57 | GEN 3:1 | Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ” |
59 | GEN 3:3 | koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ” |
311 | GEN 12:12 | Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. |
360 | GEN 14:23 | kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’ |
438 | GEN 18:13 | Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’ |
509 | GEN 20:13 | Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ” |
599 | GEN 24:7 | Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi. |
606 | GEN 24:14 | Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. |
629 | GEN 24:37 | Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani, |
631 | GEN 24:39 | “Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, ‘Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?’ |
632 | GEN 24:40 | “Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa. |
636 | GEN 24:44 | ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.” |
637 | GEN 24:45 | “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’ |
638 | GEN 24:46 | “Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo. |
639 | GEN 24:47 | “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake, |
702 | GEN 26:9 | Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.” |
735 | GEN 27:7 | ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ |
882 | GEN 31:8 | Pamene abambo anu anati, ‘Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, ‘Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi. |
886 | GEN 31:12 | Ndipo iye anati, ‘Tayangʼana ndipo taona kuti atonde onse okwerana ndi ziweto ali amichocholozi, amawangamawanga kapena a mathothomathotho, popeza ndaona zonse zimene Labani wakhala akukuchitira. |
903 | GEN 31:29 | Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, ‘Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’ |
933 | GEN 32:5 | Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. |
938 | GEN 32:10 | Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ |
946 | GEN 32:18 | Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’ |
947 | GEN 32:19 | Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” |
949 | GEN 32:21 | Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” |
1101 | GEN 37:17 | Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’ ” Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani. |
1142 | GEN 38:22 | Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ” |
1284 | GEN 42:31 | Koma tinamuwuza kuti, ‘Ndife anthu woona mtima osati akazitape. |
1294 | GEN 43:3 | Koma Yuda anati kwa iye, “Munthu uja anatichenjeza monenetsa kuti, ‘Simudzandionanso ine pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanu.’ |
1296 | GEN 43:5 | Koma mukapanda kumulola, ife sitipita, chifukwa munthuyo anatiwuza kuti, ‘Simudzandionanso pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanuyo.’ ” |
1298 | GEN 43:7 | Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, ‘Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, ‘Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?” |
1329 | GEN 44:4 | Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? |
1344 | GEN 44:19 | Mbuye wanga munafunsa akapolo anufe kuti, ‘Kodi muli ndi abambo anu kapena mʼbale wanu?’ |
1345 | GEN 44:20 | Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’ |
1346 | GEN 44:21 | “Ndipo inu munatiwuza kuti, ‘Mubwere naye kwa ine kuti ndidzamuone ndekha.’ |
1347 | GEN 44:22 | Ife tinati, ‘Mbuye wathu, mnyamatayo sangasiye abambo ake, akawasiya ndiye kuti abambo akewo adzafa.’ |
1348 | GEN 44:23 | Koma inu munatichenjeza kuti, ‘Pokhapokha mutabwera naye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri, simudzandionanso.’ |
1350 | GEN 44:25 | “Abambo athu anatiwuza kuti, ‘Pitaninso mukagule kachakudya pangʼono.’ |
1351 | GEN 44:26 | Koma tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’ |
1352 | GEN 44:27 | “Koma kapolo wanu, abambo athu anatiwuza kuti, ‘Inu mukudziwa kuti mkazi wanga anandiberekera ana aamuna awiri. |
1357 | GEN 44:32 | Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, ‘Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’ |
1368 | GEN 45:9 | Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, ‘Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe. |
1376 | GEN 45:17 | Farao anati kwa Yosefe, “Uwawuze abale ako kuti, ‘Senzetsani nyama zanu katundu ndi kubwerera ku dziko la Kanaani. |
1378 | GEN 45:19 | “Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno. |
1418 | GEN 46:31 | Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine. |
1420 | GEN 46:33 | Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ |
1456 | GEN 48:4 | nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’ |
1512 | GEN 50:5 | ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ” |
1524 | GEN 50:17 | ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira. |
1593 | EXO 3:13 | Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” |
1594 | EXO 3:14 | Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” |
1603 | EXO 4:1 | Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ” |
1624 | EXO 4:22 | Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’ |
1625 | EXO 4:23 | Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ” |
1634 | EXO 5:1 | Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ” |
1641 | EXO 5:8 | Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ |
1643 | EXO 5:10 | Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu. |
1649 | EXO 5:16 | Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.” |
1650 | EXO 5:17 | Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ |
1662 | EXO 6:6 | “Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo. |
1695 | EXO 7:9 | “Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.” |
1705 | EXO 7:19 | Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.” |
1716 | EXO 8:1 | Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ” |
1731 | EXO 8:16 | Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze. |
1781 | EXO 10:3 | Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze. |
1843 | EXO 12:26 | Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, ‘Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’ |
1844 | EXO 12:27 | Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza. |
1876 | EXO 13:8 | Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’ |
1882 | EXO 13:14 | “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu. |
1893 | EXO 14:3 | Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ |
1902 | EXO 14:12 | Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.” |
1957 | EXO 16:9 | Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ” |
1960 | EXO 16:12 | “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” |
1964 | EXO 16:16 | Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ” |
1971 | EXO 16:23 | Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ” |
1980 | EXO 16:32 | Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” |
2031 | EXO 19:4 | ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. |
2039 | EXO 19:12 | Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu. |
2074 | EXO 20:22 | Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. |
2083 | EXO 21:5 | “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’ |
2447 | EXO 32:8 | Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” |
2451 | EXO 32:12 | Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. |
2452 | EXO 32:13 | Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ” |
2462 | EXO 32:23 | Iwo anati kwa ine, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’ |
2463 | EXO 32:24 | Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.” |
2466 | EXO 32:27 | Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ” |
2475 | EXO 33:1 | Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ |
2479 | EXO 33:5 | Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.” |
2486 | EXO 33:12 | Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ |
2749 | LEV 1:3 | “ ‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire. |
2756 | LEV 1:10 | “ ‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema. |
2760 | LEV 1:14 | “ ‘Koma ngati chopereka kwa Yehova ndi nsembe yopsereza ya mbalame, ndiye ikhale njiwa kapena mawunda. |
2764 | LEV 2:1 | “ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, |
2767 | LEV 2:4 | “ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. |
2774 | LEV 2:11 | “ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. |
2777 | LEV 2:14 | “ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. |
2780 | LEV 3:1 | “ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema. |
2785 | LEV 3:6 | “ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, choperekacho chikhale nkhosa yayimuna kapena yayikazi yopanda chilema. |
2791 | LEV 3:12 | “ ‘Ngati munthuyo apereka mbuzi ngati nsembe, abwere nayo kwa Yehova. |
2796 | LEV 3:17 | “ ‘Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.’ ” |