6947 | JDG 15:16 | Ndipo Samsoni anati, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu. Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu 1,000.” |
6956 | JDG 16:5 | Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.” |
9674 | 2KI 5:23 | Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi. |