Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   “Word!    February 25, 2023 at 00:56    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

363  GEN 15:2  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko?
369  GEN 15:8  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”
559  GEN 22:11  Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!” Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
1265  GEN 42:12  Iye anawawuza kuti, “Ayi! Inu mwabwera kudzaona pamene palibe chitetezo mʼdziko muno.”
1387  GEN 45:28  Ndipo Israeli anati, “Ndatsimikizadi! Mwana wanga Yosefe akanali ndi moyodi. Ndipita ndikamuone ndisanafe.”
1389  GEN 46:2  Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!” Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”
1584  EXO 3:4  Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!” Ndipo anayankha, “Wawa.”
1848  EXO 12:31  Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha.
2470  EXO 32:31  Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide.
4198  NUM 16:3  Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?”
4207  NUM 16:12  Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera!
4257  NUM 17:27  Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika!
5988  JOS 7:10  Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?
5998  JOS 7:20  Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi:
6452  JOS 22:24  “Ayi! Ife tinachita izi kuopa kuti tsiku lina zidzukulu zanu zingadzanene kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Kodi inu mukufuna chiyani kwa Yehova Mulungu wa Israeli?
6499  JOS 24:21  Koma anthuwo anati kwa Yoswa, “Ayi! Ife tidzatumikira Yehova.”
6505  JOS 24:27  Yoswa anati kwa anthu onse, “Tamvani! Mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa. Mwalawu wamva mawu onse amene Yehova wayankhula kwa ife. Udzakhala mboni yotitsutsa ngati mukhala osakhulupirika kwa Mulungu wanu.”
6615  JDG 4:14  Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata.
6728  JDG 8:7  Gideoni anayankha kuti, “Mwatero! Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna mʼdzanja langa, ndidzakukwapulani ndi matsatsa a minga ya mʼchipululu.”
7288  1SA 3:10  Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.”
7390  1SA 8:19  Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira.
7521  1SA 14:11  Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.”
7734  1SA 20:2  Yonatani anayankha kuti, “Sizitheka! Iwe sufa ayi! Taona abambo anga sachita chinthu chilichonse chachikulu kapena chachingʼono wosandiwuza ine. Tsopano abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Sichoncho ayi.”
7741  1SA 20:9  Yonatani anati, “Sizitheka! Ndikanadziwa kuti abambo anga atsimikiza kuti akuchite choyipa, kodi sindikanakuwuza?”
7917  1SA 26:9  Koma Davide anamuyankha Abisai kuti, “Usamuphe! Ndani adzapha wodzozedwa wa Yehova ndi kupezeka wosalakwa?
8336  2SA 13:16  Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera.
8348  2SA 13:28  Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.”
8406  2SA 15:14  Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”
8573  2SA 20:16  mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.”
8756  1KI 1:36  Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, “Ameni! Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu akhazikitse kuti zichitike motero.
8841  1KI 3:22  Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.” Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
9626  2KI 4:19  Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!” Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.”
9632  2KI 4:25  Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo!
9634  2KI 4:27  Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”
9683  2KI 6:5  Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”
9772  2KI 9:12  Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.” Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”
9847  2KI 11:14  Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
10962  1CH 21:23  Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.”
11674  2CH 23:13  Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
12269  EZR 10:12  Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu.
13538  JOB 29:2  “Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi, masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,
14451  PSA 35:21  Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa! Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
14564  PSA 40:16  Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!” abwerere akuchita manyazi.
17387  ECC 1:2  “Zopandapake! Zopandapake!” atero Mlaliki. “Zopandapake kotheratu! Zopandapake.”
17395  ECC 1:10  Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Taona! Ichi ndiye chatsopano?” Chinalipo kale, kalekale; chinalipo ife kulibe.
18619  ISA 44:16  Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto wowotcherapo nyama imene amadya, nakhuta. Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti, “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
19021  JER 1:6  Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”
19635  JER 25:32  Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani! Mavuto akuti akachoka pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina; mphepo ya mkuntho ikuyambira ku malekezero a dziko.”
19693  JER 28:6  Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni.
20034  JER 41:8  Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja.
20276  JER 50:41  “Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri, wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
20504  LAM 4:15  Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!” “Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!” Akamathawa ndi kumangoyendayenda, pakati pa anthu a mitundu yonse amati, “Asakhalenso ndi ife.”
20648  EZK 7:2  “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti: “Chimaliziro! Chimaliziro chafika ku ngodya zinayi za dziko.
20651  EZK 7:5  “Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: “Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo! Taona chikubwera!
21901  DAN 3:25  Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.”
22670  MIC 2:6  Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere! Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi; ife sitidzachititsidwa manyazi.”
22776  NAM 2:9  Ninive ali ngati dziwe, ndipo madzi ake akutayika. Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.
22974  ZEC 2:10  “Tulukani! Tulukani! Thawaniko ku dziko la kumpoto,” akutero Yehova, “pakuti ndinakumwazirani ku mphepo zinayi zamlengalenga,” akutero Yehova.
23427  MAT 8:13  Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, “Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira.” Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.
23439  MAT 8:25  Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”
23560  MAT 12:2  Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.”
24024  MAT 23:37  “Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune.
24395  MRK 4:3  “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake.
24431  MRK 4:39  Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
24626  MRK 9:19  Yesu anayankha kuti, “Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo.”
24706  MRK 10:49  Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.”
24718  MRK 11:9  Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti, “Hosana! “Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”
24924  MRK 15:29  Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu,
25166  LUK 4:34  “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
25411  LUK 9:41  Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
25543  LUK 12:15  Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”
25997  LUK 22:64  Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?”
26025  LUK 23:21  Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
26159  JHN 1:46  Natanieli anafunsa kuti, “Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?” Filipo anati, “Bwera udzaone.”
26287  JHN 5:8  Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.”
26662  JHN 12:13  Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti, “Hosana! “Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye! “Yodala Mfumu ya Israeli!”
26900  JHN 19:6  Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
27153  ACT 5:25  Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.”
27300  ACT 9:15  Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli.
27580  ACT 16:28  Koma Paulo anafuwula kuti, “Usadzipweteke! Tonse tilipo!”
30852  REV 5:5  Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”
30890  REV 7:12  Iwo anati, “Ameni! Matamando ndi ulemerero, nzeru, mayamiko, ulemu, ulamuliro ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi, Ameni!”
31003  REV 14:8  Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”
31081  REV 18:19  Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti, “Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, kumene onse anali ndi sitima pa nyanja analemera kudzera mʼchuma chake! Mu ora limodzi wawonongedwa.
31087  REV 19:1  Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
31089  REV 19:3  Ndipo anafuwulanso kuti, “Haleluya! Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
31092  REV 19:6  Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati, “Haleluya! Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
31125  REV 21:3  Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.