22 | GEN 1:22 | Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.” |
28 | GEN 1:28 | Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.” |
200 | GEN 8:16 | “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. |
390 | GEN 16:8 | Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.” |
417 | GEN 17:19 | Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. |
431 | GEN 18:6 | Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.” |
460 | GEN 19:2 | Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.” |
472 | GEN 19:14 | Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. |
473 | GEN 19:15 | Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.” |
476 | GEN 19:18 | Koma Loti anawawuza kuti, “Ayi, ambuye anga chonde musatero! |
479 | GEN 19:21 | Mngeloyo anati kwa iye, “Chabwino, ndavomeranso pempho lako, sindiwononga mudzi ukunenawo. |
500 | GEN 20:4 | Nthawi imeneyi nʼkuti Abimeleki asanamukhudze mkaziyo, kotero kuti anati, “Ambuye, kodi mudzawonongadi mtundu wolungama? |
604 | GEN 24:12 | Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika. |
638 | GEN 24:46 | “Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo. |
691 | GEN 25:32 | Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?” |
746 | GEN 27:18 | Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.” Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?” |
755 | GEN 27:27 | Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati, “Haa, fungo la mwana wanga lili ngati fungo la munda umene Yehova waudalitsa. |
803 | GEN 29:7 | Iye anati, “Taonani, dzuwa likanalipo ndipo nthawi yosonkhanitsa nkhosa sinakwane. Bwanji osazimwetsa madzi nkhosazi.” |
846 | GEN 30:15 | Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.” Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.” |
858 | GEN 30:27 | Koma Labani anati kwa iye, “Chonde, ngati mungandikomere mtima musapite chifukwa ndadziwa kudzera mwa kuwombeza kwanga kuti Yehova wandidalitsa chifukwa cha inu.” |
865 | GEN 30:34 | Labani anati, “Ndavomera, zikhale monga mmene wayankhuliramu.” |
938 | GEN 32:10 | Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ |
958 | GEN 32:30 | Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.” Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo. |
1012 | GEN 34:31 | Koma iwo anayankha kuti, “Pepani, nanga achite kumusandutsa mlongo wathu ngati mkazi wachiwerewere?” |
1093 | GEN 37:9 | Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.” |
1097 | GEN 37:13 | ndipo Israeli anati kwa Yosefe, “Tsono, ndikufuna kukutuma kwa abale ako.” Iye anayankha nati, “Chabwino.” |
1105 | GEN 37:21 | Koma Rubeni atamva izi, anapulumutsa Yosefe. Iye anati kwa abale ake, “Ayi, tisamuphe, |
1137 | GEN 38:17 | Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.” Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?” |
1335 | GEN 44:10 | Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.” |
1358 | GEN 44:33 | “Tsono, chonde mulole kuti ine kapolo wanu nditsalire kuno kukhala kapolo wa mbuye wathu mʼmalo mwa mnyamatayu. Koma iye apite pamodzi ndi abale akewa. |
1367 | GEN 45:8 | “Motero, si inu amene munanditumiza kuno koma Mulungu. Iye anandisandutsa kukhala nduna yayikulu ya Farao, ndipo zonse za mʼnyumba mwake zili mʼmanja mwangamu. Komanso amene akulamulira dziko lonse la Igupto ndi ine. |
1389 | GEN 46:2 | Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!” Iye anayankha, “Ee, Ambuye.” |
1424 | GEN 47:3 | Farao anafunsa abale akewo kuti, “Mumagwira ntchito yanji?” Iwo anamuyankha kuti, “Ife, bwana ndife oweta ziweto, monga ankachitira makolo athu. |
1470 | GEN 48:18 | nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” |
1471 | GEN 48:19 | Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” |
1477 | GEN 49:3 | “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu. |
1482 | GEN 49:8 | “Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda; dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako; abale ako adzakugwadira iwe. |
1542 | EXO 1:9 | Iyo inati kwa anthu ake, “Taonani, Aisraeli achuluka ndipo ndi amphamvu kwambiri kuposa ife. |
1563 | EXO 2:8 | Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. |
1596 | EXO 3:16 | “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani. |
1627 | EXO 4:25 | Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.” |
1638 | EXO 5:5 | Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.” |
1650 | EXO 5:17 | Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ |
1731 | EXO 8:16 | Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze. |
2423 | EXO 31:2 | “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. |
2503 | EXO 34:6 | Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, |
2562 | EXO 35:30 | Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, |
3220 | LEV 16:18 | “Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe. |
4019 | NUM 10:30 | Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.” |
4024 | NUM 10:35 | Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu. |
4025 | NUM 10:36 | “Pamene likupumula, ankanena kuti, “Bwererani, Inu Yehova, ku chinamtindi cha Aisraeli.” |
4149 | NUM 14:40 | Mmamawa tsiku linalo anapita mbali ya ku dziko la mapiri. Iwo anati, “Tachimwa, tipita ku dziko limene Yehova anatilonjeza.” |
