Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   E    February 11, 2023 at 19:19    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

39  GEN 2:8  Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja.
41  GEN 2:10  Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi.
46  GEN 2:15  Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira.
79  GEN 3:23  Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera.
80  GEN 3:24  Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
96  GEN 4:16  Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.
97  GEN 4:17  Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki.
98  GEN 4:18  Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki.
106  GEN 4:26  Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi. Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.
112  GEN 5:6  Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
113  GEN 5:7  Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
115  GEN 5:9  Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.
116  GEN 5:10  Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
117  GEN 5:11  Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
124  GEN 5:18  Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.
125  GEN 5:19  Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
127  GEN 5:21  Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.
128  GEN 5:22  Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
129  GEN 5:23  Zaka zonse za Enoki zinali 365.
130  GEN 5:24  Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
239  GEN 10:4  Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
245  GEN 10:10  Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
256  GEN 10:21  Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
257  GEN 10:22  Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
259  GEN 10:24  Aripakisadi anabereka Sela, ndipo Selayo anabereka Eberi.
260  GEN 10:25  A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
281  GEN 11:14  Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi.
282  GEN 11:15  Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
283  GEN 11:16  Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi.
284  GEN 11:17  Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
318  GEN 12:19  Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!”
338  GEN 14:1  Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu
343  GEN 14:6  amene ankakhala ku Ahori, ku dziko la mapiri la Seiri mpaka ku Eli Parani kufupi ndi chipululu.
344  GEN 14:7  Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara.
346  GEN 14:9  Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu.
350  GEN 14:13  Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu.
361  GEN 14:24  Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
363  GEN 15:2  Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko?
549  GEN 22:1  Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!” Ndipo iye anayankha kuti,Ee Ambuye.”
555  GEN 22:7  Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?” Abrahamu anayankha,Ee mwana wanga.” Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”
559  GEN 22:11  Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!” Iye anayankha kuti,Ee Ambuye.”
580  GEN 23:8  nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari
582  GEN 23:10  Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu
585  GEN 23:13  ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.”
586  GEN 23:14  Koma Efroni anamuyankha Abrahamu nati,
588  GEN 23:16  Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.
589  GEN 23:17  Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa
663  GEN 25:4  Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
668  GEN 25:9  Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti,
684  GEN 25:25  Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau.
685  GEN 25:26  Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
686  GEN 25:27  Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba.
687  GEN 25:28  Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.
688  GEN 25:29  Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala.
689  GEN 25:30  Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).
691  GEN 25:32  Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?”
692  GEN 25:33  Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.
693  GEN 25:34  Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita. Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.
727  GEN 26:34  Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti.
729  GEN 27:1  Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.” Iye anayankha, “Ine abambo.”
733  GEN 27:5  Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama,
734  GEN 27:6  Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti,
739  GEN 27:11  Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala.
743  GEN 27:15  Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo.
746  GEN 27:18  Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.” Ndipo anayankha,Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”
747  GEN 27:19  Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”
749  GEN 27:21  Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”
750  GEN 27:22  Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.”
751  GEN 27:23  Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa.
752  GEN 27:24  Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
758  GEN 27:30  Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja.
760  GEN 27:32  Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?” Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
762  GEN 27:34  Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”
764  GEN 27:36  Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”
766  GEN 27:38  Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
769  GEN 27:41  Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”
770  GEN 27:42  Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire.
779  GEN 28:5  Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau.
780  GEN 28:6  Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.”
782  GEN 28:8  Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani;
885  GEN 31:11  Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, ‘Yakobo.’ Ine ndinayankha,Ee, Ambuye.’
932  GEN 32:4  Yakobo anatumiza amithenga ake kwa mʼbale wake Esau ku dera la Seiri, dziko la Edomu.
933  GEN 32:5  Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano.
935  GEN 32:7  Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.”
937  GEN 32:9  Mʼmaganizo ake iye ankanena kuti, “Ngati Esau atabwera ndi kuthira nkhondo gulu limodzi, gulu lina lotsalalo likhoza kupulumuka.”
940  GEN 32:12  Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe.
942  GEN 32:14  Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake:
946  GEN 32:18  Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’
947  GEN 32:19  Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ”
948  GEN 32:20  Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye.
962  GEN 33:1  Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja.
965  GEN 33:4  Koma Esau anathamanga kukakumana ndi Yakobo ndipo anamukupatira namupsompsona. Onse awiri ankangolira.
966  GEN 33:5  Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?” Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”
969  GEN 33:8  Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?” Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.”