Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   “    February 11, 2023 at 19:19    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

3  GEN 1:3  Pamenepo Mulungu anati, Kuwale” ndipo kunawaladi.
5  GEN 1:5  Mulungu anatcha kuwalako usana” ndipo mdima anawutcha usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
6  GEN 1:6  Kenaka Mulungu anati, Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
8  GEN 1:8  Mulungu anatcha thambo lija kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
9  GEN 1:9  Mulungu anati, Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
10  GEN 1:10  Mulungu anawutcha mtundawo dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
11  GEN 1:11  Kenaka Mulungu anati, Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
14  GEN 1:14  Mulungu anati, Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;
20  GEN 1:20  Mulungu anati, Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.”
22  GEN 1:22  Mulungu anazidalitsa nati, Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”
24  GEN 1:24  Kenaka Mulungu anati, Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi.
26  GEN 1:26  Zitatha izi Mulungu anati, Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
28  GEN 1:28  Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
29  GEN 1:29  Kenaka Mulungu anati, Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.
47  GEN 2:16  Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu;
49  GEN 2:18  Ndipo Yehova Mulungu anati, Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.”
54  GEN 2:23  Munthu uja anati, Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”
57  GEN 3:1  Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
58  GEN 3:2  Mkaziyo anati kwa njokayo, Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu,
60  GEN 3:4  Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo.
61  GEN 3:5  Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”
65  GEN 3:9  Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, Uli kuti?”
66  GEN 3:10  Iye anayankha, Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”
67  GEN 3:11  Ndipo anamufunsa, Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”
68  GEN 3:12  Koma munthu uja anati, Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”
69  GEN 3:13  Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Wachitachi nʼchiyani?” Mkaziyo anati, Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
70  GEN 3:14  Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, Popeza wachita zimenezi, Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.
72  GEN 3:16  Kwa mkaziyo Iye anati, Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati; ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo adzakulamulira.”
73  GEN 3:17  Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako.
78  GEN 3:22  Ndipo Yehova Mulungu anati, Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.”
81  GEN 4:1  Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.”
86  GEN 4:6  Choncho Yehova anati kwa Kaini, Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa?
88  GEN 4:8  Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.
89  GEN 4:9  Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”
90  GEN 4:10  Yehova anati, Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka.
93  GEN 4:13  Kaini anati kwa Yehova, Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga.
95  GEN 4:15  Koma Yehova anamuwuza kuti, Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe.
103  GEN 4:23  Lameki anawuza akazi akewo kuti, Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
105  GEN 4:25  Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.”
108  GEN 5:2  Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha Munthu.”
135  GEN 5:29  Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
141  GEN 6:3  Tsono Yehova anati, Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”
145  GEN 6:7  Choncho Yehova anati, Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.”
151  GEN 6:13  Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko.
161  GEN 7:1  Ndipo Yehova anati kwa Nowa, Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.
200  GEN 8:16  Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo.
205  GEN 8:21  Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.
206  GEN 8:22  Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.”
207  GEN 9:1  Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi.
210  GEN 9:4  Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda.
212  GEN 9:6  Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.
215  GEN 9:9  Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo,
218  GEN 9:12  Ndipo Mulungu anati, Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo.
223  GEN 9:17  Choncho Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
231  GEN 9:25  anati, Atembereredwe Kanaani! Adzakhala kapolo wa pansi kwenikweni kwa abale ake.”
232  GEN 9:26  Anatinso, Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu.
244  GEN 10:9  Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
270  GEN 11:3  Tsono anawuzana kuti, Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.
271  GEN 11:4  Kenaka anati, Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
273  GEN 11:6  Yehova anati, Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita.
300  GEN 12:1  Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.
301  GEN 12:2  Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
306  GEN 12:7  Yehova anadza kwa Abramu nati, Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.
310  GEN 12:11  Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri.
317  GEN 12:18  Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako?
327  GEN 13:8  Tsono Abramu anati kwa Loti, Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale.
333  GEN 13:14  Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo.
356  GEN 14:19  ndipo anadalitsa Abramu nati, Mulungu Wammwambamwamba, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
358  GEN 14:21  Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”
359  GEN 14:22  Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira
362  GEN 15:1  Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.”
363  GEN 15:2  Koma Abramu anati, Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko?
365  GEN 15:4  Yehova anayankhula naye nati: Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.”
366  GEN 15:5  Yehova anapita naye Abramu panja nati, Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
368  GEN 15:7  Ndipo anamuwuza kuti, Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.”
369  GEN 15:8  Koma Abramu anati, Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”
370  GEN 15:9  Kotero Yehova anati kwa iye, Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.”
374  GEN 15:13  Tsono Yehova anati kwa iye, Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.
379  GEN 15:18  Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
384  GEN 16:2  ndipo Sarai anati kwa Abramu, Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.” Abramu anamvera Sarai.
387  GEN 16:5  Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
388  GEN 16:6  Abramu anati, Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
390  GEN 16:8  Ndipo mngeloyo anati, Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha, Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
391  GEN 16:9  Mngelo wa Yehova anamuwuza kuti, Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukamugonjere.
393  GEN 16:11  Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.
395  GEN 16:13  Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.”
399  GEN 17:1  Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.
402  GEN 17:4  Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
407  GEN 17:9  Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali.
413  GEN 17:15  Mulungu anatinso kwa Abrahamu, Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara.
415  GEN 17:17  Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?”
416  GEN 17:18  Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Bwanji mumudalitse Ismaeli.”
417  GEN 17:19  Koma Mulungu anati, Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.
428  GEN 18:3  Ngati mwandikomera mtima, mbuye wanga, musamulambalale mtumiki wanu.
430  GEN 18:5  Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.” Ndipo iwo anamuyankha nati, Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.”
431  GEN 18:6  Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.”
434  GEN 18:9  Anthuwo anafunsa Abrahamu kuti, Mkazi wako Sara ali kuti?” Iye anati, Ali mu tentimu.”
435  GEN 18:10  Tsono mmodzi mwa iwo anati, Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi.
437  GEN 18:12  Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba.”
438  GEN 18:13  Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’