2021 | EXO 18:21 | Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. |
2025 | EXO 18:25 | Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. |
2659 | EXO 38:25 | Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. |
3533 | LEV 26:8 | Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga. |
3691 | NUM 2:32 | Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. |
4698 | NUM 31:32 | Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000, |
4699 | NUM 31:33 | Ngʼombe 72,000, |
4700 | NUM 31:34 | abulu 61,000, |
4702 | NUM 31:36 | Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali: nkhosa 337,500, |
4709 | NUM 31:43 | Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500, |
4710 | NUM 31:44 | ngʼombe 36,000, |
4711 | NUM 31:45 | abulu 30,500, |
4909 | DEU 1:15 | Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko. |
5790 | DEU 32:30 | Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000 kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse, Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa, Yehova akanapanda kuwataya? |
6805 | JDG 9:49 | Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi. |
7383 | 1SA 8:12 | Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. |
7455 | 1SA 11:8 | Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. |
7492 | 1SA 13:5 | Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni. |
7685 | 1SA 18:7 | Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati: “Sauli wapha 1,000, Koma Davide wapha miyandamiyanda.” |
7786 | 1SA 21:12 | Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, “Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti, “Sauli wapha 1,000, koma Davide wapha miyandamiyanda?” |
8216 | 2SA 8:4 | Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. |
8453 | 2SA 17:1 | Ahitofele anati kwa Abisalomu, “Mundilole ndisankhe asilikali 12,000, ndinyamuke usiku womwe uno kuti ndithamangire Davide. |
8493 | 2SA 18:12 | Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’ |
8896 | 1KI 5:29 | Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri, |
9051 | 1KI 8:63 | Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova. |
9082 | 1KI 9:28 | Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni. |
9092 | 1KI 10:10 | Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni. |
9096 | 1KI 10:14 | Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000, |
9108 | 1KI 10:26 | Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu. |
9175 | 1KI 12:21 | Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini, nasankha ankhondo okwanira 180,000, kuti akamenyane ndi nyumba ya Israeli kuti amubwezere Rehobowamu mwana wa Solomoni ufumu wake. |
9656 | 2KI 5:5 | Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero. |
10202 | 2KI 23:33 | Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34. |
10222 | 2KI 24:16 | Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000. |
10453 | 1CH 5:21 | Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, |
10544 | 1CH 7:5 | Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo. |
10751 | 1CH 12:27 | Anthu a fuko la Levi analipo 4,600, |
10752 | 1CH 12:28 | mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700, |
10821 | 1CH 15:25 | Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. |
10899 | 1CH 18:4 | Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. |
10919 | 1CH 19:7 | Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo. |
11108 | 1CH 26:26 | Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. |
11115 | 1CH 27:1 | Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000. |
11149 | 1CH 28:1 | Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima. |
11175 | 1CH 29:6 | Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. |
11190 | 1CH 29:21 | Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse. |
11201 | 2CH 1:2 | Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja. |
11213 | 2CH 1:14 | Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu. |
11334 | 2CH 7:5 | Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu. |
11382 | 2CH 9:13 | Kulemera kwa golide amene Solomoni amalandira pa chaka kunali makilogalamu 23,000, |
11461 | 2CH 13:3 | Abiya anapita ku nkhondo ndi asilikali odziwa bwino nkhondo 400,000, ndipo Yeroboamu anandandalitsa ankhondo, asilikali 800,000 odziwa bwino nkhondo, osankhidwa ndi amphamvu, woti amenyane naye. |
11714 | 2CH 25:5 | Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango. |
11721 | 2CH 25:12 | Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka. |
11765 | 2CH 27:5 | Yotamu anachita nkhondo ndi mfumu ya Aamoni ndipo anawagonjetsa. Chaka chimenecho Aamoni anapereka makilogalamu 3,400, matani 1,000 a tirigu ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni anabweretsa zinthu zomwezi chaka chachiwiri ndi chachitatu. |
11856 | 2CH 30:24 | Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. |
11978 | 2CH 35:7 | Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu. |
12096 | EZR 2:64 | Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, |
12876 | JOB 1:3 | ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa. |
13938 | JOB 42:12 | Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. |
17493 | ECC 6:6 | ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi? |
17527 | ECC 7:28 | pamene ine ndinali kufufuzabe koma osapeza kanthu, ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000, koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama. |
17656 | SNG 4:4 | Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo. |
17875 | ISA 7:23 | Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga. |
21787 | EZK 48:16 | Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250. |
21801 | EZK 48:30 | “Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250, |
21803 | EZK 48:32 | “Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani. |
21804 | EZK 48:33 | “Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni. |
22724 | MIC 6:7 | Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga? |
23751 | MAT 16:10 | Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? |
24092 | MAT 25:15 | Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake. |
24097 | MAT 25:20 | Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’ |
24099 | MAT 25:22 | “Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, ‘Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.’ |
24588 | MRK 8:19 | Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?” Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.” |
24589 | MRK 8:20 | “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.” |
30597 | 2PE 3:8 | Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! |