1 | GEN 1:1 | Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
2 | GEN 1:2 | Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. |
3 | GEN 1:3 | Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
4 | GEN 1:4 | Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima. |
5 | GEN 1:5 | Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba. |
6 | GEN 1:6 | Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” |
7 | GEN 1:7 | Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi. |
8 | GEN 1:8 | Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri. |
9 | GEN 1:9 | Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. |
10 | GEN 1:10 | Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
11 | GEN 1:11 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. |
12 | GEN 1:12 | Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
14 | GEN 1:14 | Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; |
16 | GEN 1:16 | Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. |
17 | GEN 1:17 | Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi, |
18 | GEN 1:18 | kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
20 | GEN 1:20 | Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.” |
21 | GEN 1:21 | Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
22 | GEN 1:22 | Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.” |
24 | GEN 1:24 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. |
25 | GEN 1:25 | Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
26 | GEN 1:26 | Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” |
27 | GEN 1:27 | Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi. |
28 | GEN 1:28 | Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.” |
29 | GEN 1:29 | Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu. |
30 | GEN 1:30 | Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi. |
31 | GEN 1:31 | Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi. |
32 | GEN 2:1 | Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo. |
33 | GEN 2:2 | Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. |
34 | GEN 2:3 | Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira. |
35 | GEN 2:4 | Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba, |
36 | GEN 2:5 | zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka, |
38 | GEN 2:7 | Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. |
39 | GEN 2:8 | Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. |
40 | GEN 2:9 | Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa. |
41 | GEN 2:10 | Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi. |
42 | GEN 2:11 | Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni; uwu umazungulira dziko lonse la Havila, kumene kuli golide. |
43 | GEN 2:12 | (Golide wa ku dziko ili ndi wabwino. Kulinso miyala yokongola ya bedola ndi onikisi). |
44 | GEN 2:13 | Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
45 | GEN 2:14 | Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigirisi; umayenda chakummawa kwa Asiriya. Ndipo mtsinje wachinayi ndi Yufurate. |
46 | GEN 2:15 | Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira. |
47 | GEN 2:16 | Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu; |
48 | GEN 2:17 | koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.” |
49 | GEN 2:18 | Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.” |
50 | GEN 2:19 | Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. |
51 | GEN 2:20 | Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. |
52 | GEN 2:21 | Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. |
53 | GEN 2:22 | Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye. |