndikudziwa zimene mwana wake wamngʼono wamwamuna uja anamuchitira,
240  GEN 10:5  (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
244  GEN 10:9  Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
267  GEN 10:32  Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.
270  GEN 11:3  Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
271  GEN 11:4  Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
272  GEN 11:5  Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga.
275  GEN 11:8  Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo.
300  GEN 12:1  Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
309  GEN 12:10  Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri.
313  GEN 12:14  Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi.
316  GEN 12:17  Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu.
322  GEN 13:3  Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba,
328  GEN 13:9  Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.”
329  GEN 13:10  Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora).
337  GEN 13:18  Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.
340  GEN 14:3  Mafumu onse anathiridwa nkhondowa anagwirizana pamodzi kupita ku Chigwa cha Sidimu (Nyanja ya Mchere).
342  GEN 14:5  Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu
344  GEN 14:7  Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara.
347  GEN 14:10  Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.
348  GEN 14:11  Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo.
351  GEN 14:14  Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani.
352  GEN 14:15  Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko.
354  GEN 14:17  Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).
357  GEN 14:20  Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.” Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.
359  GEN 14:22  Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira
362  GEN 15:1  Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: “Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.”
366  GEN 15:5  Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
369  GEN 15:8  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”
370  GEN 15:9  Kotero Yehova anati kwa iye, “Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.”
371  GEN 15:10  Abramu anabweretsadi zonsezi nadula chilichonse pakati nʼkuzindandalika, chidutswa chilichonse kuyangʼanana ndi chinzake; koma njiwa ndi nkhunda sanazidule pakati.
372  GEN 15:11  Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa.