15474 | PSA 91:14 | “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa. |
24631 | MRK 9:24 | Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!” |
25799 | LUK 18:42 | Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” |
26768 | JHN 14:31 | koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine. “Nyamukani; tizipita.” |
27793 | ACT 22:21 | Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.” |
28940 | 2CO 4:13 | Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula, |