109 | GEN 5:3 | Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
112 | GEN 5:6 | Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. |
114 | GEN 5:8 | Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira. |
116 | GEN 5:10 | Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
120 | GEN 5:14 | Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira. |
124 | GEN 5:18 | Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. |
131 | GEN 5:25 | Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. |
134 | GEN 5:28 | Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. |
141 | GEN 6:3 | Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.” |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
171 | GEN 7:11 | Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. |
184 | GEN 7:24 | Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150. |
187 | GEN 8:3 | Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, |
188 | GEN 8:4 | ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. |
197 | GEN 8:13 | Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
277 | GEN 11:10 | Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. |
292 | GEN 11:25 | Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
351 | GEN 14:14 | Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. |
415 | GEN 17:17 | Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” |
519 | GEN 21:5 | Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa. |
573 | GEN 23:1 | Sara anakhala ndi moyo zaka 127. |
614 | GEN 24:22 | Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100. |
666 | GEN 25:7 | Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. |
676 | GEN 25:17 | Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. |
980 | GEN 33:19 | Malo amenewo anagula kwa zidzukulu za Hamori, abambo a Sekemu ndi ndalama 100 zasiliva. |
1040 | GEN 35:28 | Isake anakhala ndi moyo zaka 180. |
1086 | GEN 37:2 | Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake. |
1405 | GEN 46:18 | Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16. |
1430 | GEN 47:9 | Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.” |
1449 | GEN 47:28 | Yakobo anakhala ku Igupto zaka 17 ndipo zaka za moyo wake zinali 147. |
1529 | GEN 50:22 | Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 |
1533 | GEN 50:26 | Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto. |
1672 | EXO 6:16 | Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1674 | EXO 6:18 | Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. |
1676 | EXO 6:20 | Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137. |
1835 | EXO 12:18 | Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo. |
2021 | EXO 18:21 | Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. |
2025 | EXO 18:25 | Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. |
2206 | EXO 25:10 | “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. |
2213 | EXO 25:17 | “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. |
2219 | EXO 25:23 | “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. |
2261 | EXO 26:25 | Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse. |
2274 | EXO 27:1 | “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. |
2385 | EXO 30:2 | Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. |
2597 | EXO 36:30 | Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse. |
2606 | EXO 37:1 | Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. |
2611 | EXO 37:6 | Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. |
2615 | EXO 37:10 | Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. |
2630 | EXO 37:25 | Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo. |
2635 | EXO 38:1 | Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. |
2658 | EXO 38:24 | Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika. |
2661 | EXO 38:27 | Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. |
3408 | LEV 23:5 | Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. |
3409 | LEV 23:6 | Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. |
3437 | LEV 23:34 | “Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova. |
3442 | LEV 23:39 | “ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso. |
3533 | LEV 26:8 | Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga. |
3646 | NUM 1:41 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500. |
3668 | NUM 2:9 | Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka. |
3675 | NUM 2:16 | Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka. |
3683 | NUM 2:24 | Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka. |
3687 | NUM 2:28 | Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500. |
3690 | NUM 2:31 | Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. |
3743 | NUM 3:50 | Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. |
3865 | NUM 7:14 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3871 | NUM 7:20 | Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110 yodzaza ndi lubani; |
3877 | NUM 7:26 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3883 | NUM 7:32 | Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3889 | NUM 7:38 | mbale yagolide imodzi yolemera 110, yodzaza ndi lubani; |
3895 | NUM 7:44 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3901 | NUM 7:50 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3907 | NUM 7:56 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani, |
3913 | NUM 7:62 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3919 | NUM 7:68 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3925 | NUM 7:74 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3931 | NUM 7:80 | mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
3937 | NUM 7:86 | Mbale khumi ndi ziwiri zagolide zodzaza ndi lubanizo zinkalemera magalamu 110 iliyonse, monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Pamodzi, mbale zagolide zinkalemera kilogalamu imodzi ndi theka. |
3969 | NUM 9:3 | Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.” |
3971 | NUM 9:5 | ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. |
3977 | NUM 9:11 | Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. |
4057 | NUM 11:32 | Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse. |
4244 | NUM 17:14 | Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. |
4542 | NUM 26:51 | Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. |
4595 | NUM 28:16 | “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. |
4596 | NUM 28:17 | Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. |
4670 | NUM 31:4 | Mutumize ku nkhondoko amuna 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.” |
4671 | NUM 31:5 | Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli. |
4672 | NUM 31:6 | Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza. |
4680 | NUM 31:14 | Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo. |
4700 | NUM 31:34 | abulu 61,000, |
4705 | NUM 31:39 | abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61; |
4706 | NUM 31:40 | anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32. |