2 | GEN 1:2 | Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. |
11 | GEN 1:11 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. |
12 | GEN 1:12 | Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
24 | GEN 1:24 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
42 | GEN 2:11 | Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
101 | GEN 4:21 | Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. |
242 | GEN 10:7 | Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani. |
260 | GEN 10:25 | A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. |
262 | GEN 10:27 | Hadoramu, Uzali, Dikila, |
296 | GEN 11:29 | Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. |
334 | GEN 13:15 | Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya. |
336 | GEN 13:17 | Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.” |
351 | GEN 14:14 | Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. |
352 | GEN 14:15 | Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko. |
363 | GEN 15:2 | Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko? |
378 | GEN 15:17 | Dzuwa litalowa ndipo mdima utagwa, panaoneka mʼphika wofuka nthunzi ya moto ndi sakali yoyaka ndipo zinadutsa pakati pa zidutswa za nyama zija. |
406 | GEN 17:8 | Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.” |
511 | GEN 20:15 | Tsono Abimeleki anati kwa Abrahamu, “Dziko langa ndi limene ukulionali; ukhale paliponse pamene ufuna.” |
662 | GEN 25:3 | Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. |
673 | GEN 25:14 | Misima, Duma, Masa, |
837 | GEN 30:6 | Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani. |
852 | GEN 30:21 | Patapita nthawi Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha Dina. |
914 | GEN 31:40 | Moyo wanga unali wotere: Dzuwa limanditentha masana ndipo usiku ndimazunzika ndi kuzizira. Tulo sindimalipeza konse. |
957 | GEN 32:29 | Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.” |
960 | GEN 32:32 | Dzuwa linamutulukira Yakobo pamene amachoka pa Penueli. Tsono ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyungʼunyu yake ija. |
982 | GEN 34:1 | Tsopano Dina, mwana amene Leya anaberekera Yakobo, anapita kukacheza ndi akazi ena a mʼdzikolo. |
984 | GEN 34:3 | Koma Sekemu anamukondadi namwali uja, Dina, mwana wa Yakobo motero kuti anamuyankhula mawu womutonthoza. |
986 | GEN 34:5 | Yakobo anamva kuti mwana wake Dina wagwiriridwa, koma sanachitepo kanthu msanga kudikira mpaka ana ake amuna omwe anali ku busa atabwerako. |
988 | GEN 34:7 | Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo. |
992 | GEN 34:11 | Pamenepo Sekemu anati kwa abambo ndi alongo ake a Dina, “Inu mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani chilichonse munganene. |
994 | GEN 34:13 | Ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi abambo ake, Hamori mwachinyengo chifukwa mlongo wawo, Dina anali atayipitsidwa. |
1002 | GEN 34:21 | Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi. |
1006 | GEN 34:25 | Patapita masiku atatu, amuna onse akumvabe ululu wa kuchita mdulidwe uja, ana awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, anatenga malupanga ndi kulowa mu mzindawo mwakachetechete napha amuna onse. |
1007 | GEN 34:26 | Anapha Hamori ndi Sekemu. Anakatenga Dina ku nyumba kwa Sekemu nanyamuka. |
1020 | GEN 35:8 | Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro). |
1022 | GEN 35:10 | Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli. |
1024 | GEN 35:12 | Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.” |
1037 | GEN 35:25 | Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa: Dani ndi Nafutali. |
1062 | GEN 36:21 | Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori. |
1066 | GEN 36:25 | Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi. |
1067 | GEN 36:26 | Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. |
1069 | GEN 36:28 | Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani. |
1071 | GEN 36:30 | Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri. |
1073 | GEN 36:32 | Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba. |
1101 | GEN 37:17 | Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’ ” Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani. |
1402 | GEN 46:15 | Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33. |
1410 | GEN 46:23 | Mwana wa mwamuna wa Dani anali: Husimu. |
1427 | GEN 47:6 | Dziko lonse la Igupto lili mʼdzanja lako. Uwakhazike abambo ako ndi abale ako mʼmalo achonde kwambiri. Akhale ku Goseni. Ndipo ngati ukudziwapo ena mwa iwo amene ali akatswiri pa kuweta ziweto, uwapatse udindo woyangʼanira ziweto zanga.” |
1441 | GEN 47:20 | Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao, |
1490 | GEN 49:16 | “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli. |
1491 | GEN 49:17 | Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu, songo yokhala mʼnjira imene imaluma chidendene cha kavalo kuti wokwerapoyo agwe chagada. |
1494 | GEN 49:20 | “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma, ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu. |
1537 | EXO 1:4 | Dani, Nafutali; Gadi ndi Aseri. |
1593 | EXO 3:13 | Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” |
1594 | EXO 3:14 | Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” |
1783 | EXO 10:5 | Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu. |
1784 | EXO 10:6 | Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao. |
1792 | EXO 10:14 | Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo. |
1793 | EXO 10:15 | Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto. |
2427 | EXO 31:6 | Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi: |
2452 | EXO 32:13 | Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ” |
2566 | EXO 35:34 | Ndipo Iye wapereka kwa Bezaleli pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani luso lophunzitsa ena. |
2657 | EXO 38:23 | pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala. |
3458 | LEV 24:11 | Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. |
3558 | LEV 26:33 | Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. |
3563 | LEV 26:38 | Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. |
3617 | NUM 1:12 | Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani, |
3619 | NUM 1:14 | Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi, |
3643 | NUM 1:38 | Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
3644 | NUM 1:39 | Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700. |
3673 | NUM 2:14 | Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli. |
3684 | NUM 2:25 | Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai. |
3690 | NUM 2:31 | Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. |
3893 | NUM 7:42 | Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake. |
3898 | NUM 7:47 | ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli. |
3917 | NUM 7:66 | Pa tsiku lakhumi Ahiyezeri mwana wa Amisadai, mtsogoleri wa fuko la Dani anabweretsa chopereka chake. |
3974 | NUM 9:8 | Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.” |
4009 | NUM 10:20 | ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. |
4014 | NUM 10:25 | Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. |
4024 | NUM 10:35 | Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu. |
4088 | NUM 13:12 | kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali; |
4103 | NUM 13:27 | Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi. |
4108 | NUM 13:32 | Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali. |
4116 | NUM 14:7 | ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, “Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi. |
4117 | NUM 14:8 | Ngati Yehova akukondwera nafe, adzatitsogolera kulowa mʼdziko limenelo. Dziko loyenda mkaka ndi uchi adzalipereka kwa ife, |
4196 | NUM 16:1 | Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza, |
4207 | NUM 16:12 | Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! |
4219 | NUM 16:24 | “Uza gulu lonse kuti, ‘Khalani kutali ndi matenti a Kora, Datani ndi Abiramu.’ ” |
4220 | NUM 16:25 | Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. |
4222 | NUM 16:27 | Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo. |
4371 | NUM 21:30 | “Koma ife tawagonjetsa; Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni. Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa, mzinda womwe umafika ku Medeba. |
4486 | NUM 25:14 | Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni. |