17881 | ISA 8:4 | Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.” |
18630 | ISA 44:27 | Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’ ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako. |
19090 | JER 3:19 | “Ine mwini ndinati, “ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga ndikukupatsani dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’ Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ ndi kuti simudzaleka kunditsata. |
22169 | HOS 1:6 | Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. |
23325 | MAT 5:22 | Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena. |
23340 | MAT 5:37 | Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo. |
25247 | LUK 6:32 | “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. |
25248 | LUK 6:33 | Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi. |
25249 | LUK 6:34 | Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. |
25583 | LUK 12:55 | Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. |
26712 | JHN 13:13 | Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. |