634 | GEN 24:42 | “Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu, |
885 | GEN 31:11 | Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, ‘Yakobo.’ Ine ndinayankha, ‘Ee, Ambuye.’ |
1421 | GEN 46:34 | Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.” |
1595 | EXO 3:15 | Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli. |
1596 | EXO 3:16 | “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani. |
1598 | EXO 3:18 | “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’ |
1702 | EXO 7:16 | Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. |
3815 | NUM 5:22 | Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ” “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ” |
4043 | NUM 11:18 | “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. |
4387 | NUM 22:11 | ‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ” |
4424 | NUM 23:7 | Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’ |
5864 | JOS 1:11 | “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ” |
7126 | JDG 21:22 | Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ” |
7439 | 1SA 10:19 | Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.” |
7474 | 1SA 12:12 | “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. |
7700 | 1SA 18:22 | Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” |
7753 | 1SA 20:21 | Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse. |
9142 | 1KI 11:31 | Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. |
9475 | 1KI 21:21 | Iye akuti ‘Taonani, ine ndidzabweretsa mavuto pa iwe. Ndidzawononga kotheratu zidzukulu zako ndi kuchotsa mu Israeli munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu. |
10058 | 2KI 18:30 | Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’ |
10135 | 2KI 21:12 | Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru. |
12023 | EZR 1:2 | Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. |
13536 | JOB 28:28 | Ndipo Iye anati kwa munthu, ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ” |
17856 | ISA 7:4 | Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. |
18415 | ISA 36:15 | Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’ |
18465 | ISA 38:5 | “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako. |
18548 | ISA 41:27 | Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’ Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu. |
19172 | JER 6:14 | Amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba pokha. Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere. |
19233 | JER 8:11 | Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba chabe nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere. |
19513 | JER 21:4 | ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. |
19875 | JER 34:5 | udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.” |
20058 | JER 42:14 | ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’ |
20131 | JER 46:17 | Kumeneku iwo adzafuwula kuti, ‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti, Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’ |
20148 | JER 47:6 | “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova, kodi udzapumula liti? Bwerera mʼmalo ako; ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’ |
20151 | JER 48:2 | Palibenso amene akutamanda Mowabu; ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa: ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’ Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete; ankhondo adzakupirikitsani. |
20875 | EZK 16:44 | “ ‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’ |
20884 | EZK 16:53 | “ ‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu. |
21016 | EZK 21:8 | Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. |
21041 | EZK 21:33 | “Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti, “ ‘Lupanga, lupanga, alisolola kuti liphe anthu, alipukuta kuti liwononge ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi. |
21275 | EZK 30:2 | “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. “ ‘Ufuwule mawu awa akuti, ‘Kalanga, tsiku lafika!’ |
22007 | DAN 7:5 | “Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’ |
22896 | ZEP 3:7 | Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita. |
22947 | HAG 2:23 | “ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.” |
23028 | ZEC 6:12 | Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova. |
23406 | MAT 7:21 | “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. |
23407 | MAT 7:22 | Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ |
23454 | MAT 9:6 | Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ” |
23635 | MAT 13:27 | “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’ |
23874 | MAT 20:13 | “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? |
23916 | MAT 21:21 | Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. |
24049 | MAT 24:23 | Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. |
24089 | MAT 25:12 | “Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’ |
24117 | MAT 25:40 | “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’ |
24122 | MAT 25:45 | “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’ |
24338 | MRK 2:9 | Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ |
24676 | MRK 10:19 | Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ” |
24732 | MRK 11:23 | Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. |
24807 | MRK 13:21 | Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. |
25200 | LUK 5:24 | Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ” |
25261 | LUK 6:46 | “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? |
25476 | LUK 11:2 | Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere. |
25479 | LUK 11:5 | Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, |
25595 | LUK 13:8 | “Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa. |
25612 | LUK 13:25 | Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’ |
25632 | LUK 14:10 | Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. |
25639 | LUK 14:17 | Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ |
25644 | LUK 14:22 | “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’ |
25669 | LUK 15:12 | Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo. |
25678 | LUK 15:21 | “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’ |
25719 | LUK 16:30 | “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’ |
25768 | LUK 18:11 | Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. |
25770 | LUK 18:13 | “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’ |
25818 | LUK 19:18 | “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’ |
25820 | LUK 19:20 | “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. |
27359 | ACT 10:31 | Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. |
27383 | ACT 11:7 | Kenaka ine ndinamva mawu akuti, ‘Petro, Imirira. Ipha, nudye.’ |
27384 | ACT 11:8 | “Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’ |
27465 | ACT 13:34 | Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa: “ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’ |
27472 | ACT 13:41 | “ ‘Onani, inu anthu onyoza, dabwani ndipo wonongekani, chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu, inu simudzazikhulupirira ngakhale wina atakufotokozerani!’ ” |
27905 | ACT 26:14 | Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ” |