21 | GEN 1:21 | Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
51 | GEN 2:20 | Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. |
63 | GEN 3:7 | Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala. |
70 | GEN 3:14 | Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. |
73 | GEN 3:17 | Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’ “Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe, movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo masiku onse a moyo wako. |
86 | GEN 4:6 | Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? |
93 | GEN 4:13 | Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. |
145 | GEN 6:7 | Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.” |
149 | GEN 6:11 | Chiwawa chinadzaza pa dziko lapansi kotero kuti dziko linakhala lowonongeka pamaso pa Mulungu. |
153 | GEN 6:15 | Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. |
163 | GEN 7:3 | Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi. |
177 | GEN 7:17 | Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko. |
181 | GEN 7:21 | Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu. |
182 | GEN 7:22 | Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa. |
183 | GEN 7:23 | Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye. |
193 | GEN 8:9 | Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. |
194 | GEN 8:10 | Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. |
217 | GEN 9:11 | Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.” |
223 | GEN 9:17 | Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.” |
234 | GEN 9:28 | Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. |
265 | GEN 10:30 | Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa. |
275 | GEN 11:8 | Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. |
303 | GEN 12:4 | Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. |
306 | GEN 12:7 | Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe. |
317 | GEN 12:18 | Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? |
320 | GEN 13:1 | Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. |
330 | GEN 13:11 | Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. |
337 | GEN 13:18 | Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe. |
340 | GEN 14:3 | Mafumu onse anathiridwa nkhondowa anagwirizana pamodzi kupita ku Chigwa cha Sidimu (Nyanja ya Mchere). |
345 | GEN 14:8 | Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo |
347 | GEN 14:10 | Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri. |
354 | GEN 14:17 | Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu). |
388 | GEN 16:6 | Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa. |
389 | GEN 16:7 | Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri. |
431 | GEN 18:6 | Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.” |
437 | GEN 18:12 | Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, “Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba.” |
444 | GEN 18:19 | Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye.” |
454 | GEN 18:29 | Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.” |
456 | GEN 18:31 | Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?” Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.” |
457 | GEN 18:32 | Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.” |
471 | GEN 19:13 | chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.” |
472 | GEN 19:14 | Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. |
479 | GEN 19:21 | Mngeloyo anati kwa iye, “Chabwino, ndavomeranso pempho lako, sindiwononga mudzi ukunenawo. |
487 | GEN 19:29 | Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako. |
493 | GEN 19:35 | Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka. |
494 | GEN 19:36 | Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo. |
498 | GEN 20:2 | ndipo Abrahamu ankawawuza za Sara kuti, “Iyeyu ndi mlongo wanga.” Choncho Abimeleki, mfumu wa ku Gerari anamutenga Sara uja. |
501 | GEN 20:5 | Kodi Abrahamu sanandiwuze kuti iyeyu ndi mlongo wake? Ndiponso mkaziyu ankanena kuti Abrahamu ndi mlongo wake. Choncho ine pochita izi, ndinkachita moona mtima ndiponso mopanda chinyengo.” |
506 | GEN 20:10 | Ndipo Abrahamu anafunsa Abimeleki kuti, “Chifukwa chiyani wachita zimenezi?” |
521 | GEN 21:7 | Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.” |
531 | GEN 21:17 | Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. |
533 | GEN 21:19 | Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe. |
541 | GEN 21:27 | Choncho Abrahamu anabweretsa nkhosa ndi ngʼombe nazipereka kwa Abimeleki, ndipo anthu awiriwo anachita pangano. |
562 | GEN 22:14 | Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.” |
578 | GEN 23:6 | “Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.” |
583 | GEN 23:11 | nati, “Ayi mbuye wanga tandimverani, ine ndikukupatsani mundawo ndiponso phanga limene lili mʼmenemo. Ndikukupatsani malowa pamaso pa anthu a mtundu wanga. Chonde ikani mtembo wamkazi wanu.” |
589 | GEN 23:17 | Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa |
592 | GEN 23:20 | Choncho Ahiti anapereka munda pamodzi ndi phanga la mʼmenemo kwa Abrahamu kuti akhale manda. |
601 | GEN 24:9 | Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu. |
606 | GEN 24:14 | Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. |
609 | GEN 24:17 | Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.” |
612 | GEN 24:20 | Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse. |
615 | GEN 24:23 | Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?” |
617 | GEN 24:25 | Ndipo anapitiriza kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chilipo kwathu ndipo malo woti mugone aliponso.” |
624 | GEN 24:32 | Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse. |
625 | GEN 24:33 | Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.” Labani anati, “Yankhulani.” |
637 | GEN 24:45 | “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’ |
648 | GEN 24:56 | Koma iye anawawuza kuti, “Chonde musandichedwetse. Yehova wandithandiza kale pa ulendo wanga. Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.” |
650 | GEN 24:58 | Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?” Iye anayankha kuti, “Ndipita.” |
653 | GEN 24:61 | Kenaka Rebeka ndi antchito ake ananyamuka kukakwera ngamira zawo ndipo anapita naye pamodzi munthu uja. Choncho wantchito uja anatenga Rebeka nʼkumapita. |
657 | GEN 24:65 | nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?” Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso. |
677 | GEN 25:18 | Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo. |
681 | GEN 25:22 | Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova. |
690 | GEN 25:31 | Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.” |
691 | GEN 25:32 | Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?” |
693 | GEN 25:34 | Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita. Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja. |
696 | GEN 26:3 | Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako. |
699 | GEN 26:6 | Choncho Isake anakhala ku Gerari. |
702 | GEN 26:9 | Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.” |
704 | GEN 26:11 | Choncho Abimeleki analamula anthu ake onse nati, “Aliyense amene avutitse munthu uyu pamodzi ndi mkazi wake adzaphedwa ndithu.” |
706 | GEN 26:13 | Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. |
710 | GEN 26:17 | Choncho Isake anachokako kumeneko nakakhala ku chigwa cha Gerari kumene anakhazikikako. |
714 | GEN 26:21 | Kenaka iwo anakumba chitsime china, koma anakangananso chifukwa cha chitsimecho. Choncho anachitcha dzina lakuti Chidani. |
742 | GEN 27:14 | Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera. |
747 | GEN 27:19 | Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.” |
755 | GEN 27:27 | Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati, “Haa, fungo la mwana wanga lili ngati fungo la munda umene Yehova waudalitsa. |
759 | GEN 27:31 | Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.” |
774 | GEN 27:46 | Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.” |
775 | GEN 28:1 | Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani. |
808 | GEN 29:12 | Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake. |
816 | GEN 29:20 | Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele. |
821 | GEN 29:25 | Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?” |
831 | GEN 29:35 | Anatenganso pathupi pena, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna, iye anati, “Nthawi ino ndidzalemekeza Yehova.” Choncho anamutcha Yuda. Kenaka analeka kubereka. |
832 | GEN 30:1 | Rakele ataona kuti sakumuberekera Yakobo ana, anayamba kumuchitira nsanje mʼbale wake. Choncho anati kwa Yakobo, “Undipatse ana kapena apo ayi ndingofa!” |
835 | GEN 30:4 | Ndipo anamupatsa Yakobo wantchito wake Biliha kuti alowane naye. Choncho Yakobo analowana ndi Biliha, |
837 | GEN 30:6 | Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani. |