94 | GEN 4:14 | Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.” |
98 | GEN 4:18 | Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki. |
99 | GEN 4:19 | Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. |
103 | GEN 4:23 | Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. |
104 | GEN 4:24 | Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.” |
131 | GEN 5:25 | Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. |
132 | GEN 5:26 | Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
134 | GEN 5:28 | Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. |
136 | GEN 5:30 | Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
137 | GEN 5:31 | Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira. |
161 | GEN 7:1 | Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu. |
173 | GEN 7:13 | Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo. |
254 | GEN 10:19 | mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. |
257 | GEN 10:22 | Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. |
294 | GEN 11:27 | Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. |
298 | GEN 11:31 | Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. |
303 | GEN 12:4 | Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. |
304 | GEN 12:5 | Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. |
320 | GEN 13:1 | Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. |
324 | GEN 13:5 | Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. |
326 | GEN 13:7 | Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo. |
327 | GEN 13:8 | Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. |
329 | GEN 13:10 | Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). |
330 | GEN 13:11 | Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. |
331 | GEN 13:12 | Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. |
333 | GEN 13:14 | Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. |
349 | GEN 14:12 | Anatenganso Loti, mwana wa mʼbale wake wa Abramu pamodzi ndi katundu wake popeza ankakhala mu Sodomu. |
351 | GEN 14:14 | Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. |
353 | GEN 14:16 | Ndipo anawalanda katundu wawo yense nabwera naye Loti, katundu wake yense, pamodzi ndi akazi ndi anthu ena. |
459 | GEN 19:1 | Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu. |
462 | GEN 19:4 | Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti. |
463 | GEN 19:5 | Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.” |
464 | GEN 19:6 | Loti anatuluka panja kukakumana nawo natseka chitseko |
467 | GEN 19:9 | Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. |
468 | GEN 19:10 | Koma anthu aja anali mʼkatiwa anasuzumira namukokera Loti uja mʼkati mwa nyumba nʼkutseka chitseko. |
470 | GEN 19:12 | Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno, |
472 | GEN 19:14 | Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. |
473 | GEN 19:15 | Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.” |
474 | GEN 19:16 | Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo. |
476 | GEN 19:18 | Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero! |
481 | GEN 19:23 | Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka. |
484 | GEN 19:26 | Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere. |
487 | GEN 19:29 | Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako. |
488 | GEN 19:30 | Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga. |
494 | GEN 19:36 | Choncho ana onse awiri a Loti aja anatenga pathupi pa abambo awo. |
544 | GEN 21:30 | Iye anayankha kuti, “Landirani ana ankhosa aakazi kuchokera mʼdzanja langa ngati umboni kuti ndinakumba chitsime ichi.” |
585 | GEN 23:13 | ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.” |
621 | GEN 24:29 | Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani. |
624 | GEN 24:32 | Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse. |
625 | GEN 24:33 | Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.” Labani anati, “Yankhulani.” |
642 | GEN 24:50 | Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu. |
679 | GEN 25:20 | ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu. |
692 | GEN 25:33 | Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo. |
771 | GEN 27:43 | Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. |
776 | GEN 28:2 | Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. |
779 | GEN 28:5 | Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau. |
793 | GEN 28:19 | Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi. |
