|
4477 | Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.” | |
6720 | Gideoni anatumiza amithenga ku dziko lonse la ku mapiri la Efereimu kukanena kuti, “Tsikani mumenyane ndi Amidiyani ndipo mulande madooko awo owolokera mpaka ku Beti-Bara.” Choncho anthu onse a fuko la Efereimu anasonkhana ndipo analanda madooko awo owolokera mpaka ku Betibaala. | |
20223 | “Ndidzatentha malinga a Damasiko; moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.” |