Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   n    February 11, 2023 at 19:19    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

1  GEN 1:1  Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.
2  GEN 1:2  Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
3  GEN 1:3  Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.
4  GEN 1:4  Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.
5  GEN 1:5  Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
6  GEN 1:6  Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
7  GEN 1:7  Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
8  GEN 1:8  Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
9  GEN 1:9  Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
10  GEN 1:10  Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
11  GEN 1:11  Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
12  GEN 1:12  Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
13  GEN 1:13  Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu.
14  GEN 1:14  Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;