207 | GEN 9:1 | Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi. |
245 | GEN 10:10 | Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. |
276 | GEN 11:9 | Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi. |
307 | GEN 12:8 | Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. |
322 | GEN 13:3 | Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, |
339 | GEN 14:2 | anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). |
345 | GEN 14:8 | Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo |
384 | GEN 16:2 | ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.” Abramu anamvera Sarai. |
391 | GEN 16:9 | Mngelo wa Yehova anamuwuza kuti, “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukamugonjere. |
396 | GEN 16:14 | Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi. |
416 | GEN 17:18 | Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.” |
454 | GEN 18:29 | Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.” |
457 | GEN 18:32 | Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.” |
496 | GEN 19:38 | Mwana wamkazi wamngʼono naye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha iye Beni-Ammi. Iyeyu ndiye kholo la Aamoni onse. |
528 | GEN 21:14 | Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba. |
545 | GEN 21:31 | Kotero malo amenewo anatchedwa Beeriseba, chifukwa anthu awiriwo analumbirirapo malumbiro. |
546 | GEN 21:32 | Atatha kuchita pangano pa Beeriseba, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wankhondo wake anabwerera ku dziko la Afilisti. |
547 | GEN 21:33 | Abrahamu anadzala mtengo wa bwemba ku Beeriseba, ndipo anapemphera pamenepo mʼdzina la Yehova, Mulungu Wamuyaya. |
553 | GEN 22:5 | Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.” |
567 | GEN 22:19 | Kenaka Abrahamu anabwerera kumene anasiya antchito ake kuja nanyamukira nawo pamodzi kupita ku Beeriseba. Ndipo Abrahamu anakhala ku Beeriseba. |
569 | GEN 22:21 | Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. |
570 | GEN 22:22 | Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” |
571 | GEN 22:23 | Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa. |
576 | GEN 23:4 | “Ine ndine mlendo wongoyendayenda kwanu kuno. Bwanji mundigulitse malo woti akhale manda kuti ndiyikepo thupi la mkazi wanga.” |
607 | GEN 24:15 | Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu. |
616 | GEN 24:24 | Anamuyankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betueli, mwana amene Milika anaberekera Nahori.” |
623 | GEN 24:31 | Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.” |
639 | GEN 24:47 | “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake, |
642 | GEN 24:50 | Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu. |
649 | GEN 24:57 | Koma iwo anati, “Bwanji timuyitane mtsikanayo ndipo timufunse ngati afuna kupita nanu panopa.” |
654 | GEN 24:62 | Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. |
670 | GEN 25:11 | Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya). |
679 | GEN 25:20 | ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu. |
681 | GEN 25:22 | Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova. |
716 | GEN 26:23 | Kenaka Isake anachoka ku malo kuja kupita ku Beeriseba. |
720 | GEN 26:27 | Tsopano Isake anawafunsa kuti, “Bwanji mwabwera kwa ine, popeza munandichitira nkhanza ndi kundithamangitsa?” |
726 | GEN 26:33 | Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero. |
727 | GEN 26:34 | Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti. |
735 | GEN 27:7 | ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ |
754 | GEN 27:26 | Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.” |
776 | GEN 28:2 | Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. |
779 | GEN 28:5 | Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau. |
784 | GEN 28:10 | Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani. |
793 | GEN 28:19 | Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi. |
803 | GEN 29:7 | Iye anati, “Taonani, dzuwa likanalipo ndipo nthawi yosonkhanitsa nkhosa sinakwane. Bwanji osazimwetsa madzi nkhosazi.” |
821 | GEN 29:25 | Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?” |
825 | GEN 29:29 | Labani anapereka wantchito wake wamkazi Biliha kwa Rakele kuti akhale wantchito wake. |
834 | GEN 30:3 | Pamenepo Rakele anati kwa Yakobo, “Mdzakazi wanga Biliha nayu. Lowana naye kuti mwina nʼkundibalira mwana, ndipo kudzera mwa iyeyu nanenso nʼkukhala ndi ana.” |
835 | GEN 30:4 | Ndipo anamupatsa Yakobo wantchito wake Biliha kuti alowane naye. Choncho Yakobo analowana ndi Biliha, |
836 | GEN 30:5 | ndipo Bilihayo anatenga pathupi namubalira Yakobo mwana wamwamuna. |
