Wildebeest analysis examples for:   nya-nya   Word,”    February 11, 2023 at 19:19    Script wb_pprint_html.py   by Ulf Hermjakob

9  GEN 1:9  Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
60  GEN 3:4  “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo.
395  GEN 16:13  Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.”
700  GEN 26:7  Anthu akumaloko atafunsa Isake za mkazi wake, iye anati, “Ndi mlongo wanga ameneyu.” Iye anaopa kunena kuti, “Ndi mkazi wanga ameneyu,” popeza ankaganiza kuti anthu akumeneku akhoza kumupha ndi kukwatira mkazi wake popeza Rebeka anali wokongola.
1169  GEN 39:19  Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri.
1454  GEN 48:2  Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.
1501  GEN 49:27  “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa; umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha, ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”
1628  EXO 4:26  Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe.
5262  DEU 12:20  Yehova Mulungu wanu akadzakulitsa dziko lanu monga anakulonjezerani, ndipo mukapukwa nyama mumanena kuti, “Ndikufuna nyama,” pamenepo mudzadya mmene mungafunire.
5276  DEU 13:3  chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe),
5330  DEU 15:9  Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa.
5337  DEU 15:16  Koma ngati kapoloyo akuwuzani kuti, “Ine sindikufuna kumasulidwa,” chifukwa choti wakukondani inuyo pamodzi ndi banja lanu ndiponso kuti kwamukomera iyeyo kuti azikhalabe nanu,
5380  DEU 17:14  Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,”
5486  DEU 22:14  namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, “Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake,”
5557  DEU 25:8  Pamenepo akuluakulu a mu mzinda wawowo adzamuyitanitsa nakamba naye. Ngati alimbikirabe kunena kuti, “Ine sindikufuna kumukwatira mkaziyu,”
6759  JDG 9:3  Abale a amayi akewo anamuyankhulira mawu amenewa kwa nzika zonse za ku Sekemu, ndipo mitima ya anthu onse inali pa Abimeleki chifukwa anati, “Uyu ndi mʼbale wathu,”
6876  JDG 12:5  Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi”
7194  RUT 4:2  Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi.
7258  1SA 2:16  Ngati munthuyo anena kuti, “Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira,” mtumikiyo amayankha kuti, “Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda.”
7320  1SA 4:21  Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake.
7377  1SA 8:6  Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova.
7568  1SA 15:6  Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.
7814  1SA 23:1  Davide atawuzidwa kuti “Onani, Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila ndi kulanda zokolola zawo za mʼnkhokwe,”
7943  1SA 27:10  Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.”
8522  2SA 19:9  Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye. Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo.
9214  1KI 13:27  Mneneri wokalambayo anati kwa ana ake, “Mundimangire chishalo pa bulu,” ndipo anaterodi.
9446  1KI 20:35  Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana.
9533  1KI 22:50  Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana.
9738  2KI 8:7  Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,”
10002  2KI 17:15  Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.
11675  2CH 23:14  Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,”
14083  PSA 12:6  “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”
15029  PSA 70:4  Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo.
15090  PSA 73:15  Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,” ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
15474  PSA 91:14  “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15515  PSA 94:18  Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
16201  PSA 129:1  “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;
16318  PSA 139:11  Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
16649  PRO 7:4  Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
16724  PRO 9:16  Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17049  PRO 20:25  Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,” popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
17121  PRO 23:7  paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.
17161  PRO 24:12  Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
17173  PRO 24:24  Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,” anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
17182  PRO 24:33  Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,” kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
17190  PRO 25:7  paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,” kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa. Chimene wachiona ndi maso ako,
17290  PRO 28:24  Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.
17522  ECC 7:23  Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati, “Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,” koma nzeruyo inanditalikira.
18020  ISA 14:22  Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni. Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo. Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,” akutero Yehova.
18021  ISA 14:23  “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu ndiponso dambo lamatope; ndidzawusesa ndi tsache lowononga,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
18056  ISA 17:3  Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israeli,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
18059  ISA 17:6  Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
18078  ISA 19:4  Ndidzawapereka Aigupto kwa olamulira ankhanza, ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,” akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
18136  ISA 22:14  Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
18274  ISA 29:11  Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
18275  ISA 29:12  Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
18456  ISA 37:34  Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera; sadzalowa mu mzinda umenewu,” akutero Yehova.
