18530 | ISA 41:9 | Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi. Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’ Ndinakusankha ndipo sindinakutaye. |
18608 | ISA 44:5 | Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’ wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo; winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli. |
22190 | HOS 2:18 | “Tsiku limeneli,” Yehova akuti, “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’ sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’ |
22197 | HOS 2:25 | Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ” |
28248 | ROM 9:25 | Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,” |