73 | GEN 3:17 | Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako. |
885 | GEN 31:11 | Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, ‘Yakobo.’ Ine ndinayankha, ‘Ee, Ambuye.’ |
4018 | NUM 10:29 | Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.” |
6621 | JDG 4:20 | Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ” |
6877 | JDG 12:6 | Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’ ” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000. |
18581 | ISA 43:6 | Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; |
19175 | JER 6:17 | Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’ koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’ |
19198 | JER 7:10 | ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? |
19544 | JER 22:21 | Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere. Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’ Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono. Simunandimvere Ine. |
22197 | HOS 2:25 | Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ” |
23994 | MAT 23:7 | Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’ |
24779 | MRK 12:37 | Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?” Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo. |
25892 | LUK 20:44 | Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?” |
25958 | LUK 22:25 | Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ |
26785 | JHN 15:17 | Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’ |