18535  ISA 41:14  Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
18587  ISA 43:12  Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa; ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu. Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
18706  ISA 48:22  “Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.
18771  ISA 52:5  Tsopano Ine Yehova ndikuti, “Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu, amene amawalamulira amawanyoza,” akutero Yehova. “Ndipo tsiku lonse, akungokhalira kuchita chipongwe dzina langa.
18794  ISA 54:1  “Sangalala, iwe mayi wosabala, iwe amene sunabalepo mwana; imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa,” akutero Yehova.
18799  ISA 54:6  Yehova wakuyitananso, uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima, mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,” akutero Mulungu wako.
18801  ISA 54:8  Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa ndili wokwiya kwambiri. Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya, ndidzakuchitira chifundo,” akutero Yehova Mpulumutsi wako.
18803  ISA 54:10  Ngakhale mapiri atagwedezeka ndi zitunda kusunthidwa, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Pangano langa lamtendere silidzasintha,” akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.
18810  ISA 54:17  palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke, ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa. Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova. Chipambano chawo chichokera kwa Ine,” akutero Yehova.
18818  ISA 55:8  “Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova.
18854  ISA 57:19  anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo. Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,” “Ndipo ndidzawachiritsa.” Akutero Yehova.
18856  ISA 57:21  “Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.
18890  ISA 59:20  “Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,” akutero Yehova.
18891  ISA 59:21  Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.
18973  ISA 65:7  ndi a makolo awo,” akutero Yehova. “Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo, Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata zimene anachita kale.”
18991  ISA 65:25  Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ngʼombe, koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala chinthu chopweteka kapena chowononga,” akutero Yehova.
19011  ISA 66:20  Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.
19012  ISA 66:21  Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
19014  ISA 66:23  “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova.
19023  JER 1:8  Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
19030  JER 1:15  Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova. “Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu polowera pa zipata za Yerusalemu; iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.
19034  JER 1:19  Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
19043  JER 2:9  “Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
19046  JER 2:12  Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi, ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,” akutero Yehova.
19056  JER 2:22  Ngakhale utasamba ndi soda kapena kusambira sopo wambiri, kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,” akutero Ambuye Yehova.
19063  JER 2:29  “Kodi mukundizengeranji mlandu? Nonse mwandiwukira,” akutero Yehova.
19072  JER 3:1  “Ngati munthu asudzula mkazi wake ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo? Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri? Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri. Komabe bwerera kwa ine,” akutero Yehova.
19081  JER 3:10  Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.
19085  JER 3:14  “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.
19087  JER 3:16  Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova.
19091  JER 3:20  Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake, momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,” akutero Yehova.
19097  JER 4:1  “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli, bwererani kwa Ine,” akutero Yehova. “Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga ndipo musasocherenso.
19105  JER 4:9  “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima, ansembe adzachita mantha kwambiri, ndipo aneneri adzathedwa nzeru,” akutero Yehova.
19142  JER 5:15  Inu Aisraeli,” Yehova akuti, “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali, ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo, mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa, zimene akunena inu simungazimvetse.
19145  JER 5:18  “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova.
19170  JER 6:12  Nyumba zawo adzazipereka kwa ena, pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo. Ndidzatambasula dzanja langa kukantha anthu okhala mʼdzikomo,” akutero Yehova.
19173  JER 6:15  Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo? Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe; sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,” akutero Yehova.
19239  JER 8:17  Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu, mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza, ndipo zidzakulumani,”
19250  JER 9:5  Iwe wakhalira mʼchinyengo ndipo ukukana kundidziwa Ine,” akutero Yehova.
19268  JER 9:23  koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi: kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa, kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo, chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi. Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,” akutero Yehova.
19269  JER 9:24  “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe.
19335  JER 12:17  Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.
19387  JER 15:3  “Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.