635 | GEN 24:43 | taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’ |
636 | GEN 24:44 | ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.” |
882 | GEN 31:8 | Pamene abambo anu anati, ‘Zamawangamawanga zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana amawangamawanga; ndipo pamene anati, ‘Zamichocholozi zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinaswa ana a michocholozi. |
1593 | EXO 3:13 | Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” |
1695 | EXO 7:9 | “Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.” |
2031 | EXO 19:4 | ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. |
2083 | EXO 21:5 | “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’ |
2486 | EXO 33:12 | Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ |
3813 | NUM 5:20 | Koma ngati wayenda njira yoyipa uli pa ukwati ndi mwamuna wako ndi kudzidetsa pogonana ndi mwamuna amene si mwamuna wako,’ |
4137 | NUM 14:28 | Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena: |
6669 | JDG 6:13 | Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.” |
6700 | JDG 7:4 | Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.” |
6848 | JDG 11:17 | Kenaka Israeli anatumiza amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu,’ Koma mfumu ya ku Edomu sinamvere zimenezo. Aisraeli anatumizanso amithenga kwa mfumu ya ku Mowabu, ndipo iyo inakananso. Choncho Israeli anakhala ku Kadesi. |
7474 | 1SA 12:12 | “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. |
7519 | 1SA 14:9 | Akatiwuza kuti, ‘Imani pomwepo mpaka tikupezeni,’ ife tikangoyima pomwepo osapita kumene kuli iwoko. |
7520 | 1SA 14:10 | Koma akadzati, ‘Bwerani kuno,’ ndiye ife tikapitedi, chifukwa ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova wapereka mʼmanja mwathu.” |
7739 | 1SA 20:7 | Akanena kuti, ‘Wachita bwino,’ ndiye kuti zinthu zindiyendera bwino ine mtumiki wako. Koma ngati akapsa mtima, ndiye udziwe kuti iwo atsimikiza zondichita zoyipa. |
7753 | 1SA 20:21 | Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse. |
7754 | 1SA 20:22 | Koma ndikadzati, ‘Taona mivi ili patsogolo pako,’ iwe udzachoke chifukwa Yehova ndiye walola kuti uchokepo. |
8143 | 2SA 5:8 | Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.” |
8348 | 2SA 13:28 | Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” |
8418 | 2SA 15:26 | Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.” |
8439 | 2SA 16:10 | Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ” |
8575 | 2SA 20:18 | Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. |
8842 | 1KI 3:23 | Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ” |
9017 | 1KI 8:29 | Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usiku ndi usana, malo ano amene Inu munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo,’ choncho imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera akuyangʼana malo ano. |
9035 | 1KI 8:47 | ndipo ngati asintha maganizo ali ku dziko la ukapololo ndi kulapa ndi kukudandaulirani mʼdziko la owagonjetsa ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa, tachita zinthu zoyipa,’ |
9164 | 1KI 12:10 | Anyamata anzake amene anakula nawo limodzi aja anamuyankha kuti, “Anthu amene ananena kwa iwe kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa, koma inu peputsani goli lathu,’ uwawuze kuti ‘Chala changa chakanise nʼchachikulu kupambana chiwuno cha abambo anga. |
9707 | 2KI 6:29 | Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.” |
9715 | 2KI 7:4 | Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.” |
9741 | 2KI 8:10 | Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.” |
11410 | 2CH 10:10 | Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga. |
11891 | 2CH 32:11 | Pamene Hezekiya akunena kuti ‘Yehova Mulungu wathu adzatipulumutsa kuchoka mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya,’ iye akukusocheretsani, kuti mufe ndi njala ndi ludzu. |
12533 | NEH 9:18 | Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa. |
13082 | JOB 9:27 | Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga, ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’ |
13278 | JOB 17:14 | ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’ |
13455 | JOB 24:15 | Munthu wachigololo amadikira chisisira; iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’ ndipo amaphimba nkhope yake. |
13616 | JOB 31:24 | “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’ |
13678 | JOB 33:24 | kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’ |
13705 | JOB 34:18 | Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’ |
13779 | JOB 37:6 | Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’ ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’ |
15395 | PSA 89:5 | ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya. Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ” Sela. |
18297 | ISA 30:10 | Iwo amawuza alosi kuti, ‘Musationerenso masomphenya!’ Ndipo amanena kwa mneneri kuti, ‘Musatinenerenso zoona,’ mutiwuze zotikomera, munenere za mʼmutu mwanu. |
18407 | ISA 36:7 | Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’ |
18567 | ISA 42:17 | Koma onse amene amadalira mafano amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ ndidzawachititsa manyazi kotheratu. |
18631 | ISA 44:28 | Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna; iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ” |
18974 | ISA 65:8 | Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo, popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’ Inenso chifukwa cha mtumiki wanga; sindidzawononga onse. |
19037 | JER 2:3 | Israeli anali wopatulika wa Yehova, anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola; onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa ndipo mavuto anawagwera,’ ” akutero Yehova. |
19061 | JER 2:27 | Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’ |
