5839 | DEU 33:27 | Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’ |
8803 | 1KI 2:30 | Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ” Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.” Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.” |
9546 | 2KI 1:9 | Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ” |
13308 | JOB 19:7 | “Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha; ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama. |
13373 | JOB 21:14 | Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu. |
13422 | JOB 22:29 | Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’ Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa. |
13863 | JOB 39:25 | Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali, kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo. |
17336 | PRO 30:15 | “Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’ |
19054 | JER 2:20 | “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu ndi kudula msinga zanu; munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere. Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. |
20643 | EZK 6:11 | “Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri. |
22836 | HAB 2:19 | Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; mʼkati mwake mulibe mpweya. |
23170 | MAL 1:12 | “Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’ |