549 | GEN 22:1 | Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!” Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” |
1239 | GEN 41:43 | Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto. |
5602 | DEU 27:15 | “Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5603 | DEU 27:16 | “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5604 | DEU 27:17 | “Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5605 | DEU 27:18 | “Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5606 | DEU 27:19 | “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5607 | DEU 27:20 | “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5608 | DEU 27:21 | “Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5609 | DEU 27:22 | “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5610 | DEU 27:23 | “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5611 | DEU 27:24 | “Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5612 | DEU 27:25 | “Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
5613 | DEU 27:26 | “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” |
7284 | 1SA 3:6 | Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.” Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” |
8236 | 2SA 9:6 | Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.” |
8504 | 2SA 18:23 | Iye anati, “Zivute zitani ine ndikufuna kuti ndipite.” Choncho Yowabu anati “Pita!” Ndipo Ahimaazi anathamanga kudzera njira ya ku chigwa ndipo anamupitirira Mkusi uja. |
9191 | 1KI 13:4 | Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza. |
9787 | 2KI 9:27 | Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko. |
14334 | PSA 29:9 | Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!” |
15766 | PSA 106:48 | Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, Kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Ameni!” Tamandani Yehova. |
22302 | HOS 10:8 | Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa. Ili ndiye tchimo la Israeli. Minga ndi mitungwi zidzamera ndi kuphimba maguwa awo ansembe. Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!” ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!” |
23446 | MAT 8:32 | Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. |
24220 | MAT 27:22 | Pilato anafunsa kuti, “Nanga ndichite chiyani ndi Yesu wotchedwa Khristu?” Onse anayankha kuti “Mpachikeni!” |
24221 | MAT 27:23 | Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?” Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!” |
24566 | MRK 7:34 | Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, “Efataa!” (Kutanthauza kuti, “Tsekuka!”) |
24888 | MRK 14:65 | Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya. |
24908 | MRK 15:13 | Anafuwula kuti, “Mpachikeni!” |
24909 | MRK 15:14 | Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!” |
26952 | JHN 20:16 | Yesu anati kwa iye, “Mariya.” Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi). |
27069 | ACT 3:4 | Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” |
27295 | ACT 9:10 | Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!” Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.” |
27493 | ACT 14:10 | Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda. |
30862 | REV 6:1 | Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” |
30864 | REV 6:3 | Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!” |
30866 | REV 6:5 | Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake. |
30868 | REV 6:7 | Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!” |
31040 | REV 16:17 | Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” |
31166 | REV 22:17 | Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo. |