19083 | JER 3:12 | Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti, “ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale, pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale. |
19084 | JER 3:13 | Ungovomera kulakwa kwako kuti unawukira Yehova Mulungu wako. Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndiponso kuti sunandimvere,’ ” akutero Yehova. |
19106 | JER 4:10 | Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.” |
19113 | JER 4:17 | Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda, chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ” akutero Yehova. |
19129 | JER 5:2 | Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ komabe akungolumbira mwachinyengo.” |
19172 | JER 6:14 | Amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba pokha. Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere. |
19233 | JER 8:11 | Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba chabe nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere. |
19300 | JER 11:5 | Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.” Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.” |
19316 | JER 11:21 | “Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’ |
19334 | JER 12:16 | Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga. |
19346 | JER 13:11 | Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova. |
19416 | JER 16:11 | Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. |
19419 | JER 16:14 | Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ |
19560 | JER 23:7 | Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ |
19587 | JER 23:34 | Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. |
19589 | JER 23:36 | Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. |
19591 | JER 23:38 | Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, |
19601 | JER 24:8 | “ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto. |
19634 | JER 25:31 | Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi, chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse; adzaweruza mtundu wonse wa anthu ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ” akutero Yehova. |
19679 | JER 27:14 | Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. |
19687 | JER 27:22 | ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ” |
19691 | JER 28:4 | Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ” |
19736 | JER 29:32 | Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova. |
19739 | JER 30:3 | Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.” |
19746 | JER 30:10 | “ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo; usade nkhawa, iwe Israeli,’ akutero Yehova. ‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali, zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo. Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere, ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha. |
19747 | JER 30:11 | Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu kumene ndinakubalalitsirani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa. Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ” |
19794 | JER 31:34 | Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake, kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’ chifukwa onse adzandidziwa Ine, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,” akutero Yehova. “Ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.” |
19854 | JER 33:10 | “Yehova akuti, ‘Inu mumanena za malo ano kuti ndi bwinja,’ malo opandamo anthu kapena nyama. Komatu mizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu mʼmene tsopano muli zii mudzamvekanso |
19857 | JER 33:13 | Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova. |
19858 | JER 33:14 | “ ‘Taonani masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzachitadi zokoma zimene ndinalonjeza Aisraeli ndi nyumba ya Yuda. |
19989 | JER 38:25 | Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ |
20582 | EZK 3:11 | Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.” |
20589 | EZK 3:18 | Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. |
20783 | EZK 13:6 | Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi. |
20784 | EZK 13:7 | Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe. |
20817 | EZK 14:17 | “Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. |
20837 | EZK 16:6 | “ ‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’ |
21073 | EZK 22:28 | Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule. |
21235 | EZK 28:9 | Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’ pamaso pa iwo amene akukupha? Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu, mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo. |
21261 | EZK 29:9 | Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ |
21279 | EZK 30:6 | “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: “ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu. Adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ” ndikutero Ine Ambuye Yehova. |
21357 | EZK 33:8 | Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. |
21363 | EZK 33:14 | Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, |
21441 | EZK 36:13 | “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’ |
21537 | EZK 39:20 | Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova. |
22173 | HOS 2:1 | “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ |
22175 | HOS 2:3 | “Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ” |
22197 | HOS 2:25 | Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ” |
22564 | AMO 8:14 | Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya, kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’ kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’ Iwowo adzagwa ndipo sadzadzukanso.” |
22928 | HAG 2:4 | Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. |
22931 | HAG 2:7 | Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. |