90 | GEN 4:10 | Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. |
231 | GEN 9:25 | anati, “Atembereredwe Kanaani! Adzakhala kapolo wa pansi kwenikweni kwa abale ake.” |
232 | GEN 9:26 | Anatinso, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu. |
467 | GEN 19:9 | Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. |
475 | GEN 19:17 | Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!” |
476 | GEN 19:18 | Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero! |
689 | GEN 25:30 | Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu). |
702 | GEN 26:9 | Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.” |
844 | GEN 30:13 | Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri. |
1114 | GEN 37:30 | nabwerera kwa abale ake nati, “Mnyamata uja mulibemo! Nanga ndilowere kuti ine tsopano?” |
1117 | GEN 37:33 | Iye anawuzindikira ndipo anati, “Ndi mkanjo wa mwana wanga umenewu! Nyama yakuthengo yolusa yamudya. Mosakayika, mwana wanga Yosefe wakhadzulidwa.” |
1262 | GEN 42:9 | Pamenepo anakumbukira maloto aja amene analota za iwo ndipo anati, “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muone pamene palibe chitetezo.” |
1275 | GEN 42:22 | Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.” |
1332 | GEN 44:7 | Koma iwo anati kwa iye, “Kodi mbuye wanga mukuneneranji zimenezi? Sizingatheke ndi pangʼono pomwe kuti antchito anufe nʼkuchita zoterozo ayi! |
1342 | GEN 44:17 | Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.” |
1359 | GEN 44:34 | Ndingabwerere bwanji kwa abambo anga ngati sindingapite ndi mnyamatayu? Ayi! Sindifuna kukaona tsoka limene lingakagwere abambo anga.” |
1362 | GEN 45:3 | Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndine Yosefe! Kodi abambo anga akanali ndi moyo?” Koma abale ake sanathe kumuyankha chifukwa anali ndi mantha kwambiri pamaso pake. |
1363 | GEN 45:4 | Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, “Senderani pafupi nane.” Atasendera iye anati, “Ine ndine mʼbale wanu Yosefe amene munamugulitsa ku Igupto! |
1385 | GEN 45:26 | Iwo anawuza abambo awo kuti, “Yosefe akanali ndi moyo! Ndiponsotu, ndiye akulamulira dziko la Igupto.” Yakobo anangoti kakasi osankhulupirira. |
1481 | GEN 49:7 | Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli. |
1650 | EXO 5:17 | Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ |
1788 | EXO 10:10 | Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa. |
1789 | EXO 10:11 | Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao. |
1806 | EXO 10:28 | Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.” |
1815 | EXO 11:8 | Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri. |
1848 | EXO 12:31 | Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha. |
1915 | EXO 14:25 | Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.” |
1951 | EXO 16:3 | kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!” |
2470 | EXO 32:31 | Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide. |
4024 | NUM 10:35 | Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu. |
4029 | NUM 11:4 | Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya! |
4043 | NUM 11:18 | “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. |
4111 | NUM 14:2 | Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno! |
4122 | NUM 14:13 | Mose anati kwa Yehova, “Aigupto adzamva zimenezi! Mwa mphamvu yanu munawatulutsa anthu amenewa pakati pawo. |
4150 | NUM 14:41 | Koma Mose anati, “Chifukwa chiyani simukumvera lamulo la Yehova? Zimenezi sizitheka! |
4203 | NUM 16:8 | Mose anawuzanso Kora kuti, “Inu Alevi, tsopano tamverani! |
4221 | NUM 16:26 | Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.” |
4257 | NUM 17:27 | Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika! |
4315 | NUM 20:3 | Anakangana ndi Mose kuti, “Kunali bwino ifenso tikanangofa pamene abale athu anafa pamaso pa Yehova! |
4358 | NUM 21:17 | Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi: “Tulutsa madzi, chitsime iwe! Chiyimbireni nyimbo, |
4370 | NUM 21:29 | Tsoka kwa iwe Mowabu! Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi! Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa ndipo ana ake aakazi ngati akapolo, akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori. |
4442 | NUM 23:25 | Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa! |
4452 | NUM 24:5 | “Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo, misasa yako, iwe Israeli! |
4458 | NUM 24:11 | Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.” |
4905 | DEU 1:11 | Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera! |
5161 | DEU 9:2 | Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?” |
5172 | DEU 9:13 | Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi! |
5568 | DEU 25:19 | Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi! |
5596 | DEU 27:9 | Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. |
5757 | DEU 31:27 | Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira! |
5763 | DEU 32:3 | Ndidzalalikira dzina la Yehova. Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu! |
5789 | DEU 32:29 | Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izi ndi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani! |
5798 | DEU 32:38 | milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo ndi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?” Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni! Ibwere kuti idzakutetezenitu! |
5799 | DEU 32:39 | “Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo! Palibe mulungu wina koma Ine ndekha. Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo, ndavulaza ndipo ndidzachiritsa, ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga. |
