26 | GEN 1:26 | Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” |
62 | GEN 3:6 | Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. |
99 | GEN 4:19 | Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. |
102 | GEN 4:22 | Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
103 | GEN 4:23 | Lameki anawuza akazi akewo kuti, “Ada ndi Zila, ndimvereni; inu akazi anga imvani mawu anga. Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya. |
111 | GEN 5:5 | Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira. |
114 | GEN 5:8 | Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira. |
117 | GEN 5:11 | Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira. |
120 | GEN 5:14 | Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira. |
123 | GEN 5:17 | Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira. |
126 | GEN 5:20 | Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira. |
129 | GEN 5:23 | Zaka zonse za Enoki zinali 365. |
133 | GEN 5:27 | Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira. |
137 | GEN 5:31 | Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira. |
254 | GEN 10:19 | mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. |
329 | GEN 13:10 | Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). |
339 | GEN 14:2 | anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). |
342 | GEN 14:5 | Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu |
345 | GEN 14:8 | Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo |
362 | GEN 15:1 | Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati: “Usaope Abramu. Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yayikulu.” |
430 | GEN 18:5 | Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.” Ndipo iwo anamuyankha nati, “Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.” |
480 | GEN 19:22 | Koma uthawireko mofulumira chifukwa sindichita kena kalikonse mpaka utafikako.” (Nʼchifukwa chake mudziwo unatchedwa Zowari). |
481 | GEN 19:23 | Pamene Loti amafika ku Zowari, nʼkuti dzuwa litatuluka. |
488 | GEN 19:30 | Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga. |
565 | GEN 22:17 | ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, |
580 | GEN 23:8 | nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari |
591 | GEN 23:19 | Zitatha izi, Abrahamu anayika mkazi wake Sara mʼphanga la mʼmunda wa ku Makipela, kufupi ndi ku Mamre (kumene ndi ku Hebroni) mʼdziko la Kanaani. |
606 | GEN 24:14 | Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. |
661 | GEN 25:2 | Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. |
668 | GEN 25:9 | Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti, |
677 | GEN 25:18 | Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo. |
697 | GEN 26:4 | Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako, |
788 | GEN 28:14 | Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. |
790 | GEN 28:16 | Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.” |
791 | GEN 28:17 | Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.” |
804 | GEN 29:8 | Iwo anayankha, “Ayi sitingatero. Tidikira mpaka nkhosa zonse zisonkhane. Zikatero, tigubuduza mwalawu kuwuchotsa pamwamba pa chitsimepo, kenaka nʼkuzimwetsa madzi nkhosazo.” |
811 | GEN 29:15 | Tsono Labani anawuza Yakobo kuti, “Zoona iwe ndi ife ndi abale. Koma suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro. Ndiwuze kuti malipiro ako azikhala wotani?” |
820 | GEN 29:24 | Ndipo Labani anapereka wantchito wake wamkazi Zilipa kwa Leya kuti akhale wantchito wake. |
828 | GEN 29:32 | Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.” |
840 | GEN 30:9 | Pamene Leya anaona kuti waleka kubereka ana, iye anatenga wantchito wake Zilipa namupereka kwa Yakobo kuti alowane naye. |
841 | GEN 30:10 | Zilipa, wantchito wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. |
843 | GEN 30:12 | Zilipa, wantchito wa Leya anamubalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. |
851 | GEN 30:20 | Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni. |
863 | GEN 30:32 | Mundilole ndiyendeyende pakati pa ziweto zanu lero ndi kuchotsamo mwana wankhosa wamkazi aliyense wakuda, mbuzi iliyonse yamathothomathotho ndi yamawangamawanga. Zimenezi ndiye zikhale malipiro anga. |
882 | GEN 31:8 | Pamene abambo anu anati, ‘Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, ‘Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi. |
915 | GEN 31:41 | Zinthu zinali chonchi kwa zaka makumi awiri zimene ndinali mʼnyumba mwanu. Ndinakugwirirani ntchito kwa zaka khumi ndi zinayi chifukwa cha ana anu aakazi awiri ndipo zaka zina zisanu ndi chimodzi chifukwa cha ziweto zanu, ndipo munandisinthira malipiro kakhumi konse. |
917 | GEN 31:43 | Labani anayankha Yakobo nati, “Ana aakaziwa ndi anga, ana awo ndi anganso. Ziwetozi ndi zanga. Chilichonse ukuona apa ndi changa. Koma tsopano ndingachite chiyani ndi ana anga aakaziwa kapena ndi ana awo? |
