| 1 | GEN 1:1 | Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
| 2 | GEN 1:2 | Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. |
| 3 | GEN 1:3 | Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. |
| 4 | GEN 1:4 | Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima. |
| 5 | GEN 1:5 | Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba. |
| 6 | GEN 1:6 | Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” |
| 7 | GEN 1:7 | Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi. |
| 8 | GEN 1:8 | Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri. |
| 9 | GEN 1:9 | Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. |
| 10 | GEN 1:10 | Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
| 11 | GEN 1:11 | Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. |
| 12 | GEN 1:12 | Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
| 13 | GEN 1:13 | Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu. |
| 14 | GEN 1:14 | Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; |