801 | GEN 29:5 | Iye anawafunsanso kuti, “Kodi Labani, mdzukulu wa Nahori mukumudziwa?” Iwo anayankha, “Inde tikumudziwa?” |
806 | GEN 29:10 | Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo. |
809 | GEN 29:13 | Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika. |
810 | GEN 29:14 | Ndipo, Labani anati kwa iye, “Iwe ndiwe ndithu fupa ndi mnofu wanga.” Yakobo anakhala ndi Labani mwezi umodzi. |
811 | GEN 29:15 | Tsono Labani anawuza Yakobo kuti, “Zoona iwe ndi ife ndi abale. Koma suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro. Ndiwuze kuti malipiro ako azikhala wotani?” |
812 | GEN 29:16 | Tsono Labani anali ndi ana aakazi awiri; dzina la wamkulu linali Leya, ndipo dzina la wamngʼono linali Rakele. |
813 | GEN 29:17 | Leya anali ndi maonekedwe wofowoka koma Rakele anali wa maonekedwe wokongola kwambiri. |
815 | GEN 29:19 | Labani anati, “Kuli bwino kuti ndimupereke kwa iwe ameneyu kusiyana ndi munthu wina. Khala ndi ine kuno.” |
817 | GEN 29:21 | Kenaka Yakobo anati kwa Labani, “Nthawi yanga ndakwanitsa, ndipatseni mwana wanu kuti ndimukwatire.” |
818 | GEN 29:22 | Pamenepo Labani anakonza phwando la ukwati, nayitana anthu onse a pamalopo. |
819 | GEN 29:23 | Koma pokwana usiku, Labani anatenga mwana wake wamkazi Leya namupatsa Yakobo, ndipo Yakobo anagona naye. |
820 | GEN 29:24 | Ndipo Labani anapereka wantchito wake wamkazi Zilipa kwa Leya kuti akhale wantchito wake. |
821 | GEN 29:25 | Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?” |
822 | GEN 29:26 | Labani anayankha, “Si mwambo wathu kuno kupereka wamngʼono ku banja, wamkulu asanakwatiwe. |
823 | GEN 29:27 | Yamba watsiriza sabata ya chikondwerero cha ukwati wa Leya; kenaka ndidzakupatsanso Rakele. Koma udzayenera kundigwirira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri.” |
824 | GEN 29:28 | Yakobo anachitadi momwemo. Anamaliza sabata ya chikondwerero cha Leya, ndipo Labani anamupatsa Rakele kuti akhale mkazi wake. |
825 | GEN 29:29 | Labani anapereka wantchito wake wamkazi Biliha kwa Rakele kuti akhale wantchito wake. |
826 | GEN 29:30 | Yakobo analowana ndi mkazi wake Rakele, ndipo Yakobo anakonda Rakele kuposa Leya. Ndipo anamugwirira ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. |
827 | GEN 29:31 | Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala. |
828 | GEN 29:32 | Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.” |
830 | GEN 29:34 | Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi. |
834 | GEN 30:3 | Pamenepo Rakele anati kwa Yakobo, “Mdzakazi wanga Biliha nayu. Lowana naye kuti mwina nʼkundibalira mwana, ndipo kudzera mwa iyeyu nanenso nʼkukhala ndi ana.” |
840 | GEN 30:9 | Pamene Leya anaona kuti waleka kubereka ana, iye anatenga wantchito wake Zilipa namupereka kwa Yakobo kuti alowane naye. |
841 | GEN 30:10 | Zilipa, wantchito wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. |
842 | GEN 30:11 | Pamenepo Leya anati, “Mwayi wangawo!” Choncho anamutcha Gadi. |
843 | GEN 30:12 | Zilipa, wantchito wa Leya anamubalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. |
844 | GEN 30:13 | Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri. |
845 | GEN 30:14 | Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni anapita ku munda ndipo anapezako zipatso za mankhwala wobereketsa. Tsono anatengerako mayi wake Leya. Rakele anati kwa Leya, “Chonde patseko mankhwala wakupezera mwana wakowo.” |
847 | GEN 30:16 | Choncho pamene Yakobo ankabwera kuchokera ku munda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nati, “Lero mukagona ku nyumba chifukwa ndakubwerekani ndi mankhwala wobereketsa a mwana wanga.” Choncho usiku umenewo Yakobo anakalowa kwa Leya. |
848 | GEN 30:17 | Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anatenga pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu. |
849 | GEN 30:18 | Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa chopereka wantchito wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho anamutcha Isakara. |
850 | GEN 30:19 | Leya anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu ndi chimodzi. |
851 | GEN 30:20 | Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni. |
852 | GEN 30:21 | Patapita nthawi Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha Dina. |
856 | GEN 30:25 | Rakele atabereka Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, “Ndimasuleni kuti ndizipita ku dziko la kwathu. |
858 | GEN 30:27 | Koma Labani anati kwa iye, “Chonde, ngati mungandikomere mtima musapite chifukwa ndadziwa kudzera mwa kuwombeza kwanga kuti Yehova wandidalitsa chifukwa cha inu.” |