933 | GEN 32:5 | Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. |
947 | GEN 32:19 | Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” |
970 | GEN 33:9 | Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.” |
1010 | GEN 34:29 | Anawatengera chuma chawo chonse, akazi ndi ana awo, pamodzi ndi zonse zimene zinapezeka mʼnyumba zawo. Zonsezi zinayesedwa ngati zolandidwa ku nkhondo. |
1035 | GEN 35:23 | Ana a Leya ndi awa: Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni. |
1038 | GEN 35:26 | Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa: Gadi ndi Aseri. Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu. |
1043 | GEN 36:2 | Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi |
1052 | GEN 36:11 | Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. |
1054 | GEN 36:13 | Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau. |
1055 | GEN 36:14 | Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora. |
1056 | GEN 36:15 | Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, |
1058 | GEN 36:17 | Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau. |
1061 | GEN 36:20 | Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
1065 | GEN 36:24 | Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni. |
1068 | GEN 36:27 | Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. |
1070 | GEN 36:29 | Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
1074 | GEN 36:33 | Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake. |
1080 | GEN 36:39 | Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. |
1086 | GEN 37:2 | Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake. |
1130 | GEN 38:10 | Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa. |
1150 | GEN 38:30 | Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera. |
1225 | GEN 41:29 | Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zikubwera mu dziko lonse la Igupto, |
1227 | GEN 41:31 | Zakudya zochuluka za mʼdzikomo zija sizidzakumbukirikanso chifukwa njala imene iti idzabwereyo idzakhala yoopsa. |
1241 | GEN 41:45 | Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto. |
1246 | GEN 41:50 | Zisanafike zaka zanjala, Yosefe anabereka ana aamuna awiri mwa Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni. |
1249 | GEN 41:53 | Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zija zinatha, |
1289 | GEN 42:36 | Abambo awo Yakobo anawawuza kuti, “Mwandilanda ana anga ine. Yosefe anamwalira ndipo Simeoni palibenso, ndiye tsopano mukufuna mutengenso Benjamini. Zonsezi zandigwera ine!” |
1397 | GEN 46:10 | Ana aamuna a Simeoni ndi awa: Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani. |
1399 | GEN 46:12 | Ana aamuna a Yuda ndi awa: Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani. Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli. |
1401 | GEN 46:14 | Ana aamuna a Zebuloni ndi awa: Seredi, Eloni ndi Yahaleeli. |
1403 | GEN 46:16 | Ana aamuna a Gadi ndi awa: Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli. |
1405 | GEN 46:18 | Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16. |
1430 | GEN 47:9 | Yakobo anayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga.” |
1445 | GEN 47:24 | Koma podzakolola, mudzapereka gawo limodzi la magawo asanu aliwonse kwa Farao. Magawo anayi enawo adzakhala anu. Zina mudzasunge mbewu ndi zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi ana anu.” |
1487 | GEN 49:13 | “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja; adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi; malire ake adzafika ku Sidoni. |
1500 | GEN 49:26 | Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa madalitso a mapiri akale oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona. Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe, pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake. |
1524 | GEN 50:17 | ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira. |
1536 | EXO 1:3 | Isakara, Zebuloni, Benjamini; |
1576 | EXO 2:21 | Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake. |
1577 | EXO 2:22 | Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.” |
1600 | EXO 3:20 | Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite. |
1627 | EXO 4:25 | Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.” |
1628 | EXO 4:26 | Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe. |
1634 | EXO 5:1 | Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ” |
1671 | EXO 6:15 | Ana a Simeoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Saulo mwana wa kwa mkazi wa Chikanaani. Awa anali mafuko a Simeoni. |
1677 | EXO 6:21 | Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri. |
1749 | EXO 9:6 | Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. |
1788 | EXO 10:10 | Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa. |
1808 | EXO 11:1 | Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani. |