4259 | NUM 18:1 | Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. |
4279 | NUM 18:21 | “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. |
4328 | NUM 20:16 | koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.” “Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu. |
4381 | NUM 22:5 | anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati: “Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo. |
4405 | NUM 22:29 | Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.” |
4414 | NUM 22:38 | Balaamu anayankha Balaki kuti, “Taonani, ndabwera kwa inu lero, kodi ine ndili ndi mphamvu zoti nʼkuyankhula chilichonse? Inetu ndiyenera kuyankhula zokhazo zimene Mulungu wandiwuza.” |
4470 | NUM 24:23 | Ndipo ananenanso uthenga wina kuti, “Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi? |
4723 | NUM 32:3 | “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni, |
5012 | DEU 4:6 | Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.” |
5875 | JOS 2:4 | Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera. |
5895 | JOS 2:24 | Iwo anati kwa Yoswa, “Ndithu, Yehova wapereka dziko lonse mʼmanja mwathu. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha.” |
5961 | JOS 6:10 | Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!” |
5991 | JOS 7:13 | “Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’ |
6074 | JOS 10:8 | Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.” |
6598 | JDG 3:28 | Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. |
6610 | JDG 4:9 | Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. |
6705 | JDG 7:9 | Usiku umenewo Yehova anati kwa Gideoni, “Dzuka, pita kachite nkhondo ku misasayo, chifukwa ndayipereka mʼmanja mwako. |
6741 | JDG 8:20 | Tsono anawuza Yetero, mwana wake wachisamba kuti, “Tiye, ipha anthu amenewa!” Koma chifukwa Yeteri anali wamngʼono sanasolole lupanga lake, popeza anachita mantha. |
6744 | JDG 8:23 | Koma Gideoni anawawuza kuti, “Sindidzakulamulirani, mwana wanganso sadzakulamulirani. Koma Yehova ndiye adzakulamulirani.” |
6867 | JDG 11:36 | Mwanayo anayankha kuti, “Abambo, ngati munalonjeza kwa Yehova ndi pakamwa panu, chitani zimene munalonjezera pakuti Yehova wakuthandizani kulipsira adani anu Amowabu.” |
6944 | JDG 15:13 | Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja. |
7037 | JDG 19:11 | Akuyandikira ku Yebusi nʼkuti kutada ndithu. Tsono mtumiki uja anawuza mbuye wake kuti, “Tiyeni, tipatukire ku mzinda wa Ayebusiwa ndipo tigone.” |
7038 | JDG 19:12 | Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.” |
7049 | JDG 19:23 | Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. |
7059 | JDG 20:3 | Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.” |
7137 | RUT 1:8 | Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe. |
7144 | RUT 1:15 | Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.” |
7288 | 1SA 3:10 | Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.” |
7289 | 1SA 3:11 | Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve. |
7319 | 1SA 4:20 | Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako. |
7376 | 1SA 8:5 | Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.” |
7399 | 1SA 9:6 | Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.” |
7401 | 1SA 9:8 | Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” |
7403 | 1SA 9:10 | Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo. |
7435 | 1SA 10:15 | Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.” |
7467 | 1SA 12:5 | Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.” |
7482 | 1SA 12:20 | Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. |
7568 | 1SA 15:6 | Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki. |
7602 | 1SA 16:5 | Samueli anayankha kuti, “Inde, kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Mudzipatule ndipo mubwere kudzapereka nsembe pamodzi nane.” Kenaka iye anamupatula Yese ndi ana ake aamuna ndipo anawayitana kudzapereka nsembe. |
7608 | 1SA 16:11 | Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?” Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.” Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.” |
7614 | 1SA 16:17 | Choncho Sauli anati kwa atumiki ake, “Chabwino, kandipezereni munthu wodziwa bwino kuyimba ndipo mubwere naye kuno.” |
7657 | 1SA 17:37 | Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu.” Sauli anati kwa Davide, “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.” |
7675 | 1SA 17:55 | Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.” |
7770 | 1SA 20:38 | Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake. |
7772 | 1SA 20:40 | Pambuyo pake Yonatani anapereka zida zake za nkhondo kwa mnyamatayo ndipo anati, “Pita, nyamula ubwerere nazo ku mzinda.” |
7814 | 1SA 23:1 | Davide atawuzidwa kuti “Onani, Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila ndi kulanda zokolola zawo za mʼnkhokwe,” |
7815 | 1SA 23:2 | anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ndikamenyane nawo Afilistiwa?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, kamenyane nawo Afilisti ndi kupulumutsa mzinda wa Keila.” |
7830 | 1SA 23:17 | Iye anamuwuza kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Iwe udzakhala mfumu ya Israeli ndipo ine ndidzakhala wachiwiri wako. Ngakhale abambo anga Sauli akudziwa zimenezi.” |