1649 | EXO 5:16 | Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.” |
3098 | LEV 13:45 | “Munthu wa khate lotere avale sanza, tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wapamwamba ndipo azifuwula kuti, ‘Ndine wodetsedwa, ndine wodetsedwa!’ |
4038 | NUM 11:13 | Ndingayipeze kuti nyama yoti anthu onsewa adye? Iwowa akulirira ine kuti, ‘Tipatse nyama tidye!’ |
4043 | NUM 11:18 | “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. |
4046 | NUM 11:21 | Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ |
4440 | NUM 23:23 | Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo, palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli. Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti, ‘Onani zimene Mulungu wachita!’ |
6455 | JOS 22:27 | Koma mosiyana ndi zimenezi, guwali likhale umboni pakati pa ife ndi inu ndiponso mibado imene ikubwerayo, kuti ife timapembedzanso Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe za mtendere. Motero mʼtsogolo muno zidzukulu zanu sizidzatha kunena kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Yehova!’ |
6785 | JDG 9:29 | Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’ ” |
7272 | 1SA 2:30 | “Paja Ine Yehova Mulungu wa Israeli ‘Ndinalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la abambo ako azidzanditumikira nthawi zonse.’ Koma tsopano ndikuti, ‘Zonsezi zithe!’ Tsopano anthu amene amandilemekeza Inenso ndidzawalemekeza koma iwo amene amandinyoza Ine ndidzawanyoza. |
7308 | 1SA 4:9 | Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” |
7753 | 1SA 20:21 | Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse. |
8034 | 2SA 1:9 | “Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’ |
8199 | 2SA 7:16 | Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ” |
8209 | 2SA 7:26 | kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. |
8210 | 2SA 7:27 | “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. |
8287 | 2SA 11:25 | Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.” |
8391 | 2SA 14:32 | Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ” |
8493 | 2SA 18:12 | Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’ |
8745 | 1KI 1:25 | Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’ |
8753 | 1KI 1:33 | mfumuyo inati kwa iwo, “Tengani atumiki anga ndipo mukweze mwana wanga Solomoni pa bulu wanga ndipo mupite naye ku Gihoni. Mukalize lipenga ndi kufuwula kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Solomoni!’ |
8767 | 1KI 1:47 | Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake, |
9232 | 1KI 14:11 | Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’ |
9473 | 1KI 21:19 | Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ” |
9541 | 2KI 1:4 | Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka. |
9543 | 2KI 1:6 | Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” |
9548 | 2KI 1:11 | Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’ ” |
9664 | 2KI 5:13 | Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ ” |
10892 | 1CH 17:24 | kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. |
11557 | 2CH 18:10 | Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ” |
11563 | 2CH 18:16 | Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’ ” |
11727 | 2CH 25:18 | Koma Yowasi mfumu ya Israeli inayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Nthawi ina kamtengo kaminga ka ku Lebanoni kanatumiza mawu kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amukwatire!’ Koma chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa minga uja. |
12413 | NEH 6:7 | Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.” |
12806 | EST 6:9 | Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ” |
12911 | JOB 3:3 | “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’ |
13413 | JOB 22:20 | Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka ndipo moto wawononga chuma chawo!’ |
13530 | JOB 28:22 | Chiwonongeko ndi imfa zikuti, ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’ |
17336 | PRO 30:15 | “Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’ |
18114 | ISA 21:9 | Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ” |
18297 | ISA 30:10 | Iwo amawuza alosi kuti, ‘Musationerenso masomphenya!’ Ndipo amanena kwa mneneri kuti, ‘Musatinenerenso zoona,’ mutiwuze zotikomera, munenere za mʼmutu mwanu. |
18548 | ISA 41:27 | Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’ Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu. |
18971 | ISA 65:5 | Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire, chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’ Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga, ngati moto umene umayaka tsiku lonse. |
18996 | ISA 66:5 | Imvani mawu a Yehova, inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake: “Abale anu amene amakudani, ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti, ‘Yehova alemekezeke kuti ife tione chimwemwe chanu!’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi. |
19061 | JER 2:27 | Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’ |
19101 | JER 4:5 | “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’ |
19175 | JER 6:17 | Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’ koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’ |
19192 | JER 7:4 | Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ |
19541 | JER 22:18 | Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’ |
19578 | JER 23:25 | “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ |
19631 | JER 25:28 | Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’ ” |
19875 | JER 34:5 | udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.” |
20083 | JER 44:4 | Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’ |
20225 | JER 49:29 | Landani matenti awo ndi nkhosa zawo, ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo. Mutengenso ngamira zawo. Anthu adzafuwula kwa iwo kuti, ‘Kuli zoopsa mbali zonse!’ |
20685 | EZK 8:12 | Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ |
20740 | EZK 11:16 | “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’ |
20779 | EZK 13:2 | “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’ |
20780 | EZK 13:3 | Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’ |
21013 | EZK 21:5 | Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ” |
21159 | EZK 25:7 | Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’ ” |
21275 | EZK 30:2 | “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. “ ‘Ufuwule mawu awa akuti, ‘Kalanga, tsiku lafika!’ |
21477 | EZK 37:11 | Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’ |
21480 | EZK 37:14 | Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’ ” |
21485 | EZK 37:19 | iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’ |
21494 | EZK 37:28 | Pamenepo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti Ine Yehova ndiye amene ndimasandutsa Israeli kukhala woyera, pamene malo anga opatulika adzakhala pakati pawo kwamuyaya!’ ” |
22007 | DAN 7:5 | “Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’ |
22217 | HOS 4:15 | “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli, Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. “Usapite ku Giligala. Usapite ku Beti-Aveni. Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’ |
22265 | HOS 8:2 | Israeli akulirira kwa Ine kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’ |
22675 | MIC 2:11 | Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti, ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri, woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’ |
22836 | HAB 2:19 | Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; mʼkati mwake mulibe mpweya. |
22896 | ZEP 3:7 | Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita. |
22998 | ZEC 4:7 | “Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ” |
23102 | ZEC 11:5 | Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. |
23163 | MAL 1:5 | Inu mudzaziona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati, ‘Yehova ndi Wamkulu, ukulu wake umafika ngakhale kunja kwa malire a Israeli!’ |
23171 | MAL 1:13 | Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. |
23408 | MAT 7:23 | Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’ |
23824 | MAT 18:28 | “Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’ |
24049 | MAT 24:23 | Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. |
24083 | MAT 25:6 | “Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’ |
24088 | MAT 25:11 | “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’ |
24098 | MAT 25:21 | “Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’ |
24100 | MAT 25:23 | “Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’ |
24404 | MRK 4:12 | kotero kuti, “ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ” |
24630 | MRK 9:23 | Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.” |
24807 | MRK 13:21 | Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. |
24811 | MRK 13:25 | nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’ |
24823 | MRK 13:37 | Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ” |
25614 | LUK 13:27 | “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’ |
25743 | LUK 17:23 | Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo. |
25762 | LUK 18:5 | koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ” |
25824 | LUK 19:24 | “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ” |
26033 | LUK 23:29 | Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’ |
27102 | ACT 4:11 | Iye ndi “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana, umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’ |
27472 | ACT 13:41 | “ ‘Onani, inu anthu onyoza, dabwani ndipo wonongekani, chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu, inu simudzazikhulupirira ngakhale wina atakufotokozerani!’ ” |
27478 | ACT 13:47 | Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ” |
27785 | ACT 22:13 | Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo. |
31064 | REV 18:2 | Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa. |
31072 | REV 18:10 | Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake. “ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, Babuloni mzinda wamphamvu! Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’ |
31079 | REV 18:17 | Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’ “Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. |