5832 | DEU 33:20 | Za fuko la Gadi anati: “Wodala amene amakulitsa malire a Gadi! Gadi amakhala kumeneko ngati mkango, kukhadzula mkono kapena mutu. |
5841 | DEU 33:29 | Iwe Israeli, ndiwe wodala! Wofanana nanu ndani anthu opulumutsidwa ndi Yehova? Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu ndi lupanga lanu la ulemerero. Adani ako adzakugonjera, ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.” |
5958 | JOS 6:7 | Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.” |
5967 | JOS 6:16 | Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu! |
5985 | JOS 7:7 | Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani! |
6072 | JOS 10:6 | Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.” |
6085 | JOS 10:19 | Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.” |
6444 | JOS 22:16 | “Gulu lonse likukufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwachita chinthu chonyansa chotere potsutsana ndi Mulungu wa Israeli? Nʼchifukwa chiyani mwapatuka ndi kuleka kutsata Yehova podzimangira nokha guwa lansembe? Mwapandukiratu Yehova! |
6450 | JOS 22:22 | “Wamphamvu uja, Mulungu ndiye Yehova! Wamphamvu uja Mulungu ndiye Yehova. Iyeyu ndiye akudziwa chifukwa chiyani tinachita zimenezi. Tikufunanso kuti inu mudziwe. Ngati tinachita izi mopandukira ndiponso moonetsa kusakhulupirira Yehova, lero lomwe lino musatisiye ndi moyo. |
6466 | JOS 23:4 | Tsono onani! Mitundu ya anthu otsalawa ndayipereka kwa mafuko anu pamodzi ndi mitundu ya anthu ya pakati pa Yorodani ndi Nyanja Yayikulu ya kumadzulo imene ndinayigonjetsa. |
6494 | JOS 24:16 | Ndipo anthu anayankha, “Sizingatheke kuti timusiye Yehova ndi kutumikira milungu ina! |
6628 | JDG 5:3 | “Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu! Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova, Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma. |
6634 | JDG 5:9 | Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli, uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu. Tamandani Yehova! |
6637 | JDG 5:12 | Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera; tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Iwe Baraki! nyamuka Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’ |
6646 | JDG 5:21 | Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola. Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika! |
6656 | JDG 5:31 | “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi. |
6678 | JDG 6:22 | Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!” |
6679 | JDG 6:23 | Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.” |
6687 | JDG 6:31 | Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” |
6775 | JDG 9:19 | Tsono ngati mukuti zimene mwachitira Yeru-Baala ndi banja lake mwazichita moona mtima ndiponso mokhulupirika, ndiye mukondwere ndi Abimeleki, nayenso akondwere nanu! |
6784 | JDG 9:28 | Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? |
6866 | JDG 11:35 | Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.” |
7307 | 1SA 4:8 | Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu. |
7308 | 1SA 4:9 | Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” |
7324 | 1SA 5:3 | Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. |
7478 | 1SA 12:16 | “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! |
7555 | 1SA 14:45 | Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe. |
7575 | 1SA 15:13 | Samueli atamupeza Sauli, Sauliyo anati kwa Samueli, “Yehova akudalitseni! Ndachita zonse zimene Yehova analamula.” |
7578 | 1SA 15:16 | Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.” Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.” |
7630 | 1SA 17:10 | Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” |
7734 | 1SA 20:2 | Yonatani anayankha kuti, “Sizitheka! Iwe sufa ayi! Taona abambo anga sachita chinthu chilichonse chachikulu kapena chachingʼono wosandiwuza ine. Tsopano abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Sichoncho ayi.” |
7744 | 1SA 20:12 | Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe. |
7762 | 1SA 20:30 | Sauli anamupsera mtima Yonatani ndipo namuwuza kuti, “Iwe mwana wobadwa mwa mkazi wamakhalidwe oyipa ndi wowukira! Kodi ukuyesa kuti ine sindikudziwa kuti umagwirizana ndi mwana wa Yese, amene akufuna kukuchititsa manyazi iwe ndi amayi ako? |
7789 | 1SA 21:15 | Akisi anawuza nduna zake kuti, “Mukumuona munthu uyu kuti ndi wamisala! Nʼchifukwa chiyani mukubwera naye kwa ine? |
7797 | 1SA 22:7 | Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo? |
7805 | 1SA 22:15 | Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.” |
7840 | 1SA 23:27 | Nthawi yomweyo munthu wina wamthenga anabwera kudzamuwuza Sauli kuti, “Bwerani msanga! Afilisti akuthira nkhondo dzikoli.” |
7853 | 1SA 24:12 | Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. |
7885 | 1SA 25:21 | Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino. |
8034 | 2SA 1:9 | “Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’ |
8044 | 2SA 1:19 | “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko! |
8050 | 2SA 1:25 | “Taonani amphamvu agwa ku nkhondo! Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda. |
8052 | 2SA 1:27 | “Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!” |
8074 | 2SA 2:22 | Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?” |
8092 | 2SA 3:8 | Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu! |
8102 | 2SA 3:18 | Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ” |