838 | GEN 30:7 | Biliha, wantchito wa Rakele, anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. |
877 | GEN 31:3 | Pamenepo Yehova anati kwa Yakobo, “Bwerera ku dziko la makolo ako ndi kwa abale ako, ndipo Ine ndidzakhala nawe.” |
887 | GEN 31:13 | Ine ndine Mulungu amene ndinadza kwa iwe pa Beteli paja. Beteli ndi kumalo kuja kumene unayimika mwala ndi kuwudzoza mafuta, komanso kulumbira kwa Ine. Tsopano choka mʼdziko lino msanga ndi kubwerera ku dziko la kwanu.’ ” |
938 | GEN 32:10 | Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ |
1013 | GEN 35:1 | Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.” |
1015 | GEN 35:3 | Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” |
1018 | GEN 35:6 | Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani. |
1019 | GEN 35:7 | Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake. |
1020 | GEN 35:8 | Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro). |
1027 | GEN 35:15 | Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli. |
1028 | GEN 35:16 | Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka. |
1030 | GEN 35:18 | Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini. |
1031 | GEN 35:19 | Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu). |
1034 | GEN 35:22 | Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi. Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri: |
1036 | GEN 35:24 | Ana a Rakele ndi awa: Yosefe ndi Benjamini. |
1037 | GEN 35:25 | Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa: Dani ndi Nafutali. |
1044 | GEN 36:3 | ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti. |
1045 | GEN 36:4 | Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; |
1051 | GEN 36:10 | Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau. |
1054 | GEN 36:13 | Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau. |
1058 | GEN 36:17 | Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau. |
1068 | GEN 36:27 | Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. |
1073 | GEN 36:32 | Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba. |
1074 | GEN 36:33 | Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake. |
1076 | GEN 36:35 | Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti. |
1079 | GEN 36:38 | Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake. |
1080 | GEN 36:39 | Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. |
1086 | GEN 37:2 | Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake. |
1111 | GEN 37:27 | Bwanji timugulitse kwa Aismaeliwa, koma ife tisamuchite kanthu kalikonse. Ameneyu ndi mʼbale wathu thupi limodzi ndi ife.” Abale ake anavomereza zimenezi. |
1131 | GEN 38:11 | Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake. |
1132 | GEN 38:12 | Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo. |
1157 | GEN 39:7 | Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!” |
1180 | GEN 40:7 | Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?” |
1257 | GEN 42:4 | Koma Yakobo sanamulole Benjamini mngʼono wake wa Yosefe kuti apite nawo chifukwa anaopa kuti choyipa chingamuchitikire. |
1289 | GEN 42:36 | Abambo awo Yakobo anawawuza kuti, “Mwandilanda ana anga ine. Yosefe anamwalira ndipo Simeoni palibenso, ndiye tsopano mukufuna mutengenso Benjamini. Zonsezi zandigwera ine!” |
1297 | GEN 43:6 | Tsono Israeli anafunsa kuti, “Bwanji inu munandiputira mavuto oterewa pomuwuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?” |
1305 | GEN 43:14 | Ndipo Mulungu Wamphamvuzonse akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo kuti akamulole mʼbale wanu wina uja ndi Benjamini kuti abwerere ndi inu. Kukakhala kulira, ndine wolira basi.” |
1306 | GEN 43:15 | Choncho abale aja anatenga mphatso, ndalama zokwanira ndi Benjamininso. Iwo anafulumira kupita ku Igupto ndipo anakaonekera kwa Yosefe. |
1307 | GEN 43:16 | Yosefe ataona Benjamini ali pamodzi ndi abale ake, anati kwa wantchito wa mʼnyumba mwake, “Atengereni anthu awa ku nyumba kwanga, ndipo uphe nyama ndi kukonza bwino chakudya popeza amenewa adya ndi ine masana ano.” |
1320 | GEN 43:29 | Pomwazamwaza maso Yosefe anaona Benjamini, mʼbale wake weniweni wa bere limodzi, ndipo anafunsa, “Kodi uyu ndiye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri amene munkandiwuza uja?” Kenaka anati, “Ambuye akukomere mtima mwana wanga.” |
1325 | GEN 43:34 | Tsono ankawagawira chakudya kuchokera pa tebulo la Yosefe. Koma chakudya cha Benjamini chinkaposa cha ena onsewa kasanu. Motero anadya ndi kumwa mpaka kukhuta, ndipo anasangalala pamodzi ndi Yosefe. |
1329 | GEN 44:4 | Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? |