8842 | 1KI 3:23 | Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ” |
13329 | JOB 19:28 | “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji, popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’ |
13410 | JOB 22:17 | Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’ |
17336 | PRO 30:15 | “Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’ |
19059 | JER 2:25 | Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu. Koma unati, ‘Zamkutu! Ine ndimakonda milungu yachilendo, ndipo ndidzayitsatira.’ |
19101 | JER 4:5 | “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’ |
19263 | JER 9:18 | Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti, ‘Aa! Ife tawonongeka! Tachita manyazi kwambiri! Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ” |
19491 | JER 19:15 | “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ” |
19578 | JER 23:25 | “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ |
20854 | EZK 16:23 | “ ‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse, |
21171 | EZK 26:2 | “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ |
21430 | EZK 36:2 | Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’ |
21501 | EZK 38:7 | “ ‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo. |
24088 | MAT 25:11 | “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’ |
25679 | LUK 15:22 | “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. |
25686 | LUK 15:29 | Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. |
27779 | ACT 22:7 | Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’ ” |
27790 | ACT 22:18 | Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ” |
31064 | REV 18:2 | Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa. |
31072 | REV 18:10 | Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake. “ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, Babuloni mzinda wamphamvu! Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’ |
31078 | REV 18:16 | ndipo adzalira mokuwa kuti, “ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu, iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira, ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale! |